Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafilimu amasonyeza kuti kukhulupirira zamizimu n’kosangalatsa, koma tiyenera kudziwa kuopsa kwake ndipo tiyenera kukhala osamala

NKHANI YA PACHIKUTO | KODI NDI BWINO KUKHULUPIRIRA ZAMATSENGA?

Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani pa Nkhani ya Kukhulupirira Zamizimu?

Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani pa Nkhani ya Kukhulupirira Zamizimu?

ANTHU ambiri amaona kuti palibe vuto ndi kukhulupirira kapena kuchita zamizimu. Amaona kuti zimene mafilimu ndi mabuku amasonyeza pa nkhani zamizimu, zimangokhala luso la opanga mafilimuwo kapena olemba nkhanizo. Komabe Baibulo limafotokoza zosiyana ndi zimene ambiri amaganiza. Limafotokoza mosapita m’mbali za kuopsa kokhulupirira zamizimu. Mwachitsanzo lemba la Deuteronomo 18:10-13 limati: “Pakati panu pasapezeke . . . wochita zamatsenga, woombeza, wanyanga, kapena wolodza ena, aliyense wofunsira kwa wolankhula ndi mizimu, wolosera zam’tsogolo kapena aliyense wofunsira kwa akufa.” N’chifukwa chiyani Baibulo limanena zimenezi? Lembali limapitiriza kunena kuti: “Pakuti aliyense wochita zimenezi ndi wonyansa kwa Yehova . . . Ukhale wopanda cholakwa pamaso pa Yehova Mulungu wako.”

N’chifukwa chiyani Baibulo limaletsa mwamphamvu kuchita zamizimu zamtundu uliwonse?

KODI KUKHULUPIRIRA ZAMIZIMU KUNAYAMBA BWANJI?

Baibulo limanena kuti kalekale Mulungu asanalenge dziko lapansi, analenga zamoyo zauzimu kapena kuti angelo. (Yobu 38:4, 7; Chivumbulutso 5:11) Yehova analenga mngelo aliyense ndi ufulu wosankha chabwino kapena choipa. Koma angelo ena anasankha kupandukira Mulungu ndipo anasiya malo awo kumwamba n’kudzayambitsa mavuto padzikoli. Patapita nthawi, dzikoli “linadzaza ndi chiwawa.”Genesis 6:2-5, 11; Yuda 6.

Baibulo limanena kuti angelo oipawo kapena kuti ziwanda zinayamba kusocheretsa anthu ambiri. (Chivumbulutso 12:9) Ziwandazi zinachititsanso kuti anthu azifuna kudziwa zam’tsogolo.1 Samueli 28:5, 7; 1 Timoteyo 4:1.

N’zoona kuti nthawi zina ziwanda zimaoneka ngati zimathandiza anthu. (2 Akorinto 11:14) Koma cholinga chachikulu cha ziwanda chimakhala kuchititsa anthu khungu kuti asadziwe choonadi chokhudza Mulungu.2 Akorinto 4:4.

Choncho malinga ndi zimene Baibulo limanena, kuchita zinthu zogwirizana ndi ziwanda n’koopsa kwambiri. N’chifukwa chake anthu amene ankafuna kukhala ophunzira a Yesu atadziwa za kuopsa kokhulupirira zamizimu, “anasonkhanitsa mabuku awo pamodzi ndi kuwatentha,” ngakhale kuti anali a ndalama zambiri.Machitidwe 19:19.

Kafukufuku wina wa nkhani za achinyamata womwe bungwe la Gallup linachita mu 2014, anasonyeza kuti atsikana ambiri amene amakonda nkhani zaufiti, amatero chifukwa chokopeka ndi anthu okongola ochita zamatsenga amene amaonetsedwa pa TV, m’mafilimu komanso chifukwa cha zomwe amawerenga m’mabuku.

Masiku anonso, anthu ambiri asiya kuchita zamizimu komanso kuonera mafilimu kapena kuwerenga mabuku a zamizimu. Mwachitsanzo, mtsikana wina dzina lake Maria * pamene anali ndi zaka 12, ankaoneka kuti ankatha kulosera zinthu zosiyanasiyana komanso zinthu zinazake zoopsa zisanachitike. Ankawerengera anzake akusukulu makadi olosera zam’tsogolo. Iye ankasangalala kwambiri chifukwa ankaona kuti zimene ankanenazo zinkachitikadi.

Maria ankaganiza kuti zomwe ankachitazo inali mphatso yochokera kwa Mulungu kuti azithandiza anthu. Koma pambuyo pake anafotokoza kuti: “Ndinayamba kuona kuti zinalibe phindu. Nthawi zonse ndinkangolosera za tsogolo la anthu ena koma sindinkatha kudziwa za tsogolo langa.”

Maria ankakhala ndi mafunso ambiri moti ankapemphera kuti Mulungu amuthandize. Kenako tsiku lina kunabwera a Mboni za Yehova omwe anayamba kuphunzira naye Baibulo. Ataphunzira anazindikira kuti si Mulungu amene ankamuthandiza kulosera zam’tsogolo. Anaphunziranso kuti ngati akufunadi kuti Mulungu azimukonda ayenera kusiya chilichonse chokhudzana ndi zamizimu. (1 Akorinto 10:21) Kenako Maria anataya mabuku komanso zinthu zonse zokhudzana ndi zamizimu. Panopa amauza anthu ena zimene amaphunzira m’Baibulo.

Munthu wina dzina lake Michael ali wachinyamata, ankakonda kuwerenga mabuku a nkhani zongopeka ofotokoza za anthu omwe ankachita zinthu ndi mphamvu zamatsenga. Michael ananena kuti: “Ndinkasangalala kuwerenga nkhani za achinyamata anzanga omwe ankachita zinthu zodabwitsa.” Pang’ono ndi pang’ono Michael anazolowera kuwerenga mabuku a zamatsenga. Iye ananenanso kuti: “Nthawi zonse ndinkangokhala ndi kamtima kofuna kuwerenga mabuku komanso kuonera mafilimu azamatsenga.”

Michael atayamba kuphunzira Baibulo, anaona kuti ndi bwino kukhala wosamala ndi zimene ankawerenga. Iye ananena kuti: “Ndinalemba mndandanda wa zinthu zanga zonse zokhudzana ndi zamizimu ndipo ndinakazitaya. Ndinaphunzira mfundo yofunika kwambiri palemba la 1 Akorinto 10:31. Lembali limati: ‘Chitani zonse kuti zibweretse ulemerero kwa Mulungu.’ Panopa ndikamawerenga buku linalake ndimadzifunsa kuti ‘Kodi bukuli silingandichititse kulephera kupereka ulemerero kwa Mulungu?’ Ndikangoona kuti zimenezo n’zimene zingachitike, ndimalisiya.”

Baibulo limafotokoza kuti mawu a Mulungu ndi nyale. Limatithandiza kapena kutiunikira kuti tidziwe zoona zake pa nkhani yokhudza kukhulupirira zamizimu. (Salimo 119:105) Limatiuzanso kuti m’tsogolomu, sikudzakhalanso anthu oipa amene amachita zinthu motsogoleredwa ndi ziwanda. Anthu amenewa akadzachoka, padzikoli padzakhala mtendere waukulu. Mwachitsanzo lemba la Salimo 37:10, 11 limati: “Patsala kanthawi kochepa, woipa sadzakhalakonso. Udzayang’ana pamene anali kukhala, ndipo sadzapezekapo. Koma anthu ofatsa adzalandira dziko lapansi, ndipo adzasangalala ndi mtendere wochuluka.”

^ ndime 10 Tasintha mayina m’nkhaniyi.