Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

Chikhulupiriro

Chikhulupiriro

Anthu ena omwe amati ndi opemphera sadziwa kuti “chikhulupiriro” chimatanthauza chiyani. Ndiyeno kodi chikhulupiriro n’chiyani, nanga n’chofunika bwanji?

Kodi chikhulupiriro n’chiyani?

ZIMENE ANTHU ENA AMANENA

Anthu ambiri amaganiza kuti munthu yemwe ali ndi chikhulupiriro amangokhulupirira chilichonse popanda umboni wokwanira. Mwachitsanzo, anthu ena opemphera anganene kuti amakhulupirira Mulungu. Koma atati afunsidwe chifukwa chimene amakhulupirira Mulungu angayankhe kuti ndi zomwe anaphunzitsidwa kuyambira ali aang’ono kapenanso kuti n’zimene akhala akumva. Izi zikusonyeza kuti kukhala ndi chikhulupiriro n’kosiyana ndi kungokhulupirira zinthu zopanda umboni.

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

“Chikhulupiriro ndicho chiyembekezo chotsimikizika cha zinthu zoyembekezeredwa, umboni wooneka wa zinthu zenizeni, ngakhale kuti n’zosaoneka.” (Aheberi 11:1) Munthu yemwe akuyembekezera zinazake ayenera kukhala ndi zifukwa zokwanira zosonyeza kuti zomwe akuyembekezerazo zidzachitikadi. Mawu achigiriki omwe anawamasulira kuti “chiyembekezo chotsimikizika” amatanthauza zinthu zambiri osati kungokhala ndi maganizo ofuna zinthu zabwino kapena kuyembekezera zinthu zosatheka. Choncho munthu amene ali ndi chikhulupiriro amakhala ndi umboni wokwanira wa zinthu zomwe akuyembekezerazo.

“Makhalidwe a Mulungu osaoneka ndi maso akuonekera bwino. Makhalidwe a Mulungu amenewa, ngakhalenso mphamvu zake zosatha ndiponso Umulungu wake, zikuonekera m’zinthu zimene anapanga.”—Aroma 1:20.

Kodi kukhala ndi chikhulupiriro n’kofunika bwanji?

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

“Popanda chikhulupiriro n’zosatheka kukondweretsa Mulungu. Pakuti aliyense wofika kwa Mulungu ayenera kukhulupirira kuti iye alikodi, ndi kuti amapereka mphoto kwa anthu omufunafuna ndi mtima wonse.”—Aheberi 11:6.

Monga tanenera kale, anthu ambiri amakhulupirira Mulungu chifukwa choti ndi zimene anaphunzitsidwa basi. Mwachitsanzo, ena amanena kuti ndi zomwe anaphunzitsidwa kuyambira ali aang’ono. Koma Mulungu amafuna kuti amene amamulambira azikhulupirira kuti iye alikodi komanso kuti amawakonda. N’chifukwa chake Baibulo limatilimbikitsa kuti tizifunafuna Mulungu mwakhama n’cholinga choti timudziwe bwino.

“Yandikirani Mulungu, ndipo iyenso adzakuyandikirani.”Yakobo 4:8.

Kodi mungatani kuti mukhale ndi chikhulupiriro?

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

Baibulo limanena kuti: “Munthu amakhala ndi chikhulupiriro chifukwa cha zimene wamva.” (Aroma 10:17) Choncho kuti munthu akhale ndi chikhulupiriro, ayenera ‘kumva’ zimene Baibulo limaphunzitsa zokhudza Mulungu. (2 Timoteyo 3:16) Kuphunzira Baibulo kungakuthandizeni kupeza mayankho a mafunso ofunika kwambiri monga akuti: Kodi Mulungu ndi ndani? Kodi pali umboni wotani wosonyeza kuti alikodi? Kodi Mulungu amatiganiziradi? Kodi Mulungu amafuna kuti moyo udzakhale wotani m’tsogolo?

Pali maumboni ambiri osonyeza kuti Mulungu alipo

A Mboni za Yehova angakuthandizeni kudziwa zimene Baibulo limaphunzitsa. Komabe monga momwe timanenera pawebusaiti yathu ya jw.org, “Timasangalala kuphunzitsa anthu Baibulo, koma sitiwakakamiza kuti alowe chipembedzo chathu. M’malomwake, timawafotokozera mwaulemu zimene Baibulo limanena, ndipo timazindikira kuti munthu aliyense ali ndi ufulu wosankha zimene akufuna kuti azikhulupirira.”

Komanso kuti munthu akhale ndi chikhulupiriro ayenera kuwerenga Baibulo ndiponso kutsimikizira payekha kuti zimene akuwerengazo ndi zoona. Mukamachita zimenezi, mudzafanana ndi anthu ena amene ankaphunzira za Mulungu m’nthawi ya atumwi. Anthuwo “analandira mawu a Mulungu ndi chidwi chachikulu kwambiri, ndipo tsiku ndi tsiku anali kufufuza Malemba mosamala kuti atsimikizire ngati zimene anamvazo zinalidi zoona.”—Machitidwe 17:11.

“Pakuti moyo wosatha adzaupeza akamaphunzira ndi kudziwa za inu, Mulungu yekhayo amene ali woona, ndi za Yesu Khristu, amene inu munamutuma.”Yohane 17:3.