Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

GALAMUKANI! Na. 4 2017 | Kodi Inuyo Mumatanganidwa Kwambiri?

Masiku ano, anthu ambiri amakhala otanganidwa moti mpaka nthawi zina sacheza ndi anzawo ngakhalenso anthu a m’banja lawo.

Ndiye kodi tingatani kuti tizigwiritsa ntchito bwino nthawi yathu?

Munthu wina wanzeru analemba kuti: “Kupuma pang’ono kuli bwino kuposa kugwira ntchito mwakhama ndi kuthamangitsa mphepo.”—Mlaliki 4:6.

Galamukani! iyi ikufotokoza mfundo zimene zingatithandize kuti tizigwiritsa ntchito nthawi mwanzeru komanso kuika zinthu zofunika pamalo oyamba.

 

NKHANI YAPACHIKUTO

Kodi Inuyo Mumatanganidwa Kwambiri?

Anthu ambiri zimawavuta kuti azikwanitsa kugwira bwino ntchito yawo komanso kusamalira mabanja awo. Kodi n’chiyani chimachititsa zimenezi? Nanga tingatani kuti tithane ndi vutoli?

Mbalame ya Kunyanja Yochititsa Chidwi Kwambiri

Kwa nthawi yaitali anthu ambiri akhala akukhulupirira kuti mbalamezi zimauluka pafupifupi mtunda wa makilomita 35,200 chaka chilichonse pa ulendo wawo wochokera ku Arctic kupita ku Antarctica. Zimenezitu n’zodabwitsa kwambiri.

‘Kusankha Dzina Labwino Ndi Kwabwino Kusiyana ndi Chuma Chochuluka’

Tingathe kukhala ndi dzina labwino komanso anthu ena angamatilemekeze. Koma kodi zimenezi zingatheke bwanji?

MFUNDO ZOTHANDIZA MABANJA

Ana Akakula N’kuchoka Pakhomo

Okwatirana ena amakumana ndi mavuto aakulu ana awo akakula n’kuchoka pakhomo. Kodi makolo ayenera kuchita chiyani kuti azolowerenso kukhala okha?

KUCHEZA NDI ANTHU

Katswiri Woona za Ubongo Akufotokoza za Chikhulupiriro Chake

Pulofesa Rajesh Kalaria akufotokoza zambiri zokhudza ntchito yake komanso zimene amakhulupirira. Kodi n’chiyani chinamuchititsa kuti ayambe kuchita chidwi ndi sayansi? Nanga n’chiyani chinachititsa kuti ayambe kukayikira zimene ankakhulupirira zokhudza mmene moyo unayambira?

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

Mayesero

Mayesero angachititse kuti mabanja athe, angasokoneze thanzi la munthu komanso angachititse munthu kuvutika ndi chikumbumtima. Ndiye kodi tingapewe bwanji mayesero?

KODI ZINANGOCHITIKA ZOKHA?

Tizipatso Tokongola Kwambiri ta Buluu

Tizipatso ta Pollia tilibe madzi alionse a buluu mkati mwake, koma timaoneka ta buluu wowala kwambiri ndipo palibenso zomera zina zomwe zimaoneka choncho. Kodi n’chiyani chimachititsa kuti tizipatsoti tizioneka motere?

Zina zimene zili pawebusaiti

Kodi Baibulo Lingandithandize kuti Ndikhale ndi Banja Losangalala?

Malangizo anzeru ochokera m’Baibulo athandiza kale anthu mamiliyoni ambirimbiri kukhala ndi mabanja osangalala.

Monica Richardson: Dokotala Akufotokoza za Chikhulupiriro Chake

Akaona zimene zimachitika kuti mwana abadwe ankadzifunsa ngati zimangochitika zokha kapena ngati pali winawake amene anakonza kuti zizichitika choncho. Kodi pamapeto pake anapeza zotani pa ntchito yawo ngati dokotala?