Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 NKHANI YA PACHIKUTO | BAIBULO—BUKU LOMWE LINAPULUMUKA M’ZAMBIRI

Baibulo Linasungidwa Bwino Kuti Lisawole

Baibulo Linasungidwa Bwino Kuti Lisawole

VUTO LIMENE LINALIPO: Anthu omwe ankalemba komanso kukopera mipukutu ya Baibulo ankagwiritsa ntchito gumbwa komanso zikopa. (2 Timoteyo 4:13) Komatu zimenezi zikanachititsa kuti mipukutuyi iwonongeke mosavuta. N’chifukwa chiyani tikutero?

Gumbwa amang’ambika, kusuluka komanso kutha mosavuta. Richard Parkinson ndi Stephen Quirke, anaphunzira zinthu zosiyanasiyana za ku Egypt ndipo anati: “Gumbwa akhoza kuwola n’kutsala ulusi kapenanso fumbi lokhalokha. Mpukutu ukakhala nthawi yaitali umachita nkhungu kapenanso kuwola chifukwa cha chinyezi ndipo akaukwirira umadyedwa ndi chiswe.” Komanso mipukutu ina ya gumbwa itapezeka, sinasungidwe bwino ndipo inawonongeka chifukwa cha chinyezi komanso kuwala.

Mipukutu ya chikopa imakhala yolimba kusiyana ndi ya gumbwa. Koma nayonso imawonongeka ikasungidwa pamalo otentha, achinyezi kapenanso owala kwambiri. * Mipukutuyi imadyedwanso ndi tizilombo. Buku lina linanena kuti: “Kawirikawiri mipukutu yakale siikhalitsa.” (Everyday Writing in the Graeco-Roman East) Choncho zikanakhala kuti mipukutu ya Baibulo inawola, uthenga wake ukanatheranso pomwepo.

ZIMENE ZINATHANDIZA KUTI BAIBULO LISUNGIKE: Lamulo lachiyuda linkalimbikitsa mfumu iliyonse kuti izikopera “buku lakelake la chilamulo” lomwe ndi mabuku 5 oyambirira a m’Baibulo. (Deuteronomo 17:18) Komanso pofika chakumapeto kwa nthawi ya atumwi n’kuti akatswiri okopera malemba atakopera mipukutu yambiri. Zimenezi zinathandiza kuti malemba azipezeka m’masunagoge a ku Isiraeli ngakhalenso kumadera akutali monga ku Makedoniya. (Luka 4:16, 17; Machitidwe 17:11) Komano zinatheka bwanji kuti mipukutuyi isungidwe mpaka pano?

Mipukutu ya ku Nyanja Yakufa inasungidwa kwa zaka zambiri m’mitsuko yomwe inaikidwa m’mapanga, m’madera ouma

Katswiri wina wa Chipangano Chatsopano dzina lake Philip W. Comfort ananena kuti: “Ayuda ankakonda kusunga mipukutu m’mitsuko n’cholinga choti isawonongeke.” Ndipo zikuoneka kuti Akhristu nawonso ankachita zomwezo chifukwa mipukutu ina yoyambirira ya Baibulo inapezeka m’mitsuko, m’zipinda zamdima ndi m’mapanga a m’madera otentha kwambiri.

ZOTSATIRA ZAKE: Mipukutu yambiri ya Baibulo idakalipo ndipo yakhalapo kwa zaka zoposa 2,000. Kunena zoona palibenso mipukutu ya mabuku ena akale yomwe yakhalapo kwa nthawi yaitali chonchi.

^ ndime 5 Mwachitsanzo, chikalata cholengeza kuti dziko la United States ndi lodziimira palokha (U.S. Declaration of Independence), chinalembedwa pachikopa. Panopa padutsa zaka zosapitirira 250 kuchokera nthawi yomwe chikalatachi chinalembedwa, koma zilembo zake zimavuta kuwerenga chifukwa zinafufutika.