Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Munthu amene ali ndi dzina labwino kapena mbiri yabwino, anthu amamudalira komanso kumulemekeza

‘Kusankha Dzina Labwino Ndi Kwabwino Kusiyana ndi Chuma Chochuluka’

‘Kusankha Dzina Labwino Ndi Kwabwino Kusiyana ndi Chuma Chochuluka’

DZINA labwino kapena mbiri ndi zinthu zofunika kwambiri moti m’mayiko ena muli malamulo oteteza zinthu zimenezi. Malamulowo amateteza anthu ku nkhani zabodza komanso miseche. Nkhani zabodza zingakhale mawu onyoza munthu wina ochita kulembedwa, owulutsidwa pawailesi kapena pa TV. Pamene miseche ingakhale kulankhula zinthu zoipitsa mbiri ya munthu wina. Zimenezi zikutikumbutsa mawu a m’Baibulo akuti: “Ndi bwino kusankha dzina labwino kusiyana ndi chuma chochuluka. Kulemekezedwa kuli bwino kuposa siliva ndi golide.” (Miyambo 22:1) Kodi tingatani kuti tikhale ndi dzina labwino komanso kuti anthu ena azitilemekeza? M’Baibulo muli malangizo othandiza pa nkhani imeneyi.

Mwachitsanzo, taganizirani zimene Baibulo limanena mu Salimo 15. Poyankha funso lakuti, ‘Ndani amene angakhale mlendo m’chihema cha Mulungu?’ wamasalimo analemba kuti: “Ndi amene . . . amachita chilungamo, ndi kulankhula zoona mumtima mwake. Iye sanena miseche . . . Sachitira mnzake choipa, ndipo satonza bwenzi lake lapamtima. Iye sagwirizana ndi munthu aliyense wonyansa . . . Akalumbira kuchita zinthu zimene kenako zakhala zoipa kwa iye, sasintha malingaliro ake. . . . Ndipo salandira chiphuphu.” (Salimo 15:1-5) Kodi inuyo simungalemekeze munthu amene amatsatira mfundo zapamwamba ngati zimenezi?

Khalidwe lina limene lingachititse kuti munthu azilemekezedwa ndi kudzichepetsa. Lemba la Miyambo 15:33 limati: “Ulemerero umabwera pambuyo pa kudzichepetsa.” Taganizirani izi: Munthu wodzichepetsa amaona zimene sakuchita bwino ndipo amayesetsa ndi mtima wonse kuti asinthe. Komanso amakhala wokonzeka kupepesa ngati wakhumudwitsa winawake. (Yakobo 3:2) Koma munthu wonyada sangachite zimenezi, m’malo mwake amafulumira kukwiya. Lemba la Miyambo 16:18 limati: “Kunyada kumafikitsa munthu ku chiwonongeko, ndipo mtima wodzikuza umachititsa munthu kupunthwa.”

Koma bwanji ngati munthu wina wakuipitsirani mbiri? Kodi mudzachita zinthu mopupuluma, mwina mutakwiya kwambiri? Dzifunseni kuti, ‘Kodi mwina poyesa kuteteza mbiri yanga ndingakhale ndikufalitsa kwambiri mabodzawo?’ Ngakhale kuti nthawi zina n’zotheka kupita kukhoti, Baibulo limapereka malangizo akuti: “Usamapite kukazenga mlandu mofulumira,” m’malomwake “kambirana mlandu wako ndi mnzako.” (Miyambo 25:8, 9) * Kuchita zinthu moganiza bwino pa nkhaniyi kungathandize kuti musawononge ndalama zambiri zolipirira kukhoti.

Sikuti Baibulo langokhala buku la chipembedzo koma ndi buku la malangizo othandiza pa moyo. Anthu amene amagwiritsa ntchito nzeru za m’bukuli amalemekezedwa kwambiri ndipo izi zimachititsa kuti akhale ndi dzina labwino.

^ ndime 5 Mfundo zina za m’Baibulo zothandiza pa nkhani ya kuthetsa kusamvana zikupezeka pa Mateyu 5:23, 24; 18:15-17.