Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YA PACHIKUTO | A MBONI ZA YEHOVA AKUMASULIRA M’ZINENERO ZAMBIRI

Ntchito Yomasulira Yathetsa Vuto la Kusiyana Zinenero

Ntchito Yomasulira Yathetsa Vuto la Kusiyana Zinenero

PADZIKO lapansi pali zinenero pafupifupi 7,000. Zimenezi zimapangitsa kuti anthu azivutika kumvana pa nkhani zokhudza maulendo, maphunziro, malonda ndi maboma. Ndipotu mavuto amenewa anayamba kalekale. Mwachitsanzo, cha m’ma 475 B.C.E., mu ulamuliro wa Mfumu Ahasiwero (yemwe mwina anali Sasta 1), Aperisi anapereka makalata ochokera kwa mfumu, kuyambira “ku Indiya kukafika ku Itiyopiya, zigawo 127.” Ndipo chifukwa cha kusiyana kwa zinenero, “chigawo chilichonse anachilembera makalata amenewa malinga ndi mmene anthu a m’chigawocho anali kulembera ndiponso m’chinenero chawo.” *

Masiku ano, maboma ambiri kapenanso mabungwe sayesa n’komwe kugwira ntchito yovutayi. Komabe pali gulu limodzi lokha limene lakwanitsa kuchita zimenezi. A Mboni za Yehova amafalitsa magazini, mabuku, Baibulo ngakhalenso mavidiyo ndi zinthu zina zongomvetsera, m’zinenero zoposa 750. Amamasuliranso zinthu zimenezi m’zinenero zamanja pafupifupi 80. Ndiponso amasindikiza mabuku ambiri a zilembo za anthu amene ali ndi vuto losaona.

A Mboni za Yehova sagwira ntchitoyi n’cholinga choti apeze ndalama. Komanso amene amagwira ntchito yomasulirayi ndi ongodzipereka. Kodi n’chifukwa chiyani amagwira ntchitoyi modzipereka chonchi, nanga amaigwira bwanji?

^ ndime 3 Onani lemba la Esitere 8:9.