Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Malangizo Otithandiza Kukhala Mwamtendere Ndi Anzathu

Malangizo Otithandiza Kukhala Mwamtendere Ndi Anzathu

Mlengi wathu amatiuza mmene tingakhalire mwamtendere ndi ena kaya tili kunyumba, kuntchito kapena tikakhala ndi anzathu. Taganizirani ena mwa malangizo anzeru awa amene anthu ambiri anawagwiritsapo ntchito.

Muzikhululuka

“Pitirizani . . . kukhululukirana ndi mtima wonse, ngati wina ali ndi chifukwa chodandaulira za mnzake.”​—AKOLOSE 3:13.

Tonse timalakwitsa, tikhoza kulakwira anthu ena kapena anthu ena angatilakwire. Mulimonsemo, timafunika kukhululukira anzathu kapenanso kukhululukiridwa. Tikakhululuka, sitimasungiranso chakukhosi munthu amene anatilakwirayo. Sitibwezera “choipa pa choipa,” ndipo sitikhalira kukumbutsa munthu zimene amalakwitsa kapena zofooka zake. (Aroma 12:17) Nanga bwanji ngati munthu wina watilakwira kwambiri ndipo sitingaiwale zimene watichitirazo? Ngati ndi choncho tingachite bwino kukambirana naye mwaulemu pa awiri. Cholinga chizikhala kukhazikitsa mtendere, osati kupeza wina wolakwa.​—Aroma 12:18.

Muzikhala Odzichepetsa Komanso Aulemu

‘Muzidzichepetsa, ndi kuona ena kukhala okuposani.’​—AFILIPI 2:3.

Tikakhala odzichepetsa komanso aulemu anthu amasangalala kuchita nafe zinthu. Amadziwa kuti tichita nawo zinthu mokoma mtima komanso mowaganizira ndipo sitingachite zinthu zowakhumudwitsa mwadala. Koma tikamadziona kuti ndife ofunika kwambiri kuposa anthu ena kapena kumangofuna kuti anthu ena aziyendera maganizo athu, timayambitsa mikangano, anthu angamatipewe komanso ngati tingakhale ndi anzathu, angakhale ochepa kwambiri.

Muzipewa Tsankho

“Mulungu alibe tsankho. Iye amalandira munthu wochokera mu mtundu uliwonse, amene amamuopa ndi kuchita chilungamo.”​—MACHITIDWE 10:34, 35.

Mlengi wathu saona kuti anthu ena ndi ofunika kwambiri kuposa ena chifukwa cha dziko lawo, chilankhulo chawo, mtundu wawo kapenanso kaonekedwe ka khungu lawo. Ndipo “kuchokera mwa munthu mmodzi anapanga mtundu wonse wa anthu.” (Machitidwe 17:26) Choncho zimenezi zikutanthauza kuti, anthu onse ndi apachibale. Tikamachita zinthu ndi anthu ena mwaulemu komanso mokoma mtima, amasangalala, ifenso timasangalala ndipo Mlengi wathu amasangalalanso kwambiri.

Muzikhala Ofatsa

“Valani . . . kufatsa.”​—AKOLOSE 3:12.

Tikakhala ofatsa, anthu ena amamva bwino. Iwo amakhala omasuka kulankhula nafe komanso kutikonza tikalakwitsa zinthu chifukwa amadziwa kuti tikhalabe odekha. Ndipo munthu wina akatipsera mtima, kumuyankha modekha kungamuthandize kuti mtima wake ukhale m’malo. Lemba la Miyambo 15:1 limati: “Kuyankha modekha kumabweza mkwiyo, koma mawu opweteka amayambitsa mkwiyo.”

Muzikhala Opatsa Komanso Muziyamika

“Kupatsa kumabweretsa chimwemwe chochuluka kuposa kulandira.”​—MACHITIDWE 20:35.

Masiku ano anthu ambiri ndi adyera ndipo amangoganizira zofuna zawo zokha. Koma chimwemwe chenicheni chimabwera chifukwa chokhala wopatsa. (Luka 6:38) Anthu opatsa amakhala osangalala chifukwa chakuti amasonyeza kuti amakonda anthu ena kuposa chuma. Chikondi chimenechi chimawathandiza kuti aziyamikira anthu ena akawasonyeza mtima wopatsa. (Akolose 3:15) Dzifunseni kuti, ‘Kodi ndingakonde kukhala ndi anthu oumira komanso osayamika kapena opatsa komanso oyamikira?’ Mfundo yake ndi yotani? Muyenera kumachita zinthu zimene mungafune kuti anthu ena akuchitireni.​—Mateyu 7:12.