NSANJA YA OLONDA Na. 4 2016 | Baibulo—Buku Lomwe Linapulumuka M’zambiri

Panali zinthu zambiri zomwe zikanachititsa kuti Baibulo lisafike masiku ano. N’chifukwa chiyani kupulumuka kwa Baibulo n’kofunika kwa ifeyo?

NKHANI YAPACHIKUTO

Kodi Kudziwa Mmene Baibulo Linapulumukira N’kothandiza?

Palibe buku lina lililonse la chipembedzo lomwe lakhala likuthandiza anthu kuti azikhulupirira zinthu zolondola. Kodi Baibulo tingalikhulupirire?

NKHANI YAPACHIKUTO

Baibulo Linasungidwa Bwino Kuti Lisawole

Anthu omwe analemba komanso kukopera Baibulo ankagwiritsa ntchito mipukutu yopangidwa ndi gumbwa komanso zikopa. Kodi zinatheka bwanji kuti mipukutu yambiri ya Baibulo ifike masiku ano?

NKHANI YAPACHIKUTO

Baibulo Linasungidwa Ngakhale Kuti Ena Ankalitsutsa

Atsogoleri andale komanso azipembedzo akhala akuletsa anthu kumasulira, kusindikiza ngakhalenso kukhala ndi Baibulo, koma sizinatheke.

NKHANI YAPACHIKUTO

Baibulo Linapulumuka Ngakhale Kuti Ena Ankafuna Kusintha Uthenga Wake

Anthu amaganizo olakwika ankafuna kusintha uthenga wa m’Baibulo. Koma zolinga zawozi zinadziwika ndiponso zinalephereka?

NKHANI YAPACHIKUTO

N’chifukwa Chiyani Baibulo Linapulumuka

Kodi Baibulo ndi losiyana bwanji ndi mabuku ena?

Kodi Mukudziwa?

Kodi chochititsa chidwi n’chiyani ndi mmene Yesu ankachitira zinthu ndi akhate? Kodi atsogoleri achipembedzo chachiyuda ankalola kuti mwamuna asiye mkazi wake pa zifukwa ziti?

Kodi Zachiwawa Zidzatha Padzikoli?

Anthu ambiri anasiya kuchita zachiwawa. Mfundo zomwe zinawathandiza zingathandizenso anthu ena?

BAIBULO LIMASINTHA ANTHU

Ndinasintha Khalidwe Langa Movutikira Kwambiri

Kodi munthu wina anapeza bwanji mtendere wamumtima atasiya khalidwe loonera zolaula?

Kodi Zimene Mumakhulupirira Zimagwirizana Ndi Zimene Baibulo Limaphunzitsa

Masiku ano pali zipembedzo zambiri zachikhristu, koma zimasiyana pa nkhani ya zikhulupiriro. Kodi mungadziwe bwanji amene amaphunzitsa zoona?

Kodi Baibulo Limanena Zotani?

Kodi Mulungu angagwiritse ntchito mabungwe azipembedzo pofuna kuti anthu akhale naye paubwenzi?

Zina zimene zili pawebusaiti

Kodi Baibulo Ndi Lochokera kwa Mulungu?

Anthu ambiri amene analemba Baibulo amati analemba maganizo a Mulungu. N’chifukwa chiyani amatero?