Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mukhoza Kudzakhala Padzikoli Kwamuyaya

Mukhoza Kudzakhala Padzikoli Kwamuyaya

LIMENELITU NDI LONJEZO LOSANGALATSA! Mlengi wathu watilonjeza kuti adzatipatsa moyo wosatha padziko lapansi pompano. Komabe anthu ambiri amaona kuti mfundo imeneyi ndi yovuta kumvetsa. Iwo amati, ‘Munthu aliyense ayenera kufa, ndipo umu ndi mmene moyo umakhalira.’ Ena amati n’zoona kuti anthu adzakhaladi kwamuyaya, koma osati padzikoli. Amanena kuti munthu angapeze moyo wosatha pokhapokha amwalire kaye, n’kupita kumwamba. Kodi inuyo mukuganiza bwanji?

Musanayankhe funsoli, bwanji tikambirane kaye mayankho a m’Baibulo a mafunso atatu awa: Tikaganizira mmene tinalengedwera, kodi timadziwa bwanji kutalika kwa nthawi imene tinafunika kukhala ndi moyo? Kodi cholinga choyambirira cha Mulungu polenga anthu ndi dzikoli chinali chotani? Kodi chinachitika n’chiyani kuti anthu azifa?

MUNTHU ANALENGEDWA MWAPADERA KWAMBIRI

Pa zinthu zonse zamoyo zimene Mulungu analenga padzikoli, anthu ndi amene analengedwa mwapadera kwambiri. N’chifukwa chiyani tikutero? Baibulo limasonyeza kuti anthu analengedwa “m’chifaniziro” cha Mulungu. (Genesis 1:26, 27) Kodi zimenezi zikutanthauza chiyani? Zikutanthauza kuti anthu analengedwa ndi makhalidwe amene Mulungu ali nawo monga ngati chikondi komanso chilungamo.

Kuwonjezera apo, anthufe tinalengedwa ndi nzeru zomwe zimatithandiza kuganiza. Tinalengedwanso kuti tizitha kusiyanitsa chabwino ndi choipa, tizigoma ndi kukula komanso kukongola kwa zinthu za m’chilengedwe, ndiponso kuti tizifuna kukhala pa ubwenzi ndi Mulungu. Timathanso kumasangalala ndi luso la zojambulajambula, nyimbo ndiponso ndakatulo. Koposa zonse, anthufe tinalengedwa ndi mtima wofuna kulambira Mulungu. Zinthu zimenezi ndi zimene zimasiyanitsa anthu ndi zamoyo zina zonse zimene zili padzikoli.

Mungachite bwino kudzifunsa kuti: ‘Zikanakhala kuti tikufunika tizikhala ndi moyo tizaka towerengeka tokha, kodi Mulungu akanatipatsa nzeru zoti tizitha kukulitsa luso lathu? Kodi akanatilenga ndi makhalidwe apadera omwe tili nawowa? Zoona n’zakuti Mulungu analenga anthu ndi luso komanso makhalidwe amenewa n’cholinga choti akhale ndi moyo padzikoli kwamuyaya.

CHOLINGA CHOYAMBIRIRA CHA MULUNGU

Anthu ena amanena kuti Mulungu sanatilenge kuti tizikhala padzikoli kwamuyaya. Iwo amati dzikoli ndi malo omwe Mulungu amangoyeserapo anthu kuti aone ngati ali oyenera kupita kumwamba kuti akakhale naye kwamuyaya. Ngati izi zili zoona, kodi sizikanakhala zomveka kunena kuti Mulungu ndi amene amachititsa zoipa zonse padzikoli? Zimenezi n’zosiyana kotheratu ndi makhalidwe a Mulungu. Baibulo limati: “Njira zake zonse ndi zolungama. Mulungu wokhulupirika, amene sachita chosalungama. Iye ndi wolungama ndi wowongoka.”​—Deuteronomo 32:4.

Baibulo limafotokoza momveka bwino za cholinga cha Mulungu pamene ankalenga dziko lapansi kuti: “Kunena za kumwamba, kumwamba ndi kwa Yehova, koma dziko lapansi analipereka kwa ana a anthu.” (Salimo 115:16) Mulungu analenga dzikoli kuti likhale lokongola n’cholinga choti pazikhala anthu. Analenganso zinthu zambirimbiri kuti anthu azisangalala ndi moyo kwamuyaya.​—Genesis 2:8, 9.

“Kunena za kumwamba, kumwamba ndi kwa Yehova, koma dziko lapansi analipereka kwa ana a anthu.”​—Salimo 115:16

Baibulo limanenanso momveka bwino za cholinga cha Mulungu polenga anthu. Iye anauza anthu oyambirira kuti ‘achuluke, adzaze dziko lapansi, ndipo ayang’anire . . . cholengedwa chilichonse chokwawa padziko lapansi.’ (Genesis 1:28) Anthuwo anali ndi mwayi waukulu wosamalira komanso kukulitsa Paradaiso. Choncho Adamu ndi Hava komanso ana amene akanabereka ankayenera kukhala padzikoli mpaka kalekale osati kumwamba.

N’CHIFUKWA CHIYANI TIMAFA?

Ndiyeno ngati tinalengedwa kuti tizikhala kwamuyaya, n’chifukwa chiyani timafa? Baibulo limasonyeza kuti mwana mmodzi wa Mulungu yemwe kenako anayamba kudziwika kuti Satana Mdyerekezi, ankafuna kusokoneza cholinga cha Mulungu mu Edeni. Kodi anachita bwanji zimenezi?

Satana anapusitsa makolo athu oyambirira, Adamu ndi Hava kuti asamvere Mulungu. Satana ananena kuti Mulungu amawamana zinazake zabwino. Tingati anati Mulungu anawamana ufulu wosankha okha pakati pa chabwino ndi choipa. Adamu ndi Hava anasankha kumvera Satana. Zotsatira zake zinali zakuti n’kupita kwa nthawi, iwo anafa monga mmene Mulungu anawachenjezera. Anatayanso mwayi wokhala kwamuyaya m’Paradaiso padziko lapansi.​—Genesis 2:17; 3:1-6; 5:5.

Zotsatira za zimene Adamu ndi Hava anachita, zimakhudza tonsefe mpaka pano. Mawu a Mulungu amati: ‘Uchimo unalowa m’dziko kudzera mwa munthu mmodzi [Adamu], ndi imfa kudzera mwa uchimo, imfayo n’kufalikira kwa anthu onse.’ (Aroma 5:12) Timafa chifukwa choti tinatengera uchimo kuchokera kwa makolo athu oyambirira osati chifukwa chakuti ndi cholinga cha Mulungu.

MUKHOZA KUDZAKHALA PADZIKOLI KWAMUYAYA

Kusamvera kwa Adamu ndi Hava sikunasokoneze cholinga cha Mulungu polenga anthu ndi dziko. Popeza Mulungu ndi wachikondi komanso chilungamo, anakonza njira yotimasulira kuukapolo wa uchimo ndi imfa zimene tinatengera kuchokera kwa makolo athu. Mtumwi Paulo anati: “Malipiro a uchimo ndi imfa, koma mphatso imene Mulungu amapereka ndi moyo wosatha kudzera mwa Khristu Yesu Ambuye wathu.” (Aroma 6:23) Mwachikondi, Mulungu “anapereka Mwana wake wobadwa yekha [Yesu Khristu], kuti aliyense wokhulupirira iye asawonongeke, koma akhale ndi moyo wosatha.” (Yohane 3:16) Pamene Yesu anadzipereka mofunitsitsa monga nsembe, anawombola zonse zimene Adamu anataya. *

Posachedwapa lonjezo la Mulungu loti dzikoli lidzakhala paradaiso likwaniritsidwa. Nanunso mukhoza kudzakhala nawo m’dziko limeneli ngati mutamvera mawu a Yesu akuti: “Lowani pachipata chopapatiza. Pakuti msewu waukulu ndi wotakasuka ukupita kuchiwonongeko, ndipo anthu ambiri akuyenda mmenemo. Koma chipata cholowera ku moyo n’chopapatiza komanso msewu wake ndi wopanikiza, ndipo amene akuupeza ndi owerengeka.” (Mateyu 7:13, 14) Choncho tsogolo lanu pa nkhaniyi likudalira zimene mungasankhe. Ndiye kodi musankha kuchita chiyani?

^ ndime 17 Kuti mumve zambiri zokhudza mmene dipo la Yesu lingakuthandizireni, onani mutu 5 m’buku lakuti Zimene Baibulo Limaphunzitsa. Bukuli ndi lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova ndipo limapezeka pawebusaiti yathu ya jw.org/ny.