Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 NKHANI YA PACHIKUTO | N’CHIFUKWA CHIYANI TIYENERA KUCHITA ZINTHU MOONA MTIMA?

Kodi Chinyengo N’choopsa Bwanji?

Kodi Chinyengo N’choopsa Bwanji?

Mayi wina wa ku South Africa, dzina lake Samantha, anati: “Mavuto ena angathe ngati utangochitako kachinyengo pang’ono.”

Kodi mukugwirizana ndi zimene mayiyu ananena? N’zoona kuti munthu aliyense amakumana ndi mavuto amene angamuchititse kuganiza zochita chinyengo. Komano zimene timachita tikakumana ndi mavuto oterowo zimasonyeza zomwe zili mumtima mwathu. Mwachitsanzo, munthu akhoza kulolera kuchita chinyengo n’cholinga choti asagwidwe komanso asachite manyazi. Koma zoona zake zikadziwika, munthuyo amakumana ndi mavuto aakulu. Tiyeni tione mavuto amene amabwera chifukwa cha chinyengo.

ANTHU AMASIYA KUKUKHULUPIRIRA

Anthu akamakhulupirirana m’pamene amagwirizana kwambiri. Koma sikuti zimenezi zimangochitika lero ndi lero. Anthu amayamba kukhulupirirana akamacheza nthawi zonse n’kumauzana zakukhosi komanso kuchita zinthu moganizirana. Komabe wina akachita zachinyengo ngakhale kamodzi kokha, mnzakeyo amasiya kumukhulupirira. Ndipotu zimakhala zovuta kuti ayambirenso kukhulupirirana.

Kodi munayamba mwanamizidwapo ndi munthu amene munkaona kuti ndi mnzanu wapamtima? Ngati ndi choncho, n’zosakayikitsa kuti munakhumudwa kwambiri. Kunena zoona chinyengo chimasokoneza mgwirizano ndiponso chibale.

CHINYENGO CHILI NGATI MATENDA OPATSIRANA

Pulofesa wa pa yunivesite ya California, dzina lake Robert Innes, anachita kafukufuku wina ndipo anapeza kuti “chinyengo chili ngati matenda opatsirana.” Choncho zimakhala zosavuta kuti munthu ayambe kuchita chinyengo ngati amakonda kuchita zinthu ndi munthu wachinyengo.

Kodi mungatani kuti musamachite nawo zinthu zachinyengo? Werengani mfundo za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni.