Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YA PACHIKUTO

A Mboni za Yehova Akumasulira M’zinenero Zambiri—Zimene Zimachitika Pomasulira

A Mboni za Yehova Akumasulira M’zinenero Zambiri—Zimene Zimachitika Pomasulira

“Nthawi zina anthu amanena kuti palibenso ntchito yovuta kuposa yomasulira mabuku.”—“The Cambridge Encyclopedia of Language.”

NTCHITO yomasulira mabuku a Mboni za Yehova imayambira patali. Mwachitsanzo, amafunika kuchita zinthu mosamala kwambiri pokonza, kufufuza komanso kulemba nkhani za m’mabukuwo. Pa nthawiyi Dipatimenti Yolemba, yomwe ili kulikulu la Mboni za Yehova padziko lonse ku New York, imaonetsetsa kuti mfundo zomwe zalembedwa n’zolondola komanso kuti zalembedwa momveka bwino. *

Kenako dipatimentiyi imatumiza nkhanizi kwa omasulira omwe ali m’mayiko osiyanasiyana, kuti akazimasulire. Omasulira ambiri amakhala m’madera omwe chinenero chomwe akumasuliracho chimayankhulidwa. Ndipotu ambiri amamasulira m’zinenero zobadwira. Iwo amafunika kudziwa bwino Chingelezi komanso chinenero chomwe akumasuliracho.

Kodi omasulira amagwira bwanji ntchito yawo?

Geraint, yemwe amagwira ntchito yomasulira ku Britain akufotokoza kuti: “Pogwira ntchitoyi sindikhala ndekha, timakhala anthu atatu. Choncho timafunika kuchita zinthu mogwirizana kuti ntchitoyi iyende bwino. Timathandizana kupeza njira zothetsera mavuto omwe timakumana nawo pomasulira. Ndipo tikamamasulira, sitimangoganizira liwu lililonse palokha koma chiganizo chonse. Timaganiziranso kwambiri tanthauzo, cholinga komanso anthu amene awalembera nkhaniyo.”

Kodi pogwira ntchitoyi mumakhala ndi cholinga chotani?

“Timafuna kuti anthu akamawerenga mabuku athu aziona ngati analembedwa m’chinenero chawo. Sitifuna kuti azichita kudziwiratu kuti tinachita kumasulira. Ndiye kuti zimenezi zitheke timayesetsa kugwiritsa ntchito mawu omveka bwino a m’chinenero chathu. Zimenezi zimachititsa kuti anthu azilakalaka kuwerenga nkhaniyo n’kuimaliza ngati mmene zimakhalira munthu akamadya chakudya chopatsa mudyo.”

Kodi kukhala komwe chinenero chimayankhulidwa kuli ndi ubwino wotani?

“Kukhala limodzi ndi anthu oyankhula chinenero chomwe tikumasulira, kumatithandiza kuti tizimasulira zomveka bwino chifukwa tsiku lililonse timamva mmene amayankhulira. Timathanso kuchita kafukufuku pa mawu enaake kuti tione ngati anthu akuwagwiritsa ntchito komanso akuwamvetsa. Zimenezi zimathandiza kuti nkhani yathu ikhale yomveka bwino ngati mmene ilili yachingelezi.”

Kodi mumagwira bwanji ntchitoyi?

“Ntchito iliyonse imaperekedwa kwa anthu atatu. Tisanayambe kumasulira, aliyense amayamba wakonzekera nkhaniyo n’cholinga choti aimvetse bwino, adziwe amene awalembera nkhaniyo komanso mmene mfundo zake zasanjidwira. Timadzifunsa kuti: ‘Kodi nkhaniyi ikutiphunzitsa chiyani? Kodi cholinga chake ndi chiyani, nanga mfundo yaikulu ndi iti?’ Kuchita zimenezi kumatithandiza kuti tiganizire njira zosiyanasiyana zomwe tingazigwiritse ntchito pomasulira.

“Kenako timakambirana zimene tapeza komanso mavuto amene takumana nawo pokonzekera. Pa nthawiyi m’pamene timatsimikizira kuti nkhaniyo taimvetsadi. Timakambirananso mmene tingasanjire mfundo zathu kuti zikhale zothyakuka bwino ngati mmene zilili zachingelezi. Timafuna kuti nkhani yomwe tamasulira izikafika pamtima anthu mofanana ndi amene akawerenge nkhaniyo m’Chingelezi.”

Ndiye zimatheka bwanji anthu atatu kumagwira ntchito limodzi bwinobwino?

“Timafuna kuti anthu akangowerenga nkhani ulendo woyamba, amve uthenga wake nthawi yomweyo. Kuti zimenezi zitheke, tikangomaliza kumasulira ndime iliyonse timaiwerenga mokweza maulendo angapo.

“Pa nthawi yomasulira, wina amalemba ziganizo m’chinenero chomwe tikumasuliracho pakompyuta ndipo enafe timaona zomwe akulembazo pamasikilini a makompyuta athu. Ndipo timaonetsetsa kuti sitinawonjezere kapena kuchotsera mfundo zina. Timaonetsetsanso kuti ziganizo zalembedwa molondola, mmene anthu amayankhulira komanso motsatira malamulo am’kalembedwe. Zikatere, wina amawerenga ndime yonse mokweza. Ndiyeno ngati powerengapo akuvutika, timaganizira zimene zikuchititsa vutolo, n’kukonzeratu. Pamapeto pake, mmodzi amawerenga nkhani yonse yomwe tamasulirayo ndipo enafe timamvetsera mwatcheru kuti tione zina zomwe tingakonze.”

Zikuoneka kuti imakhalapotu!

“Zoonadi, ndipo tikamaweruka timakhala titatopa kwambiri. Koma tsiku lotsatira timadzawerenganso nkhaniyo chifukwa timakhala titapuma. Ndiyeno pakadutsa milungu ingapo, Dipatimenti Yolemba imatitumiziranso nkhani yachingelezi ija, koma yokhala ndi zinthu zomwe zasintha. Zikatere, nafenso timakonza nkhani yomwe tamasulirayo, kenako timaiwerenganso mosamala.”

Nanga ndi mapulogalamu ati apakompyuta omwe mumagwiritsa ntchito?

“Makompyuta amatithandizadi, koma paokha sangachite zonse zomwe munthu akufuna. Choncho a Mboni za Yehova anapanga mapulogalamu a pakompyuta omwe amatithandiza kuti tisamavutike kwambiri tikamamasulira. Mwachitsanzo, anakonza dikishonale ina yomwe timasungamo mawu omwe timawagwiritsa ntchito kawirikawiri. Palinso pulogalamu ina imene imatithandiza kufufuza chilichonse chimene anzathu anamasulira kale m’chinenero chathu komanso kuona mmene anamasulira mawu enaake ovuta.”

Inuyo mumamva bwanji mukamagwira ntchito yomasulira?

“Timaona kuti mabuku omwe timamasulira ndi mphatso yopita kwa anthu ambiri. Choncho tikamamasulira timaonetsetsa kuti nkhanizo zizikhala zokoma kuwerenga, kuti anthu azikasangalala nazo komanso zikawathandize. Timasangalala kwambiri tikaona kuti nkhani inayake ya m’magazini kapena pawebusaiti yathu yathandiza munthu kusintha moyo wake.”

Ntchitoyi ili ndi phindu losaneneka

Mabuku a Mboni za Yehova akuthandiza anthu mamiliyoni ambiri padziko lonse chifukwa amawawerenga m’zinenero zawo. Mfundo zomwe zimapezeka m’mabuku, mavidiyo komanso m’nkhani zapawebusaiti ya jw.org, zimachokera m’Baibulo. Ndipotu Mulungu yemwe dzina lake ndi Yehova ananena m’buku lopatulikali kuti uthenga wake tiziulengeza kwa anthu a “fuko lililonse, chinenero chilichonse, ndi mtundu uliwonse.”—Chivumbulutso 14:6. *

^ ndime 4 Nkhani zonse zimalembedwa m’Chingelezi.

^ ndime 25 Pitani pawebusaiti ya www.jw.org kuti mupeze mabuku, mavidiyo ndi zinthu zina zongomvetsera m’chinenero chanu komanso m’zinenero zina zambiri.