Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

GALAMUKANI! Na. 3 2021 | Kodi Muyenera Kukhulupirira Kuti Kuli Mlengi?​—⁠Fufuzani

Anthu amakhala ndi maganizo osiyanasiyana pa nkhani ya mmene chilengedwe komanso moyo unayambira padzikoli. Magazini ya Galamukani! ino ikuthandizani kufufuza maumboni amene alipo pankhaniyi ndipo kenako muona kuti zolondola ndi ziti. Kodi chilengedwechi chinangokhalapo chokha kapena chinachita kulengedwa ndi Mlengi? Kudziwa yankho la funsoli kungakuthandizeni kwambiri.

 

Kodi Mungafufuze Bwanji?

Anthu akhala asakumvetsa mmene chilengedwe komanso moyo unayambira.

Zimene Zinthu Zakuthambo Zimatiuza

Zimaoneka kuti zinthu zakuthambo komanso dzikoli zinapangidwa m’njira yakuti padzikoli pazitha kukhala zamoyo. Kodi n’kutheka kuti zili choncho chifukwa zinachita kulengedwa ndi winawake?

Zimene Zamoyo Zimatiuza

Zamoyo zimakongoletsa dziko lathuli. Koma kodi zimatiuza chiyani zokhudza chiyambi chake?

Zimene Asayansi Sangatiuze

Kodi asayansi amafotokoza mmene chilengedwe komanso zamoyo zinayambira?

Zimene Baibulo Limatiuza

Kodi zomwe Baibulo limanena zimagwirizana ndi zimene asayansi apeza?

Chifukwa Chake Yankho la Funsoli Ndi Lofunika

Ngati mukukhutira ndi umboni wakuti kuli Mulungu yemwe ndi wamphamvuyonse, mukhoza kupeza madalitso panopa komanso m’tsogolo.

Fufuzani Umboni

Onani ngati pali zifukwa zomveka zimene zingakuchititseni kukhulupirira kuti kuli Mlengi.