Kodi Pali Amene Angadziwiretu Zam’tsogolo?
Kodi munayamba mwadzifunsapo kuti tsogolo lanu komanso la banja lanu lidzakhala lotani? Kodi mumaona kuti zinthu zidzayenda bwino kapena mudzakumana ndi mavuto? Kodi mukhala ndi moyo wautali kapena waufupi? Anthu akhala akudzifunsa mafunso amenewa kwa zaka zambiri.
Masiku ano akatswiri amafufuza zochitika za padziko lonse n’kumaneneratu zimene zidzachitike m’tsogolo. Ngakhale kuti zina mwa zimene amanena zimachitika, zambiri sizichitika n’komwe. Mwachitsanzo mu 1912, Guglielmo Marconi yemwe anapanga telegalafu yotumiza uthenga kudzera mumphepo ananena kuti: “Kubwera kwa njira zotumizira mauthenga kudzathandiza kuti nkhondo zithe.” Munthu wina wogwira ntchito kukampani yopanga malekodi yotchedwa Decca, yemwe mu 1962 anakana kuthandiza gulu loimba la Beatles, ankakhulupirira kuti magulu oyimba pogwiritsa ntchito gitala sapita patali.
Anthu ambiri amapita kwa anthu amatsenga kuti akawathandize kudziwa zam’tsogolo. Ena amafunsira nzeru kwa okhulupirira nyenyezi ndipo nkhani zokhudza kukhulupirira nyenyezi zimapezeka m’magazini komanso m’manyuzipepala ambiri. Enanso amapita kukaombeza kwa asing’anga kapena anthu amene amanena kuti amatha kudziwa zam’tsogolo pogwiritsa ntchito makadi olosera, manambala kapena mizera ya m’manja mwa munthu.
Kale, anthu ena akafuna kudziwa zam’tsogolo ankakafunsira kwa ansembe aamuna kapena aakazi omwe ankati amanena zinthu zochokera kwa milungu yawo. Mwachitsanzo, ena amati Mfumu Kolosase ya ku Lidiya inatumiza mphatso zamtengo wapatali kwa wansembe wina wa ku Delphi ku Girisi, kuti amuuze zimene zingachitike ngati angakamenyane ndi gulu la nkhondo la Koresi wa ku Perisiya. Wansembeyo anena kuti “ufumu wamphamvu” udzagonjetsedwa ngati Kolosase angapite kukalimbana ndi Koresi. Ndi chidaliro chonse kuti akapambana, Kolosase anapitadi kukamenya nkhondoyo koma ufumu wamphamvu umene unagonjetsedwa unali wake.
Zimene wansembeyu ananena zinali zopusitsa chifukwa zinkaoneka kuti zimene analoserazo zingakhale zoona posatengera kuti wapambana pankhondoyo ndi ndani. Kolosase anakumana ndi mavuto chifukwa anauzidwa zabodza. Kodi anthu amene amagwiritsa ntchito njira zotchuka zodziwira zam’tsogolo, zinthu zimawayendera bwanji?