Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Milford Sound

 ANTHU NDI MAYIKO

Dziko la New Zealand

Dziko la New Zealand

PAFUPIFUPI zaka 800 zapitazo, anthu a mtundu wa Maori anasamuka ku Polynesia n’kuyenda mtunda wautali kwambiri panyanja yayikulu n’kukakhazikika ku New Zealand. Ku Polynesia n’kotentha kwambiri kusiyana ndi ku New Zealand. Ku New Zealand kuli mapiri ambiri, madzi oundana, akasupe amadzi otentha komanso kumagwa sinowo kapena kuti chipale chofewa. Patatha zaka 500, anthu enanso ochokera ku Europe komwe ndi kutali kwambiri, anabwera kudzakhazikika m’dzikoli. Chikhalidwe cha anthu a ku New Zealand panopo, n’chosakanikirana ndi cha anthu a ku Britain, Germany komanso Polynesia. Anthu pafupifupi 90 pa 100 aliwonse m’dzikoli, amakhala m’tauni. Mzinda wa Wellington womwe ndi likulu la dzikoli, umadziwika kuti ndi likulu la kum’mwera kwenikweni kwa dziko lapansi.

Ziphalaphala zowira zochokera pansi panthaka ku North Island

 Dziko la New Zealand lili ndi malo ambiri ochititsa chidwi. Choncho ngakhale kuti lili kutali kwambiri, alendo pafupifupi 3 miliyoni amalowa m’dzikoli chaka chilichonse kudzaona malowa.

Mtengo wa silver fern umatalika kuposa mamita 10

Mu 1948 anthu anazindikira kuti mbalame za takahe zikanalipobe. Mbalamezi siziuluka

Ku New Zealand kuli nyama komanso zachilengedwe zambiri. Ndipo ndi dziko lokhali padziko lonse lapansi lomwe lili ndi mitundu yambiri ya mbalame zomwe siziuluka. Kumapezekanso mtundu winawake wa abuluzi otchedwa tuatara, omwe umatha kukhala ndi moyo mpaka zaka 100. Nyama zoyamwitsa za m’dzikoli ndi monga mitundu yochepa ya mileme komanso nsomba zikuluzikulu ngati anangumi ndi ma dolphin.

A Mboni za Yehova akhala akulalikira ku New Zealand kwa zaka pafupifupi 120. Amaphunzitsa anthu Baibulo m’zinenero pafupifupi 19 kuphatikizapo zinenero za ku Polynesia ngati Chinuweya, Chirarotonga, Chisamowa ndi Chitongani.

Amaori akuvina atavala zovala zachikhalidwe chawo