Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Zinangochitika Zokha?

Khosi la Nyerere

Khosi la Nyerere

AKATSWIRI ambiri amadabwa ndi mmene nyerere zimanyamulira zinthu zolemera. Pofuna kumvetsa mmene nyererezi zimachitira zimenezi, akatswiri ena apayunivesite ya Ohio, ku United States anapanga maloboti oti azitha kuchita zinthu ngati nyerere zenizeni. Kuti athe kupanga malobotiwa anajambula nyerere yeniyeni pogwiritsa ntchito makina ounika mkati mwa chinthu, kuti aone zomwe zimathandiza nyerere kunyamula zinthu zolemera.

Nyerere imatha kunyamula zinthu zolemera pogwiritsa ntchito kukamwa kwake chifukwa cha mmene khosi lake linapangidwira. Mkati mwa khosi la nyerere muli minyewa yomwe imalumikiza thupi ndi mutu wake ngati mmene zimaonekera mukaluka pamodzi zala za dzanja lamanja ndi lamanzere. Munthu wina wochita kafukufuku ananena kuti: “Kalumikizidweka n’kamene kamathandiza kwambiri kuti khosi la nyerere lizitha kunyamula zinthu zolemera. Zikuoneka kuti kulumikizana kwa minyewa yofewa ndi thupi lomwe ndi lolimba n’kumene kumachititsa kuti khosili likhale lolimba n’kumatha kukoka kapena kunyamula zinthu zolemera.” Anthu ambiri ochita kafukufuku amanena kuti kumvetsa bwino mmene khosi la nyerere limagwirira ntchito kungathandize akatswiri kupanga makina omwe angathe kuchita zinthu ngati nyerere.

Kodi inuyo mukuganiza bwanji? Kodi zinangochitika zokha kuti khosi la nyerere lilumikizane modabwitsa chonchili? Kapena pali winawake amene analipanga?