Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

GALAMUKANI! Na. 2 2017 | Kodi Ndi Bwino Kukhulupirira Zamatsenga?

Masiku ano mafilimu ndi mapulogalamu a pa TV ambiri amasonyeza anthu akuchita zamatsenga, ufiti komanso anthu ouka kumanda akudzayamwa magazi a anthu.

Kodi mukuganiza bwanji? Kodi pali vuto lililonse ngati munthu amaonera mafilimu ndi mapulogalamu otero?

Galamukani! iyi ikufotokoza zimene zimachititsa kuti anthu ambiri azichita chidwi ndi nkhani zamatsenga. Ikufotokozanso kuopsa kochita zimenezi.

 

NKHANI YAPACHIKUTO

Ambiri Amachita Chidwi ndi Nkhani Zamatsenga

Anthu ambiri akuchita chidwi ndi nkhani ngati za afiti, anthu osanduka mimbulu, ogwidwa ndi ziwanda komanso za mizukwa. N’chifukwa chiyani anthu akuchita chidwi ndi nkhani zimenezi?

NKHANI YAPACHIKUTO

Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani pa Nkhani ya Kukhulupirira Zamizimu?

Anthu ambiri amaona kuti palibe vuto ndi kuchita zamatsenga, Baibulo limanena mosapita m’mbali za kuopsa kwake. Kodi Malemba amati chiyani pa nkhani imeneyi ndipo n’chifukwa chiyani?

KODI ZINANGOCHITIKA ZOKHA?

Njuchi Zimatera Mochititsa Chidwi

Kodi kudziwa zimene njuchi imachita ikamatera kungathandize bwanji popanga maloboti otha kuwaulutsa ndi kumawawongolera? Kodi akatswiri opanga maloboti otha kuuluka angaphunzire chiyani poona zimene njuchi imachita ikamatera?

MFUNDO ZOTHANDIZA MABANJA

Mungatani Ngati Muli ndi Chisoni Chifukwa cha Imfa ya Bambo Kapena Mayi Anu?

Zimakhala zothetsa nzeru kwambiri bambo kapena mayi ako akamwalira. Kodi wachinyamata amene bambo kapena mayi anamwalira, angatani ngati ali ndi chisoni chifukwa cha imfa ya kholo lakelo?

Zimene Zimachitika Ana Akakhala ndi Chisoni

Kodi mfundo za m’Baibulo zinathandiza bwanji achinyamata atatu omwe makolo awo anamwalira kuti athe kupirira?

ANTHU NDI MAYIKO

Dziko la Spain

Ku Spain kuli mitundu yambiri ya anthu komanso zinthu zachilengedwe zosiyanasiyana zochititsa chidwi. Ku Spain n’kumene kumapezeka mafuta a maolivi ambiri kuposa mayiko ena onse padziko lapansi.

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

Mtanda

Anthu ambiri amaona kuti mtanda ndi chizindikiro cha Akhristu. Kodi Yesu anafera pamtanda? Nanga kodi ophunzira a Yesu ankagwiritsa ntchito mtanda polambira Mulungu?

Kodi Mungakonde Kumvetsa Zimene Baibulo Limaphunzitsa?

Werengani nkhaniyi kuti mudziwe zimene muyenera kuchita komanso zimene simukufunikira kuchita kuti mumvetse zimene Baibulo limaphunzitsa.

Zina zimene zili pawebusaiti

Kodi N’chiyani Chingandithandize Ndikakumana ndi Mavuto?

Achinyamata akufotokoza zimene anachita atakumana ndi mavuto.

Kodi Ziwanda Zilipodi?

Kodi ziwanda ndi chani? Kodi zinachokera kuti?