Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Zimene Zimachitika Ana Akakhala ndi Chisoni

Zimene Zimachitika Ana Akakhala ndi Chisoni

Kodi muli ndi chisoni chifukwa chakuti winawake m’banja mwanu anamwalira? Ngati ndi choncho, kodi mungapirire bwanji vutoli? Nkhaniyi ikufotokoza mmene mfundo za m’Baibulo zinathandizira achinyamata atatu, pa nthawi imene anali ndi chisoni.

ZIMENE DAMI ANANENA

Dami

Bambo atayamba kumva kupweteka mutu, tinkangoona ngati ndi mmene zimakhalira nthawi zonse. Koma zitafika poipa kwambiri, mayi anaitanitsa ambulansi. Ndimakumbukirabe madokotala atabwera kudzawatenga n’kupita nawo kuchipatala. Pa nthawiyi sindinkadziwa kuti kameneka kakhala komaliza kuwaona. Patangotha masiku atatu, bambo anga anamwalira ndi matenda otupa mitsempha. Zimenezi zinachitika ndili ndi zaka 6 zokha.

Kwa zaka zambiri ndinkadziimba mlandu ndikaganizira imfa ya bambo anga. Ndikakumbukira zimene zinachitika pa nthawi imene madokotala anabwera kudzawatenga, ndinkadzifunsa kuti: “Chifukwa chiyani ndinangoima n’kumangoyang’ana osachitapo chilichonse?” Ndikaona anthu ena achikulire omwe akudwala, ndinkadzifunsa kuti, ‘Nanga bwanji bambo anga anamwalira koma anzawowa adakali moyo?’ Patapita nthawi, mayi anga anandithandiza kuti ndiziwauza zamumtima mwanga. Komanso a Mboni za Yehova anzathu ankatilimbikitsa.

Anthu ena amaganiza kuti utha kukhala ndi chisoni pa nthawi yamaliroyo koma nthawi ikamapita chisonicho chimatha. Koma si zimene zinandichitikira. Ndinamvadi chisoni pa nthawi ya maliroyo koma nditafika zaka 13 kapena 14, m’pamene ndinkamva chisoni kwambiri.

Ndingakonde kulangiza achinyamata ena omwe bambo kapena mayi awo anamwalira kuti: “Muzifotokozera munthu wina mmene mukumvera. Ngati mutayamba mwamsanga kuchita zimenezi, zidzakuthandizani kuti musadzavutike ndi chisoni kwa nthawi yaitali.”

Ndikachita zinthu zina zapadera pa moyo wanga, zimandikhudza kwambiri ndikaganizira kuti bambo anga sanakhalepo. Koma ndimalimbikitsidwa ndi lemba la Chivumbulutso 21:4 lomwe limanena kuti posachedwa Mulungu “adzapukuta misozi yonse m’maso [mwathu], ndipo imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulira, kapena kubuula, ngakhale kupweteka.”

ZIMENE DERRICK ANANENA

Derrick

Ndimakumbukirabe titapita kukawedza nsomba komanso kukayenda kumapiri ndi bambo anga. Bambo ankakonda kwambiri mapiri.

Bambo anga anavutika ndi matenda a mtima kwa nthawi yaitali. Ndimakumbukira ndili wamng’ono kuti ndinakawaonapo kuchipatala kamodzi kapenanso kawiri. Koma pa nthawiyo sindinkadziwa kukula kwa vuto lawo. Bambo anamwalira ndi matendawo ndili ndi zaka 9.

Atangomwalira ndinalira kwambiri. Ndinkamva ngati mphamvu zandithera ndipo sindinafune kuti ndilankhulenso ndi aliyense. Imeneyi inali nthawi yovuta kwambiri pa moyo wanga ndipo ndinkaona kuti palibenso zomwe ndikanachita. Ndinali m’gulu la achinyamata kutchalitchi kwathu ndipo anzangawa anangondilimbikitsa masiku oyambirira okha koma kenako basi anasiya. Anthu a kutchalitchi kwathu ankandiuza kuti: “Nthawi ya bambo ako inali itakwana” kapena “Mulungu anawatenga” kapenanso kuti “Panopa ali kumwamba.” Zomwe ankandiuzazi sizimandikhutiritsa ngakhale kuti sindinkadziwa kuti Baibulo limaphunzitsa zotani pa nkhani ya imfa.

Kenako mayi anga anayamba kuphunzira Baibulo ndi a Mboni za Yehova ndipo patapita nthawi, ineyo ndi mchimwene wanga tinayambanso kuphunzira. Tinaphunzira zimene zimachitika munthu akamwalira komanso zoti Mulungu analonjeza kuti akufa adzauka. (Yohane 5:28, 29) Lemba la Yesaya 41:10 ndi limene linandilimbikitsa kwambiri. Palembali Mulungu ananena kuti: “Usachite mantha, pakuti ndili nawe. Usayang’ane uku ndi uku mwamantha, pakuti ine ndine Mulungu wako. Ndikulimbitsa. Ndithu ndikuthandiza.”

ZIMENE JEANNIE ANANENA

Jeannie

Ndili ndi zaka 7, mayi anga anamwalira ndi khansa. Tsiku limenelo ndinkangoona ngati ndikulota. Ndimakumbukira kuti anamwalirira kunyumba ndipo pa nthawiyo agogo anga aakazi komanso aamuna analinso kunyumbako. Tsiku limenelo aliyense anangokhala phee. Ndimakumbukiranso kuti madzulo a tsikulo tinadyera mazira. Ndinasokonezeka kwambiri moti ndinkangoona kuti chilichonse pa moyo wanga chasinthiratu.

Kuyambira nthawi imeneyo, ndinkangoona kuti ndikungofunika kukhala wolimba mtima n’kumasamalira mng’ono wanga. Koma tsopano vuto linali loti ndinayamba kubisa mmene ndinkamvera mumtima. Mpaka pano zimandivutabe kusonyeza mmene zinthu zikundikhudzira. Koma ndimadziwa kuti zimenezi zikhoza kundibweretsera mavuto ena.

Ndimakumbukira zimene a Mboni za Yehova anzathu anachita potilimbikitsa. Ngakhale kuti tinali titangoyamba kumene kusonkhana nawo pa Nyumba ya Ufumu, Akhristuwa ankachita nafe zinthu ngati kuti tinadziwana nawo kalekale. Sindikukumbukira ngati bambo anaphika chakudya chamadzulo chaka chimenecho chifukwa madzulo alionse Akhristu anzathu ankatibweretsera chakudya.

Lemba lomwe limandilimbikitsa kwambiri ndi la Salimo 25:16, 17. Palembali wamasalimo anapempha Mulungu kuti: “Ndicheukireni ndi kundikomera mtima. Pakuti ndasungulumwa ndipo ndasautsika. Masautso a mtima wanga awonjezeka. Ndilanditseni ku nkhawa zimene zili pa ine.” Zimandilimbikitsa kudziwa kuti ukakhala ndi chisoni sukhala wekha koma Mulungu amakuthandiza. Mfundo za m’Baibulo zimandithandiza kuti ndiziyang’ana kutsogolo n’kumayembekezera nthawi imene akufa adzauka. Ndikuyembekezera kudzaonanso mayi anga ali a thanzi komanso angwiro m’paradaiso padzikoli.2 Petulo 3:13.

Kodi mukufuna kuwerenga nkhani zina za m’Baibulo zolimbikitsa anthu omwe ali ndi chisoni? Pangani dawunilodi kabuku kakuti “Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira” pa www.jw.org/ny, ndipo tsegulani pomwe alemba kuti MABUKU › MABUKU.