Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 NKHANI YA PACHIKUTO | KODI MUNGATANI MUNTHU YEMWE MUNKAMUKONDA AKAMWALIRA?

Zimene Mungachite Ngati Muli Ndi Chisoni

Zimene Mungachite Ngati Muli Ndi Chisoni

Pali malangizo osiyanasiyana okhudza zimene anthu angachite ngati ali ndi chisoni. Komabe, sikuti malangizo onse amene amaperekedwa amakhala othandiza. Mwachitsanzo, mukakhala ndi chisoni anthu ena angakuuzeni kuti musalire komanso musasonyeze mmene mukumvera. Pomwe ena angakukakamizeni kuti mulire komanso muchite zinthu zosonyeza kuti muli ndi chisoni. Baibulo lili ndi malangizo othandiza kwambiri pa nkhaniyi, omwenso akugwirizana kwambiri ndi zimene ochita kafukufuku anapeza.

Anthu a zikhalidwe zina amanena kuti mwamuna salira. Komabe sitiyenera kuchita manyazi ndi kulira ngakhale patakhala pagulu. Akatswiri a maganizo amanena kuti sikulakwa kulira mogwetsa misozi pofuna kusonyeza chisoni. Ndipo kusonyeza chisoni kungathandize kuti pakapita nthawi muyambenso kukhala osangalala, ngakhale kuti imfa ndi yowawa. Koma munthu amene amayesa kubisa chisoni chake amavutika kwambiri. Baibulo silinena kuti kulira n’kulakwa kapenanso kuti mwamuna sayenera kulira. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi Yesu. Lazaro yemwe anali mnzake wapamtima atamwalira, Yesu analira ngakhale kuti ankadziwa kuti ali ndi mphamvu zoukitsa akufa.—Yohane 11:33-35.

Nthawi zambiri anthu amene wachibale wawo wamwalira mwadzidzidzi, amakwiya kwambiri. Iwo angakwiye pazifukwa zosiyanasiyana ndipo nthawi zina chingakhale chifukwa choti munthu yemwe akumudalira wanena zinazake zokhumudwitsa kapenanso zopanda umboni. Mwachitsanzo, bambo wina wa ku South Africa dzina lake Mike ananena kuti, “Bambo anga anamwalira ndili ndi zaka 14 zokha, ndipo pa maliro awo m’busa wina wa Anglican ananena kuti Mulungu amafuna anthu abwino ndipo amawatenga msanga asanakalambe. Zimenezi zinandikwiyitsa koopsa chifukwa pa nthawiyi nafenso tinkawafuna kwambiri bambo athuwo. Panopa patha zaka 63 koma zimandipwetekabe.”

Nthawi zina anthu enanso amadziimba mlandu wachibale akamwalira mwadzidzidzi. Mwinanso anganene kuti, ‘Munthuyutu sakanamwalira ndikanachita zakutizakuti.’ Kapenanso angadziimbe mlandu chifukwa chakuti munthuyo asanamwalire anakangana naye.

Ngati mukudziimba mlandu kapenanso kukwiya chifukwa cha imfa ya wachibale wanu, si bwino kubisa mmene mukumvera. M’malo mwake, mungauze mnzanu yemwe angakumvetseni ndiponso sangakuimbeni mlandu chifukwa cha mmene mukumvera. Baibulo limanena kuti: “Bwenzi lenileni limakukonda nthawi zonse, ndipo bwenzilo ndi m’bale amene anabadwira kuti akuthandize pakagwa mavuto.”—Miyambo 17:17.

Yehova Mulungu, yemwe ndi Mlengi wathu angakhale bwenzi labwino kwambiri kwa munthu amene waferedwa. Choncho muyenera kupemphera kwa iye chifukwa “amakuderani nkhawa.” (1 Petulo 5:7) Ndipotu iye amalonjeza kuti maganizo a anthu onse omwe amapemphera kwa iye adzatsitsimulidwa ndi “mtendere wa Mulungu umene umaposa kuganiza mozama kulikonse.” (Afilipi 4:6, 7) Mulungu angakutonthozeninso kudzera m’Mawu ake, omwe ndi Baibulo. Mungachite bwino kupeza mavesi a m’Baibulo omwe angakutonthozeni n’kuwalemba penapake. (Onani  bokosi.) Mwinanso mungaloweze ena mwa malembawa. Kuganizira mfundo za m’malembawa n’kothandiza kwambiri makamaka usiku pamene muli nokha komanso tulo sitikubwera.—Yesaya 57:15.

 Posachedwapa, bambo wina dzina lake Jack, mkazi wake anamwalira ndi matenda a khansa. Jack ananena kuti nthawi zina amasowa munthu wocheza naye. Koma amalimbikitsidwa akapemphera kwa Yehova. Iye ananena kuti: “Ndikapemphera kwa Yehova, sindionanso kuti ndili ndekha. Nthawi zambiri ndikadzidzimuka m’kati mwa usiku sindigonanso. Zikatere ndimangotenga Baibulo n’kuyamba kuwerenga, kenako ndimaganizira zomwe ndawerengazo ndiponso kupemphera kwa Yehova. Zimenezi zimandithandiza kuti ndiyambe kumva bwino mumtimamu ndipo tulo timabweranso.”

Chitsanzo china ndi Vanessa yemwe mayi ake anamwalira atadwala kwambiri. Nayenso anaona kuti pemphero ndi lothandiza kwambiri. Vanessa ananena kuti: “Zinthu zikafika povuta kwambiri ndinkangoyamba kupemphera n’kumatchula dzina la Mulungu kwinaku ndikulira. Yehova ankamva mapemphero anga ndipo ankandipatsadi mphamvu.”

Anthu ena amene amakonda kulangiza anthu amene akuvutika ndi chisoni, amawauza kuti azithandiza ena kapenanso kugwira ntchito zina za m’dera lawo. Zimenezi zingathandize kuti azisangalala komanso kuti chisoni chawo chichepeko. (Machitidwe 20:35) Akhristu ambiri omwe aferedwa amayesetsa kuthandiza ena ndipo amaona kuti kuchita zimenezi kumawatonthoza kwambiri.—2 Akorinto 1:3, 4.

Baibulo siliphunzitsa zimenezi. M’malo mwake, limafotokoza zifukwa zitatu zimene zimachititsa kuti anthu azifa.—Mlaliki 9:11; Yohane 8:44; Aroma 5:12.