Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mu mzinda wa Toledo muli zinthu za mbiri yakale komanso zinthu zambiri za chikhalidwe cha anthu a ku Spain. M’chaka cha 1986, mzindawu unasankhidwa kukhala mzinda wapadera padziko lonse wosunga zinthu zachikhalidwe ndipo kumapita alendo ambiri

ANTHU NDI MAYIKO

Dziko la Spain

Dziko la Spain

DZIKO la Spain lili kum’mwera chakumadzulo kwa Europe ndipo kuli mitundu yambiri ya anthu komanso zinthu zachilengedwe zosiyanasiyana zochititsa chidwi. Mbali yaikulu ya dziko la Spain kuli minda ya tirigu, ya mpesa komanso mitengo ya maolivi. Kum’mwera kwa dziko la Spain kuli nyanja yomwe imasiyanitsa dziko la Spain ndi ku Africa ndipo mtunda wake ndi wokwana pafupifupi makilomita 14 okha basi.

Kalelo, anthu ambiri ochokera ku chigawo cha Foinike, ku Girisi komanso ku Carthage, anasamukira m’dzikoli. Aroma atalanda dzikoli cha m’ma 200 B.C.E., anatchula dzikoli kuti Hispania. Patapita nthawi anthu a mtundu wa Visigoti ndi wa Moor, anasiya mayiko ndi chikhalidwe chawo n’kudzakhazikika m’dzikoli.

M’chaka china chaposachedwapa, dziko la Spain linalandira alendo oposa 68 miliyoni odzaona malo. Alendo ambiri amafika m’dzikoli kudzawothera dzuwa, kudzaona nyanja komanso kudzaona zinthu za mbiri yakale. Alendo ambiri amakondanso zakudya za ku Spain monga nsomba ndi zinthu zina zokhala m’madzi, nyama, saladi komanso masamba ophika kapena othira mafuta a maolivi. Anthu ochokera m’mayiko ambiri amakonda zakudya monga Spanish omelets, paella ndiponso tapas.

Chakudya chodziwika kwambiri ku Spain chotchedwa Mariscada

Gule wa flamenco

Anthu a ku Spain ndi ansangala kwambiri komanso amakonda kucheza. Ambiri m’dzikoli ndi Akatolika, koma ndi anthu ochepa kwambiri amene amachita nawo mwambo wa Misa. M’zaka zaposachedwapa anthu ochokera ku Africa, Asia komanso ku Latin America akhala akupita ku dziko la Spain. Ambiri mwa anthuwa amakonda kukambirana ndi ena nkhani zachipembedzo. Zimenezi zathandiza kwambiri a Mboni za Yehova kuti azitha kukambirana nawo uthenga wa m’Baibulo komanso kuwathandiza kudziwa zimene Baibulo limaphunzitsa pa nkhani zosiyanasiyana.

Mu 2015, a Mboni oposa 10,500 anadzipereka kumanga kapena kukonzanso nyumba 70 zomwe amachitiramo misonkhano yawo, zotchedwa Nyumba za Ufumu. Akuluakulu a mizinda anapereka malo kwa a Mboniwa kuti amangepo nyumbazo. Pofuna kuthandiza anthu a m’mayiko ena, a Mboni za Yehova amachita misonkhano yawo m’zinenero zoposa 30 kuwonjezera pa Chisipanishi. Mu 2016, anthu oposa 186,000 anapezeka pamwambo wapadera wa Mboni za Yehova wokumbukira imfa ya Yesu Khristu.