Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 BAIBULO LIMASINTHA ANTHU

Ndithandizeni Kuti Ndikhaleko Mosangalala Komanso Mwamtendere kwa Chaka Chimodzi Chokha

Ndithandizeni Kuti Ndikhaleko Mosangalala Komanso Mwamtendere kwa Chaka Chimodzi Chokha
  • CHAKA CHOBADWA: 1971

  • DZIKO: FRANCE

  • POYAMBA: NDINKAKONDA NDEWU, CHIWEREWERE KOMANSO NDINKAMWA MANKHWALA OSOKONEZA BONGO

KALE LANGA:

Banja lathu linkakhala ku Tellancourt, mudzi womwe uli kumpoto chakum’mawa kwa dziko la France. Bambo anga anali a ku France pomwe mayi anga anali a ku Italy. Ndili ndi zaka 8 banja lathu linasamukira kudera linalake losauka la ku Rome, m’dziko la Italy. Kumeneku tinkakumana ndi mavuto ambiri ndipo makolo athu ankakonda kumenyana chifukwa cha kusowa kwa ndalama.

Ndili ndi zaka 15 mayi anga ankakonda kundiuza kuti ndisamangokhala pakhomo koma ndipeze anzanga. Pang’ono ndi pang’ono ndinayamba kusapezeka pakhomo. Kenako ndinayamba kucheza ndi anthu amakhalidwe oipa. Tsiku lina ndinakumana ndi mkulu winawake yemwe ankaoneka ngati akundifunira zabwino koma anandipatsa mankhwala osokoneza bongo. Pofuna kumusonyeza kuti ndine wochangamuka, ndinalandira mankhwalawo. Posakhalitsa, ndinazolowera kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo ndiponso kuchita zachiwerewere. Ndinagwiriridwapo maulendo angapo ndipo zimenezi zinachititsa kuti ndiyambe kudziona kuti ndine wosafunika, moti sindinkacheza ndi munthu aliyense. Ndili ndi zaka 16 ndinkafuna kudzipha ndipo tsiku lina ndinamwa mowa n’kudumphira m’madzi kuti ndingofa. Ndinavulala kwambiri ndipo ndinakhala ndili chikomokere kwa masiku atatu.

Ndinayamba kuona kuti moyo ndi wofunika, komabe ndinayambanso kuchita utambwali komanso ndinkachita ndewu. Ndinkagonana ndi anthu osiyanasiyana ndiponso ndinkapatsa anthu mankhwala ogonetsa kenako n’kuwabera. Magulu a zigawenga ankandituma kuti ndidzizembetsa mankhwala osokoneza bongo m’dziko la Italy. Zimenezi zinkachititsa kuti ndizikhala moyo wothawathawa chifukwa apolisi ankandisakasaka. Ndinkadziwa kuti Mulungu akhoza kundithandiza kuti ndizikhala moyo wabwino, komabe zinkandivuta kusiya makhalidwe oipawa. Choncho ndinamupempha kuti andithandize kukhala mosangalala komanso mwamtendere kwa chaka chimodzi chokha.

MMENE BAIBULO LINASINTHIRA MOYO WANGA:

 

Ndili ndi zaka 24, ndinaganiza zosamukira ku England chifukwa ndinkaopa kuti ndikhoza kuphedwa ndi anthu amene ndinkawazembetsera mankhwala osokoneza bongo aja. Ndisananyamuke ndinapita kukaona mayi anga. Koma nditafika, ndinadabwa kwambiri nditapeza munthu wina dzina lake Annunziato Lugarà akuuza mayi angawo nkhani za m’Baibulo. * Ndinachita mantha chifukwa munthu ameneyu anali chigawenga choopsa kwambiri.  Nditamufunsa kuti akudzatani anandiuza kuti anasintha khalidwe lake ndipo ndi wa Mboni za Yehova. Anandiuzanso zimene anachita kuti asinthe khalidwe lakelo. Ndiyeno anandipempha kuti ndikapita ku England ndikakumane ndi a Mboni za Yehova ndipo ndinavomera. Koma nditangofika ku England ndinapitiriza khalidwe langa lija.

Tsiku lina ndinakumana ndi wa Mboni za Yehova yemwe ankagawira magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! mumsewu wina wodutsa anthu ambiri ku London. Pamenepa m’pamene ndinakumbukira zimene ndinamulonjeza Annunziato moti ndinapempha wa Mboniyo kuti azindiphunzitsa Baibulo.

Ndinayambadi kuphunzira Baibulo ndipo ndinkasangalala ndi zimene ndinkaphunzirazo. Mwachitsanzo lemba la 1 Yohane 1:9 linandikhudza kwambiri. Lembali limati: “Mulungu ndi wokhulupirika ndiponso wolungama, chotero tikavomereza machimo athu, adzatikhululukira ndi kutiyeretsa ku ntchito zonse zoipa.” Lembali linandithandiza kuti ndisinthe chifukwa ndinkadziona kuti ndine wodetsedwa kwambiri. Ndinayamba kumasonkhana ndi a Mboni za Yehova ku Nyumba ya Ufumu. A Mboniwo ankandilandira bwino ndipo ndinadabwa kwambiri chifukwa anthu ake anali ogwirizana. Zimenezi n’zomwe ndinkalakalaka pamoyo wanga ndipo ndinkafunitsitsa nanenso nditakhala wa Mboni chifukwa anthu ake ankachita zinthu ngati a banja limodzi.

Sindinavutike kusiya khalidwe lachiwerewere komanso kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo. Koma zinkandivuta kulemekeza anthu komanso kuchita zinthu mowaganizira. Panopa ndimalimbanabe ndi makhalidwe ena oipa koma Yehova akundithandiza kuti ndiwathetse. Ndinabatizidwa m’chaka cha 1997 n’kukhala wa Mboni za Yehova nditaphunzira Baibulo kwa miyezi 6.

PHINDU LIMENE NDAPEZA:

 

Nditabatizidwa ndinakwatira mtsikana wina dzina lake Barbara yemwe analinso atangobatizidwa kumene. Mnzanga wina ataona mmene ndinasinthira khalidwe langa nayenso anayamba kuphunzira Baibulo. Patapita nthawi anabatizidwa n’kukhala wa Mboni za Yehova. Kenako mchemwali wake wamkulu anaphunzira Baibulo n’kukhalanso wa Mboni. Chosangalatsanso n’choti agogo anga aakazi omwe anali ndi zaka zopitirira 80 anaphunziranso Baibulo ndipo anamwalira atabatizidwa.

Panopo ndine mkulu mumpingo umene ndimasonkhana ndipo ndimalalikira nthawi zonse limodzi ndi mkazi wanga. Timaphunzira Baibulo ndi anthu oyankhula Chitaliyana omwe amakhala mumzinda wa London. Nthawi zina ndimadzimvera chisoni ndikaganizira zimene ndinkachita kale koma mkazi wanga amandilimbikitsa kwambiri. Panopa ndikusangalala kwambiri chifukwa ndinapeza zinthu zomwe ndinkalakalaka. Ndimakhala mwamtendere komanso Yehova yemwe ali ngati bambo anga amandikonda kwambiri. Ndinapempha Mulungu kuti andithandize kukhala mwamtendere komanso mosangalala kwa chaka chimodzi chokha, koma zimene wandichitira ndi zosaneneka.

Panopa ndikusangalala kwambiri chifukwa ndinapeza zinthu zomwe ndinkalakalaka.