Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 NKHANI YA PACHIKUTO | N’CHIFUKWA CHIYANI TIYENERA KUCHITA ZINTHU MOONA MTIMA?

Kodi Kukhala Oona Mtima N’kwachikale?

Kodi Kukhala Oona Mtima N’kwachikale?

A Hitoshi ankagwira ntchito mu ofesi yowerengera ndalama m’bungwe lina loona zolemba anthu ntchito ku Japan. Tsiku lina akuona mmene ndalama zagwirira ntchito m’bungwe lawolo, abwana awo anawauza kuti alembe lipoti labodza. Koma a Hitoshi anauza abwanawo kuti sangachite zimenezo chifukwa n’zosagwirizana ndi zimene amakhulupirira. Abwanawo anawaopseza kuti awachotsa ntchito ndipo m’kupita kwa nthawi anawachotsadi.

Kenako a Hitoshi anayamba kufufuza ntchito ina, koma anakhumudwa kwambiri chifukwa cha zomwe zinkawachitikira. Mwachitsanzo, pa nthawi ina akufunsidwa mafunso pakampani ina imene inkafuna kuwalemba ntchito, a Hitoshi ananena kuti sachita zinthu zachinyengo. Munthu yemwe ankawafunsayo anadabwa kwambiri moti anati, “Aliponso anthu otero masiku ano?” Komabe achibale ndi anzawo a a Hitoshi ankawalimbikitsa kuti asasiye kuchita zinthu mokhulupirika. Kenako a Hitoshi anayamba kukayikira ngati kuchita zimenezi kunalidi kothandiza moti anafika ponena kuti, “Kodi ndimachita bwino kuulula kuti sindichita zachinyengo chifukwa cha zimene ndimakhulupirira?”

Zimene zinachitikira a Hitoshi zikungosonyeza kuti anthu ambiri m’dzikoli amaona kuti kuchita zachinyengo kulibe vuto lililonse. Ndipotu ena amaona kuti bizinezi yawo ingayende bwino kwambiri atamachita zachinyengo. Mayi wina wa ku South Africa anati: “Anthu ambiri amene ndimagwira nawo ntchito amachita zachinyengo moti ndimafunika kuyesetsa kuti ndisamachite nawo zimenezi.”

Masiku ano zinthu zachinyengo zili paliponse. Mwachitsanzo, pa kafukufuku yemwe anachita katswiri wina wa maphunziro a zamaganizo pa yunivesite ya Massachusetts Amherst, dzina lake Robert S. Feldman, anapeza kuti anthu 60 pa 100 alionse amati akamacheza ndi munthu wina amakhala atanena chinachake chabodza ikamatha 10 minitsi iliyonse. A Feldman anati: “Zimene tinapezazi zinatidabwitsa kwambiri chifukwa sitinkaganiza kuti bodza ndi lofala chonchi.” N’zodabwitsa kwambiri kuti anthu amanama ngakhale kuti iwowo safuna kunamizidwa.

Koma kodi n’chifukwa chiyani anthu ambiri masiku ano amakonda kunama, kuba komanso kuchita zinthu zina zachinyengo? Kodi kuchita zachinyengo kumabweretsa mavuto otani? Nanga kodi tingatani kuti tisamachite nawo zimenezi?