Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

NSANJA YA OLONDA Na. 1 2021 | Kodi Kupemphera N’kothandizadi?

Kodi munayamba mwaganizapo kuti Mulungu samva mapemphero anu? Ngati zili choncho, dziwani kuti si inu nokha. Anthu ambiri anapemphapo Mulungu kuti awathandize koma mavuto awo sanathe. Nkhani zotsatirazi ziyankha mafunso awa: Kodi n’chifukwa chiyani sitiyenera kukayikira kuti Mulungu amamva mapemphero athu? N’chifukwa chiyani mapemphero ena sayankhidwa? Nanga kodi tiyenera kuchita chiyani kuti mapemphero athu aziyankhidwa?

 

Zimene Anthu Amanena Zokhudza Kupemphera

Kodi pemphero ndi mphatso yapadera yochokera kwa Mulungu kapena ndi mwambo wopanda tanthauzo basi?

Kodi Mulungu Amamva Mapemphero Athu?

Baibulo limatitsimikizira kuti Mulungu amamvetsera mapemphero athu tikamapemphera m’njira yovomerezeka.

N’chifukwa Chiyani Mulungu Sayankha Mapemphero Ena?

Baibulo limafotokoza mapemphero amene Mulungu amayankha komanso amene sayankha.

Kodi Mungatani Kuti Mulungu Azimvetsera Mapemphero Anu?

Tikhoza kulankhula ndi Mulungu kulikonse, nthawi iliyonse, mokweza kapenanso chamumtima. Ndipotu Yesu anatithandiza kudziwa zomwe tinganene popemphera.

Kodi Kupemphera Kungakuthandizeni Bwanji?

Kodi pemphero lingakuthandizeni bwanji kuti muthane ndi mavuto?

Kodi Mulungu Amamva Mapemphero Anu?

Baibulo limanena kuti mukapemphera kwa Mulungu, iye amamva ndipo amafunitsitsa kukuthandizani.