Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Timitsempha totumiza mauthenga (tooneka ngati ulusi wa kangaude), tomwe timapezeka m’njira imene chakudya chimadutsa

Kodi Mumadziwa Kuti Tili ndi Mitsempha Ina Imene Imagwira Ntchito Ngati Ubongo?

Kodi Mumadziwa Kuti Tili ndi Mitsempha Ina Imene Imagwira Ntchito Ngati Ubongo?

KODI anthufe tili ndi ubongo ungati? Ngati mwayankha kuti “umodzi,” simunalakwitse. Komabe, m’thupi mwathu mulinso timitsempha tina timene timatumiza ndi kulandira mauthenga. Timitsemphati timagwira ntchito mogometsa kwambiri moti asayansi ena amatitchulanso kuti “ubongo wachiwiri.” Timitsempha timeneti timapezeka m’mimba mwathu.

Kuti thupi lathu lizitha kugaya chakudya chomwe chimathandiza kuti tipeze mphamvu, pamafunika kuti ziwalo zosiyanasiyana za m’thupi lathuli zizigwira ntchito mogwirizana. Choncho m’malo moti ubongo wathu uzigwira ntchito yotumiza mauthenga m’njira imene chakudya chimadutsa, timitsempha tam’mimba ndi timene timagwira ntchito imeneyi.

Ngakhale kuti timitsemphati sitigwira ntchito ndendende ngati ubongo, komabe timagwira ntchito mogometsa kwambiri. M’mimba mwa munthu mumakhala timitsempha ta mtunduwu tokwana pafupifupi 200 kapena 600 miliyoni. Timitsemphati timapezeka m’njira imene chakudya chimadutsa. Akatswiri a sayansi amaona kuti zikanakhala kuti ntchito zonse zotumizira mauthenga zimachitikira muubongo, mitsempha ya mauthenga ikanakhala ikuluikulu kwambiri. Buku lina linanena kuti: “Zinakhala bwino kuti timitsempha ta mauthenga tomwe timapezeka m’njira ya chakudya tizigwira ntchito patokha.”​—The Second Brain.

M’MIMBA MWATHU MULI NGATI FAKITALE

Thupi lathu limatulutsa timadzi tosiyanasiyana tomwe timathandiza pogaya chakudya. Limatulutsa timadziti pa nthawi yoyenera n’kutipitsa pamene tikufunika. Pulofesa wina dzina lake Gary Mawe ananena kuti njira imene chakudya chimadutsa kuti chigayike imagwira ntchito ngati fakitale. Ndi zochititsa chidwi kwambiri tikaganizira zimene zimachitika kuti chakudya chigayike komanso mmene timadzi tosiyanasiyana timene thupi limatulutsa timagwirira ntchito pogaya chakudyacho. Mwachitsanzo, m’matumbo mwathu muli maselo amene amatha kudziwa zinthu zimene zili mu chakudya chimene tadya. Ndiyeno timitsempha totumiza mauthenga tija tikadziwa zimene zili mu chakudyacho pogwiritsa ntchito maselowa, timachititsa kuti thupi litulutse timadzi toyenera tothandiza kugaya zinthuzo. Timitsempha totumiza mauthenga timaonetsetsanso kuti thupi likutulutsa timadzi togwirizana ndi kuchuluka kwa zinthu zimene zikupezeka m’chakudyacho.

Timitsempha ta m’mimba ndi timene timayendetsa zonse zimene zimachitika m’njira imene chakudya chimadutsa kuti chigayike. Timitsemphati timayendetsa chakudya pochititsa kuti njira yachakudya izifinyika. Timaonetsetsanso kuti pakufunika mphamvu zochuluka bwanji kuti njira ya chakudyayo ifinyike.

Timitsempha totumiza mauthengati timagwiranso ntchito yoteteza thupi. Nthawi zambiri chakudya chimene timadya, chimakhala ndi tizilombo toyambitsa matenda. Chifukwa cha zimenezi asilikali ambiri oteteza thupi ku matenda amakhala m’mimba. Mukadya chakudya chowonongeka, timitsempha totumiza mauthenga timachititsa kuti njira ya chakudya ifinyike kwambiri. Zimenezi zimachititsa kuti musanze kapena kutsegula m’mimba kuti muchotse tizilombo toipa.

 TIMITSEMPHATI TIMATUMIZIRANA MAUTHENGA NDI UBONGO

Ngakhale kuti timitsempha tam’mimbati timatha kugwira ntchito patokha, timatumizirana mauthenga ndi ubongo. Mwachitsanzo, timachititsa thupi kutulutsa timadzi tomwe timathandiza ubongo kudziwa nthawi yomwe muyenera kudya komanso kuti muyenera kudya chakudya chochuluka bwanji. Timatumizanso uthenga kuubongo wokudziwitsani ngati mwakhuta kapena kukuchititsani mseru ngati mwadya kwambiri.

N’kutheka kuti mumadziwa kale kuti pamakhala kulumikizana pakati pa ubongo wanu ndi njira ya chakudya. Mwina munaonapo kuti nthawi zina mukadya chakudya chamafuta, mumamvako bwino ngakhale kuti munali wokhumudwa. Ochita kafukufuku anapeza kuti zimenezi zimachitika chifukwa chakuti timitsempha tija timakhala titatumiza uthenga kuubongo woti mukhale wosangalala. Mwinatu n’chifukwa chake anthu ambiri akakhumudwa amakonda kudya zakudya zanoninoni. Asayansi akufuna kupeza njira ina yothandizira anthu amene ali ndi matenda ovutika maganizo. Akufuna kuti njirayi izichititsa timitsemphati kutumiza mauthenga kuubongo opangitsa munthu amene ali ndi vutoli kukhala wosangalala.

Umboni wina wosonyeza kuti pamakhala kulumikizana pakati pa mitsempha ya m’mimba ndi ubongo, m’pamene munthu amabwadamuka m’mimba akakhala ndi nkhawa. Zikuoneka kuti zimenezi zimachitika timitsemphati tikachititsa kuti magazi a m’mimba asinthe kumene akulowera. Nthawi zinanso munthu akakhala ndi nkhawa amachita mseru. Pa nthawiyi ubongo umachititsa kuti timitsempha tam’mimba tija tisinthe mmene njira ya chakudya imagwirira ntchito.

Ngakhale kuti timitsempha tam’mimbati timatha kuchita zonsezi, sitingakuthandizeni kuganiza kapenanso kusankha zoti muchite. Tikutero chifukwa chakuti timitsemphati si ubongo ndipo sitingakuthandizeni kupeka nyimbo, kuwerengera ndalama kapena kulemba homuweki. Komabe, asayansi sanafike pomvetsa mmene timitsemphati timagwirira ntchito moti mpaka pano adakafufuzabe. Bwanji ulendo wina mukamadzadya chakudya, mudzaganizire kaye zinthu zosiyanasiyana zimene timitsempha totumiza mauthengati timachita.