Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Dzikoli silidzawonongeka ndi zochita za anthu chifukwa Mulungu akulonjeza kuti zinthu zidzakhala bwino kwambiri mtsogolo

 NKHANI YA PACHIKUTO | KODI ZINTHU PADZIKOLI ZAFIKA POIPA KWAMBIRI

Kodi Baibulo Limanena Zotani?

Kodi Baibulo Limanena Zotani?

ZAKA zambirimbiri m’mbuyomo, Baibulo linaneneratu za zinthu zoipa zomwe zikuchitika masiku ano. Koma chosangalatsa kwambiri n’chakuti linaneneratunso kuti anthu adzakhala ndi moyo wabwino kwambiri mtsogolo. Zomwe Baibulo linanenazi tiyenera kuzikhulupirira ndi mtima wonse chifukwa maulosi ake ambiri akhala akukwaniritsidwa mochititsa chidwi kwambiri.

Mwachitsanzo, taganizirani za maulosi awa:

  • “Mtundu udzaukirana ndi mtundu wina, ndipo ufumu udzaukirana ndi ufumu wina. Kudzakhala njala ndi zivomezi m’malo osiyanasiyana.”​—Mateyu 24:7.

  • “Koma dziwa kuti, masiku otsiriza adzakhala nthawi yapadera komanso yovuta. Pakuti anthu adzakhala odzikonda, okonda ndalama, odzimva, odzikweza, onyoza, osamvera makolo, osayamika, osakhulupirika, osakonda achibale awo, osafuna kugwirizana ndi anzawo, onenera anzawo zoipa, osadziletsa, oopsa, osakonda zabwino, achiwembu, osamva za ena, odzitukumula ndiponso onyada, okonda zosangalatsa, m’malo mokonda Mulungu.”​—2 Timoteyo 3:1-4.

Zinthu zoipa zomwe anthu akuona masiku ano, zikukwaniritsa zomwe Baibulo linaneneratu kalekale. Zinthu zafikadi poipa kwambiri padzikoli moti anthu sangathe kuthetsa zomwe zikuchitikazi. Baibulo limanena kuti anthu alibe mphamvu komanso nzeru zoti angathetsere zinthu zoipazi. Malemba awa akufotokoza bwino zimenezi:

  • “Pali njira yooneka ngati yowongoka kwa munthu, koma mapeto ake ndi imfa.”​—Miyambo 14:12.

  • “Munthu wapweteka munthu mnzake pomulamulira.”​—Mlaliki 8:9.

  • “Munthu . . . alibe ulamuliro wowongolera njira ya moyo wake.”​—Yeremiya 10:23.

Ngati anthu atapitiriza kuchita zilizonse zomwe akufuna, zinthu zikhoza kufikadi poipa kwambiri. Koma si kuti zochita za anthuzi zingadzapangitse kuti dzikoli lithe. N’chifukwa chiyani tikutero? Baibulo limanena kuti:

  • Mulungu ‘anakhazikitsa dziko lapansi pamaziko olimba. Silidzagwedezeka mpaka kalekale, mpaka muyaya.’​—Salimo 104:5.

  • “M’badwo umapita ndipo m’badwo wina umabwera, koma dziko lapansi lidzakhalapobe mpaka kalekale.”​—Mlaliki 1:4.

  • “Olungama adzalandira dziko lapansi, ndipo adzakhala mmenemo kwamuyaya.”​—Salimo 37:29.

  • “Padziko lapansi padzakhala tirigu wambiri. Pamwamba pa mapiri padzakhala tirigu wochuluka.”​—Salimo 72:16.

 Malemba a m’Baibulowa akutithandiza kupeza mayankho. Si kuti kuwonongeka kwa chilengedwe, kusowa kwa chakudya ndi madzi komanso kuchuluka kwa matenda, zingadzafike poipa mpaka anthu onse kutha padzikoli. Dzikoli silidzatha ndi nkhondo ya mabomba a nyukiliya. Tikutero chifukwa tsogolo la dzikoli lili m’manja mwa Mulungu. Mulungu anapatsa anthu ufulu wopanga zomwe akufuna. Komabe, anthuwa adzakolola mogwirizana ndi zochita zawo. (Agalatiya 6:7) Dzikoli silili ngati galimoto yopanda mabuleki yomwe ikuthamanga kwambiri moti dalaivala wake akulephera kuiwongolera. Mulungu anaikira anthu malire ndipo sadzawalola kuwononga dzikoli mpaka kalekale.​—Salimo 83:18; Aheberi 4:13.

Mulungu adzabweretsa “mtendere wochuluka” padzikoli. (Salimo 37:11) Nkhaniyi yangofotokoza zinthu zochepa zomwe zidzachitike mtsogolo. A Mboni za Yehova amaphunzira nkhani zambiri m’Baibulo zofotokoza zinthu zochititsa chidwi zomwe zidzachitike kutsogoloku.

A Mboni za Yehova ndi anthu a misinkhu komanso zikhalidwe zosiyanasiyana ndipo amachokera m’mayiko osiyanasiyananso. Amapembedza Mulungu m’modzi woona ndipo Baibulo limati dzina lake ndi Yehova. A Mboniwa sachita mantha ndi zinthu zamtsogolo chifukwa Baibulo limanena kuti: “Pakuti Yehova, Mlengi wa kumwamba, Mulungu woona, amene anaumba dziko lapansi ndi kulipanga, amene analikhazikitsa mwamphamvu, amene sanalilenge popanda cholinga, amene analiumba kuti anthu akhalemo, wanena kuti: ‘Ine ndine Yehova ndipo palibenso wina.’”​—Yesaya 45:18.

M’nkhaniyi taona zomwe Baibulo limanena zokhudza tsogolo la dzikoli komanso mmene moyo wa anthu udzakhalire mtsogolo. Kuti mudziwe zambiri pa nkhaniyi, werengani mutu 5 m’kabuku kakuti Uthenga Wabwino Wochokera kwa Mulungu. Kabukuka ndi kofalitsidwa ndi a Mboni za Yehova ndipo mungakapeze pa www.jw.org/ny

Mungaonerenso vidiyo yakuti N’chifukwa Chiyani Mulungu Analenga Dziko Lapansi? pawebusaiti ya www.jw.org/ny. (Pitani pomwe alemba kuti MABUKU > MAVIDIYO)