Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Zachiwawa Zidzatha Padzikoli?

Kodi Zachiwawa Zidzatha Padzikoli?

Kodi inuyo kapena munthu wina wa m’banja lanu anachitiridwapo zinthu zachiwawa? Kodi mumachita mantha kuti tsiku lina zidzakuchitikirani? Anthu ena amanena kuti zachiwawa “zikuchuluka padziko lonse ndipo zikuchititsa kuti anthu azikumana ndi mavuto azaumoyo.” Taonani zitsanzo izi:

NKHANZA ZA M’BANJA KOMANSO ZOKHUDZA KUGONANA: Lipoti lina la bungwe la United Nations linanena kuti: “Mayi mmodzi pa atatu alionse anamenyedwapo ndi mwamuna wake kapenanso kuchitiridwa nkhanza zokhudza kugonana ndi munthu womudziwa. Komanso mayi mmodzi pa amayi 5 alionse akhoza kugwiriridwa.”

UCHIFWAMBA NDI UMBANDA: Malipoti amasonyeza kuti ku United States kokha kuli magulu a zauchifwamba oposa 30,000. Ndipo ku Latin America pafupifupi munthu mmodzi pa atatu alionse anachitiridwapo zauchifwamba.

KUPHA ANTHU MWACHISAWAWA: Kafukufuku amasonyeza kuti m’chaka cha 2012 chokha, anthu pafupifupi 500,000 anaphedwa ndi zigawenga padziko lonse. Chiwerengerochi ndi chachikulu poyerekezera ndi anthu omwe anaphedwa pa nkhondo m’chakachi. Mayiko a kum’mwera kwa Africa komanso ku Central America ndi omwe anali ndi chiwerengero chokwera kwambiri cha anthu ophedwa. Mwachitsanzo, ku Latin America kunaphedwa anthu oposa 100,000 m’chaka cha 2013, ndipo ku Brazil kunaphedwa anthu oposa 50,000. Kodi pamenepa tinganene kuti zachiwawa zidzatha padzikoli?

KODI N’ZOTHEKA KUTHETSA ZACHIWAWA?

N’chifukwa chiyani zachiwawa zikuchitika padziko lonse? Pali zifukwa zambiri monga izi: Kuponderezana pakati pa anthu olemera ndi osauka, uchidakwa, kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo, kuona moyo wa anthu ena ngati wosafunika komanso kukulira m’banja kapena m’dera lomwe anthu amakonda zachiwawa. Anthu enanso amachita zachiwawa chifukwa chakuti anthu ambiri ochita khalidweli sapatsidwa chilango chokhwima.

Komabe mayiko ena akuyesetsa kuchepetsa zachiwawa. Mwachitsanzo, mumzinda wa São Paulo, ku Brazil, chiwerengero cha anthu ophedwa mwachisawawa chatsika kwambiri m’zaka 10 zapitazi. Ngakhale zili choncho, zauchifwamba zimachitikabe mobwerezabwereza moti anthu 10 pa 100,000 amaphedwa. Ndiyeno funso n’kumati, n’chiyani chingathandize kuti zachiwawa zitheretu padziko lonse?

Kuti zachiwawa zitheretu, anthu afunika kusintha mmene amaonera zinthu komanso khalidwe lawo. Mwachitsanzo, ayenera kusiya kunyada, umbombo ndi kudzikonda, n’kuyamba kukhala achikondi, aulemu ndiponso oganizira ena.

Kodi n’chiyani chingathandize munthu kuti asiye makhalidwe oipa? Taonani zimene Baibulo limaphunzitsa:

  • “Chifukwa kukonda Mulungu kumatanthauza kusunga malamulo ake, ndipo malamulo akewo ndi osalemetsa.”1 Yohane 5:3.

  • “Kuopa Yehova kumatanthauza kudana ndi zoipa.” *Miyambo 8:13.

 Anthu achiwawa angasinthe khalidwe lawo ngati atamakonda Mulungu komanso kupewa zinthu zomwe zingamukhumudwitse. Ndipotu zimenezi n’zotheka.

Chitsanzo pa nkhaniyi ndi Alex, * amene anakhala m’ndende ina ya ku Brazil kwa zaka 19, chifukwa cha milandu yosiyanasiyana yomenya ndi kuvulaza anthu. Iye anayamba kuphunzira Baibulo ndi a Mboni za Yehova ndipo anabatizidwa mu 2000. Kodi anasinthadi khalidwe lakeli? Alex anasinthiratu ndipo anati: “Panopa ndimakonda kwambiri Mulungu chifukwa ndimadziwa kuti anandikhululukira. Komatu ndinasiya makhalidwewa chifukwa chokonda Mulungu komanso kusafuna kumukhumudwitsa.”

César wa ku Brazil ankathyola nyumba za anthu komanso kuba moopseza ndi mfuti. Iye anachita zimenezi kwa zaka 15. Ndiye n’chiyani chinamuthandiza kuti asinthe? Pa nthawi imene anali kundende, anakumana ndi a Mboni za Yehova ndipo anayamba kuphunzira Baibulo. César anafotokoza kuti: “Nditangoyamba kuphunzira, ndinazindikira cholinga cha moyo ndiponso ndinayamba kukonda Mulungu komanso kumuopa. Zimenezi zinandithandiza kuti ndisiyiretu kuchita zinthu zoipa zomwe amadana nazo. Sindinkafunanso kuchita chilichonse chosonyeza kuti sindikuyamikira chifundo chake. Choncho ndinasintha khalidwe langa.”

Phunzirani zimene mungachite kuti mudzakhale m’dziko lopanda chiwawa

Zimene zinachitikira Alex ndi César, zikusonyeza kuti Baibulo lili ndi mphamvu zothandiza anthu kusintha zochita komanso maganizo oipa. (Aefeso 4:23) Alex ananenanso kuti: “Zimene ndinaphunzira m’Baibulo zinali ngati madzi oyera bwino omwe ankayeretsa makhalidwe anga pang’onopang’ono. Ndinali ndisanaganizepo kuti ndingadzasinthe chonchi.” Uwu ndi umboni wakuti tikamawerenga uthenga wa m’Baibulo womwe ndi woyera, tingathe kuchotsa maganizo alionse oipa mumtima mwathu. Mawu a Mulungu alidi ndi mphamvu yoyeretsa maganizo a anthu. (Aefeso 5:26) Monga mmene taonera, anthu omwe kale anali ndi makhalidwe oipa akhoza kusintha n’kukhala achifundo komanso amtendere. (Aroma 12:18) Ndipo akamatsatira mfundo za m’Baibulo, amakhalanso ndi mtendere wamumtima.Yesaya 48:18.

A Mboni za Yehova opitirira 8 miliyoni omwe akupezeka m’mayiko oposa 240, akudziwa bwino chimene chingathandize kuti zachiwawa zitheretu. Ngakhale kuti ndi ochokera m’mitundu yosiyanasiyana, onse amakonda Mulungu komanso kumuopa. Amakondananso kwambiri ndipo amakhala mwamtendere ngati banja limodzi. (1 Petulo 4:8) Umenewutu ndi umboni wakuti n’zotheka kuthetsa zachiwawa padzikoli.

ZINTHU ZACHIWAWA ZITHA POSACHEDWAPA

Baibulo limalonjeza kuti posachedwapa Mulungu athetsa zachiwawa zonse padzikoli. Ndipo limatitsimikizira kuti anthu onse okonda zachiwawa adzaphedwa “m’tsiku lachiweruzo ndi chiwonongeko cha anthu osaopa Mulungu.” (2 Petulo 3:5-7) Pa nthawiyi sikudzakhalanso anthu ozunza ena. Koma kodi tingatsimikize bwanji kuti Mulungu ndi wofunitsitsa kuthetseratu zachiwawa?

Baibulo limanena kuti “Mulungu amadana kwambiri ndi aliyense wokonda chiwawa.” (Salimo 11:5) Mlengi wathu amakonda mtendere ndi chilungamo. (Salimo 33:5; 37:28) N’chifukwa chake sadzalola kuti anthu ochita zachiwawa akhalepo mpaka kalekale.

Dziko latsopano komanso lamtendere layandikira. (Salimo 37:11; 72:14) Choncho tikukulimbikitsani kuti muyambe kuphunzira Baibulo ndi a Mboni za Yehova kuti mudziwe zimene mungachite kuti mudzakhale nawo m’dziko limeneli.

^ ndime 12 Dzina la Mulungu ndi Yehova ndipo limapezeka m’Baibulo.

^ ndime 14 Mayina asinthidwa.