Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

NSANJA YA OLONDA Na. 1 2022 | Kodi N’zotheka Kuthetsa Chidani?

Anthu ambiri padzikoli amadana ndipo amachita zinthu zankhanza zambirimbiri. Mwachitsanzo, amasala ena, kuwachitira nkhanza, kuwalankhula mawu achipongwe kapenanso kuwavulaza. Kodi chidani chidzatha? Nkhani zomwe zili m’magaziniyi zitithandiza kuona mmene Baibulo lingatithandizire kuthetsa chidani. Tionanso zomwe Mulungu analonjeza zoti adzathetseratu chidani.

 

N’zotheka Kuthetsa Chidani

Kodi ndi zinthu ziti zomwe zimachititsa kuti chidani chisamathe? Nanga anthu amachita bwanji zimenezi?

N’chifukwa Chiyani Chidani Sichikutha?

Baibulo limatiuza mmene chidani chinayambira, chifukwa chake anthu amayamba kudana ndi anzawo, komanso chifukwa chake anthu amadana kwambiri masiku ano.

Kodi Tingathetse Bwanji Chidani?

Zimene Baibulo limaphunzitsa zathandiza anthu ambiri kusiya kudana ndi anthu ena.

KODI TINGATHETSE BWANJI CHIDANI?

1 | Muziyesetsa Kupewa Tsankho

Chotsani kamtima koipidwa ndi anthu ena, potengera chitsanzo cha Yehova yemwe ndi wopanda tsankho.

KODI TINGATHETSE BWANJI CHIDANI?

2 | Musamabwezere

Mukamakhulupirira kuti posachedwapa Mulungu adzathetsa zoipa zonse, sizingakuvuteni kuthetsa mtima wofuna kubwezera.

KODI TINGATHETSE BWANJI CHIDANI?

3 | Yesetsani Kuchotsa Mtima Wachidani M’maganizo Mwanu

Mawu a Mulungu angatithandize kuthetsa chidani m’maganizo komanso mumtima mwathu.

KODI TINGATHETSE BWANJI CHIDANI?

4 | Mulungu Angakuthandizeni Kuthetsa Mtima Wachidani

Mzimu woyera wa Mulungu ungakuthandizeni kukhala ndi makhalidwe amene angakuthandizeni kuthetsa chidani.

Kodi Zinthu Zidzakhala Bwanji Chidani Chikadzatheratu?

Kodi ndi ndani amene adzathetseretu vuto la chidani?

Anthu Akuvutika Ndi Chidani Padziko Lonse

N’chiyani chingathandize kuti chidani chisapitirire? Anthu padziko lonse ayamba kale kuchita zinthu zothandiza kuti chidani chitheretu.