Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YA PACHIKUTO | KODI NDI BWINO KUKHULUPIRIRA ZAMATSENGA?

Ambiri Amachita Chidwi ndi Nkhani Zamatsenga

Ambiri Amachita Chidwi ndi Nkhani Zamatsenga

Nyuzipepala ina inanena kuti: “Kuyambira kale kunkapezeka mafilimu komanso mabuku onena za mizukwa, ofotokoza za anthu ouka kumanda akudzayamwa magazi a anthu komanso onena za anthu omwe amasanduka mimbulu. Masiku ano mafilimu ambiri akumasonyeza anthu ogwidwa ndi ziwanda komanso ena omwe ali ndi mphamvu yochita zamatsenga.”—The Wall Street Journal.

MASIKU ANO kwachuluka mafilimu, masewera a pakompyuta ndi mabuku osonyeza achinyamata komanso akuluakulu akuchita zaufiti. Amasonyezanso mizukwa ndi afiti ooneka bwino. N’chifukwa chiyani anthu amakonda kuonera mafilimu komanso kuwerenga mabuku a zamatsengawa?

Pulofesa wina woona za chikhalidwe cha anthu dzina lake Claude Fischer, analemba kuti: “Anthu ambiri ku America amakhulupirira zoti kuli mizukwa. Poyamba, munthu mmodzi pa anthu 10 alionse ankakhulupirira zimenezi. Koma chiwerengerochi chinakwera moti chafika pa munthu mmodzi pa anthu atatu alionse. Achikulire ambiri ku America amanena kuti amakhulupirira za mizukwa, zoti kuli nyumba zomwe mumakhala mizimu yoipa ndipo anafotokozapo kuti anapitako kwa a zamatsenga. Komabe achinyamata ambiri ndi amene amachita zimenezi moti chiwerengero chawo chimawirikiza kawiri chiwerengero cha anthu achikulire.”

N’zosadabwitsa kuti masiku ano nkhani zonena za anthu omwe ali ndi mphamvu yochita zamatsenga zayambanso kumveka kwambiri. Michael Calia yemwe ndi mtolankhani wa nyuzipepala imene taitchula koyambirira ija analemba kuti: “M’zikhalidwe zambiri anthu amakhulupirira anthu omwe ali ndi mphamvu yochita zamatsenga. Zimenezi zikusiyana ndi zomwe zinkachitika zaka za m’mbuyomo pomwe anthu ankakhulupirira zamizukwa, za anthu ouka kumanda kudzayamwa magazi a anthu komanso za anthu omwe amasanduka mimbulu.”

Lipoti lina linanena kuti “kulikonse padzikoli, anthu 25 pa 100 alionse mpaka anthu 50 pa 100 alionse, amakhulupirira kuti kuli mizukwa. Ndipo nkhani zamizukwa zimalembedwa m’mabuku a anthu azikhalidwe zosiyanasiyana.” Kafukufuku wina amene Pulofesa Christopher Bader ndi Pulofesa Carson Mencken, omwe ndi akatswiri oona za chikhalidwe cha anthu ku United States anachita, anasonyeza kuti anthu 70 kapena 80 pa 100 alionse a ku America amakhulupirira mtundu winawake wa zamatsenga.

Kodi pali vuto lililonse ngati munthu amakhulupirira kapena kuchita zamatsenga?