Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mmene dzina la Mulungu linkalembedwera m’mipukutu yakale ya Baibulo (mwawalitsidwamo)

Kodi Baibulo Limanena Zotani?

Kodi Baibulo Limanena Zotani?

Kodi Mulungu ali ndi dzina?

ANTHU ENA AMAKHULUPIRIRA kuti Mulungu alibe dzina ndipo ena amanena kuti dzina lake ndi Mulungu kapena Ambuye. Pomwe enanso amanena kuti Mulungu ali ndi mayina ambirimbiri. Kodi inuyo mukuganiza bwanji?

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

“Inu, amene dzina lanu ndinu Yehova, Inu nokha ndinu Wam’mwambamwamba, wolamulira dziko lonse lapansi.”—Salimo 83:18.

MFUNDO ZINANSO ZOMWE BAIBULO LIMANENA

  • N’zoona kuti Mulungu ali ndi mayina audindo ambiri koma ali ndi dzina lenileni limodzi lomwe anadzipatsa.—Ekisodo 3:15.

  • Mulungu si wosamvetsetseka ndipo amafuna kuti timudziwe bwino.—Machitidwe 17:27.

  • Ngati munthu akufuna kukhala pa ubwenzi ndi Mulungu, choyamba amafunika kudziwa dzina lake.—Yakobo 4:8.

Kodi kutchula dzina la Mulungu n’kulakwa?

KODI MUNGAYANKHE BWANJI?

  • Inde

  • Ayi

  • Mwina

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

“Usagwiritse ntchito dzina la Yehova Mulungu wako mosasamala.” (Ekisodo 20:7) Choncho n’kulakwa kugwiritsa ntchito dzina la Mulungu mopanda ulemu.—Yeremiya 29:9.

MFUNDO ZINANSO ZOMWE BAIBULO LIMANENA

  • Yesu ankadziwa komanso kutchula dzina la Mulungu.—Yohane 17:25, 26.

  • Mulungu amafuna kuti tizitchula dzina lake.—Salimo 105:1.

  • Adani a Mulungu safuna kuti anthu azigwiritsa ntchito dzina la Mulungu.—Yeremiya 23:27.