Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

2 Lingakuthandizeni Kuthetsa Mavuto

2 Lingakuthandizeni Kuthetsa Mavuto

Mavuto ena amene timakumana nawo satherapo ndipo nthawi zina vutolo limakula tisanalitulukire n’komwe. Kodi m’Baibulo muli malangizo amene angatithandize kuthetsa mavuto oterewa? Taganizirani zitsanzo zotsatirazi.

KUDA NKHAWA KWAMBIRI

Mtsikana wina dzina lake Rosie anati: “Nthawi zambiri ndinkakhala ndi nkhawa kwambiri chifukwa chomangoganizira mavuto anga ndipo mavuto ena ndinkawatenga ngati aakulu kwambiri kuposa mmene analili.” Kodi Baibulo linamuthandiza bwanji? Pali malemba ambiri amene anamuthandiza. Limodzi mwa malembawa ndi Mateyu 6:34, limene limati: “Musamade nkhawa za tsiku lotsatira, chifukwa tsiku lotsatira lidzakhala ndi zodetsa nkhawa zakenso. Zoipa za tsiku lililonse n’zokwanira pa tsikulo.” Panopa Rosie amanena kuti mawu a Yesuwa anamuthandiza kuti asiye kumadera nkhawa zamawa. Iye anati: “Ndinali kale ndi mavuto okwanira moti panalibe chifukwa chomadera nkhawa za zinthu zimene sizinachitike, zomwe mwinanso sizingachitike n’komwe.”

Nayenso Yasmine anali ndi vuto lomangokhalira kuda nkhawa. Iye anati: “Masiku ambiri ndinkalira ndipo nthawi zina usiku sindinkagona. Ndinkaona kuti zinthu sizinkandiyendera pa moyo wanga chifukwa ndinkangodera nkhawa zinthu zambirimbiri.” Kodi ndi lemba liti limene linamuthandiza? Iye anawerenga lemba la 1 Petulo 5:7, lomwe limati: ‘Muzimutulira Mulungu nkhawa zanu zonse, pakuti amakuderani nkhawa.’ Yasmine anati: “Ndinayamba kupemphera kwa Yehova pafupipafupi ndipo anayankha mapemphero anga. Ndinamva ngati ndatula chimtolo cholemera. Nthawi zina ndimakhalabe ndi nkhawa koma panopa ndimadziwa zoyenera kuchita.”

 KUCHITA ZINTHU MOZENGEREZA

Mtsikana wina dzina lake Isabella anati: “Ndimaona kuti vuto langa lozengereza ndikafuna kuchita zinthu ndi lakumtundu chifukwa bambo anganso ali ndi vuto lomweli. Ndimapezeka kuti ndangokhala kapena ndikuonera TV koma ndili ndi zinthu zina zofunika zoti ndichite. Khalidwe limeneli si labwino chifukwa limachititsa kuti kenako udzachite zinthuzo mopanikizika kapena mongoti bola zindichoke.” Mfundo ya m’Baibulo imene inamuthandiza ndi ya pa 2 Timoteyo 2:15. Lembali limati: “Chita chilichonse chotheka kuti usonyeze kuti ndiwe wovomerezeka pamaso pa Mulungu, wantchito wopanda chifukwa chochitira manyazi ndi ntchito imene wagwira.” Isabella anati: “Sindinkafuna kuti Yehova azichita manyazi ndi zochita zanga chifukwa choti ndimachita zinthu mozengereza.” Panopa Isabella anasiya kuzengereza akafuna kuchita zinthu.

Mtsikana wina dzina lake Kelsey analinso ndi vuto lomweli. Iye anati: “Ndikakhala ndi zoti ndichite, ndinkangozengereza mpaka nthawi kutha. Sizinali zabwino chifukwa kenako ndinkakhala ndi nkhawa, kulephera kugona komanso ndinkalira.” Lemba limene linamuthandiza ndi la Miyambo 13:16, limene limati: “Aliyense wochenjera amachita zinthu mozindikira, koma wopusa amafalitsa uchitsiru.” Iye anafotokoza mmene kuganizira mfundo ya palembali kunamuthandizira ndipo anati: “Ndi bwino kumachita zinthu mwanzeru komanso kumakonzekereratu. Panopa ndili ndi kabuku kamene ndimalembamo zinthu zimene ndikufuna kuchita. Zimenezi zimandithandiza kuti ndizichita zinthu pa nthawi yoyenera, m’malo modikira mpaka nthawi itatha.”

KUSOWA WOCHEZA NAYE

Mayi wina dzina lake Kirsten anati: “Mwamuna wanga anangochoka, n’kundisiyira ana 4.” Kodi ndi mfundo ya m’Baibulo iti yomwe inamuthandiza? Ndi mfundo ya palemba la Miyambo 17:17, limene limati: “Bwenzi lenileni limakukonda nthawi zonse, ndipo bwenzilo ndi m’bale amene anabadwira kuti akuthandize pakagwa mavuto.” Mayiyu anafotokozera anzake a kumpingo za vuto lakeli ndipo anamuthandiza kwambiri. Iye anati: “Anzangawa ankandithandiza kwambiri. Ena ankandipatsa zinthu zosiyanasiyana. Kangapo konse anzanga ena anatithandiza pamene tinkasamuka. Mnzanga wina anandithandiza kuti ndipeze ntchito. Pakakhala vuto lililonse, anzangawa ankandithandiza.”

Delphine amene tamutchula kale uja analinso ndi vuto losowa wocheza naye. Iye anati: “Ndinkaona kuti aliyense ali ndi wocheza naye koma ine ndili ndekhandekha.” Lemba limene linamuthandiza ndi la Salimo 68:6, limene limati: “Mulungu akuchititsa osungulumwa kukhala m’nyumba.” Delphine anati: “Ndinazindikira kuti sikuti vesili likungonena za nyumba yeniyeni koma likutanthauzanso kuti Mulungu amatipatsa nyumba yauzimu yomwe ndi chitetezo chimene timapeza tikhala ndi anthu amene amakonda Yehova. Koma ndinazindikiranso kuti n’zosatheka kuti ndizigwirizana kwambiri ndi anthu amenewa popanda kugwirizana kaye ndi Yehova. Lemba lomwe linandithandiza ndi la Salimo 37:4, lomwe limati: ‘Sangalala mwa Yehova, ndipo adzakupatsa zokhumba za mtima wako.’”

Delphine ananenanso kuti: “Ndinazindikira kuti ndikufunika kulimbitsa kwambiri ubwenzi wanga ndi Yehova chifukwa sindingapeze mnzanga wabwino kuposa Yehova. Kenako ndinakonza zoti ndizipeza nthawi yochita zinthu ndi anthu amene amakonda Yehova, n’cholinga choti akhale anzanga. Ndinaphunziranso kuti ndisamaganizire kwambiri zimene anthu ena amalakwitsa. Ndizingochita nawo zinthu ngati sindikuona zimene amalakwitsazo.”

N’zoona kuti anthu amene amatumikira Yehova si angwiro. A Mboni za Yehova amakumana ndi mavuto ngati anthu ena onse. Koma mfundo zimene amaphunzira m’Baibulo zimawapangitsa kuti aziyesetsa kuthandiza anthu ena. Ndi nzeru kucheza ndi anthu ngati amenewa. Komabe, kodi mfundo za m’Baibulo zingatithandizenso pa mavuto amene sangathe panopa, monga matenda okhalitsa ndiponso imfa ya wachibale kapena mnzathu?

Kutsatira mfundo za m’Baibulo kungakuthandizeni kuti mupeze anzanu amene angamakuthandizeni