Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

MFUNDO ZOTHANDIZA MABANJA | ACHINYAMATA

Kodi Mungatani Kuti Mukhale ndi Anzanu Apamtima?

Kodi Mungatani Kuti Mukhale ndi Anzanu Apamtima?

VUTO LIMENE LIMAKHALAPO

Masiku ano munthu amatha kucheza ndi anthu ambiri omwe ali kutali pogwiritsa ntchito zipangizo zamakono. Komabe mwina inuyo mumaona kuti anthu amene mukucheza nawo mwanjira imeneyi si anzanu apamtima. Mnyamata wina ananena kuti: “Poyamba ndinkacheza ndi anzanga ambirimbiri omwe panopa sitichezanso ngati kale. Koma bambo anga ali ndi anzawo apamtima omwe anayamba kucheza nawo kalekale.”

Kodi n’chifukwa chiyani masiku ano anthu amavutika kupeza anzawo apamtima?

ZIMENE MUYENERA KUDZIWA

Zipangizo zamakono zikuthandiza anthu kupeza anzawo ambiri koma osati apamtima. Masiku ano anthu amatha kugwiritsa ntchito njira zosiyanasiyana pocheza ndi anzawo ngakhale ali kutali. M’malo moti azicheza pamasom’pamaso akumangotumizirana mauthenga. Mwachitsanzo, buku lina linati: “Anthu sacheza kwambiri pamasom’pamaso ngati kale. Ndipo ana asukulu amakonda kucheza ndi anzawo pogwiritsa ntchito zipangizo zamakono.”—Artificial Maturity.

Nthawi zina anthu amene timacheza nawo pogwiritsa ntchito zipangizo zamakono, angaoneke ngati anzathu apamtima. Mwachitsanzo, mnyamata wina wazaka 22 dzina lake Brian * ananena kuti: “Ndinkakonda kutumizira anzanga mauthenga kuti ndingowapatsako moni. Koma posachedwapa ndazindikira kuti anzanga ambiri ankangodikira kuti ndiyambe ndine kuwatumizira uthenga. Kenako ndinasiya kuwatumizira mauthenga kuti ndione ngati nawonso anganditumizireko. Koma ndi ochepa chabe amene anachita zimenezi. Zomwe zinachitikazi zinandithandiza kudziwa kuti anthu ena amene ndinkacheza nawo si anzanga apamtima ngati mmene ndinkaganizira.”

Komatu zimenezi sizikutanthauza kuti kugwiritsa ntchito zipangizo zamakono sikungakuthandizeni kukhala ndi anzanu apamtima. Zimenezi zingakhale zotheka makamaka ngati anzanuwo mumachezanso nawo pamasom’pamaso. Choncho ndi bwino kukumbukira kuti zipangizo zamakono, nthawi zambiri zimangokuthandizani kupeza anthu oti muzicheza nawo, osati anzanu apamtima.

ZIMENE MUNGACHITE

Kodi mnzako wapamtima amakhala wotani? Baibulo limasonyeza kuti mnzako weniweni ‘amakumatirira kuposa m’bale wako.’ (Miyambo 18:24) Kodi mumafuna kuti mnzanu azichita zimenezi? Nanga inuyo mumachita zimenezi? Kuti muyankhe mafunsowa molondola, lembani makhalidwe abwino atatu amene mumafuna kuti mnzanu akhale nawo. Kenako lembani makhalidwe abwino atatu amene inuyo muli nawo. Ndiyeno dzifunseni kuti: ‘Pa anthu amene ndimacheza nawo pogwiritsa ntchito zipangizo zamakono, kodi ndi ndani amene amasonyeza makhalidwe amenewa? Kodi anzangawa anganene kuti ineyo ndimasonyeza makhalidwe abwino ati?’—Lemba lothandiza: Afilipi 2:4.

Muzidziwa zinthu zomwe n’zofunika. Nthawi zambiri anthu amene amayamba kucheza pogwiritsa ntchito zipangizo zamakono, amayamba kugwirizana chifukwa choti amakonda zofanana. Komabe chofunika kwambiri si kukonda zofanana koma kuyendera mfundo zofanana. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi zimene mtsikana wina wazaka 21, dzina lake Leanne ananena. Iye anati: “Sindicheza ndi anthu ambirimbiri, koma anzanga ochepa amene ndili nawo amandithandiza kuti ndizisonyeza makhalidwe abwino.”—Lemba lothandiza: Miyambo 13:20.

Muzikonda kucheza ndi anthu pamasom’pamaso. Kucheza ndi anthu pogwiritsa ntchito zipangizo zamakono, n’kosiyana kwambiri ndi kucheza nawo pamasom’pamaso. Izi zili choncho chifukwa chakuti, mukamaonana ndi munthu amene mukucheza naye, m’pamene mumazindikira mmene akumvera mumtima poona momwe akuyankhulira komanso mmene akuonekera.—Lemba lothandiza: 1 Atesalonika 2:17.

Muzilemberana makalata. Anthu ena amaona kuti kulemba kalata ndi kwachikale. Komatu n’kofunika chifukwa kupatula nthawi kuti mulembe kalatayo kumasonyeza kuti mumakonda kwambiri munthu yemwe mwamulemberayo. Komabe masiku ano anthu ambiri salemba makalata chifukwa amakhala otanganidwa. Mwachitsanzo, mayi wina dzina lake Sherry Turkle, analemba m’buku lake za mnyamata wina yemwe ananena kuti sanalandirepo kalata pa moyo wake. Mnyamatayu ananena kuti: “Ndimalakalaka ndikanakhala ndi moyo pa nthawi imene anthu ankalemberana kwambiri makalata.” (Alone Together) Nanunso mungachite bwino kwambiri kumalembera anzanu makalata.

Mfundo yofunika kwambiri: Kuyankhulana nthawi zonse pogwiritsa ntchito zipangizo zamakono sikungathandize kuti munthu akhale ndi anzake apamtima. Koma amafunika kuchita zinthu limodzi ndi anzakewo, kusonyezana chikondi, chifundo, kudekha komanso kukhululukirana. Makhalidwewa ndi amene amathandiza kuti anthu azigwirizana kwambiri. Koma ngati mukungogwiritsa ntchito zipangizo zamakono, zingakhale zovuta kusonyezana makhalidwe amenewa.

^ ndime 8 Tasintha maina ena m’nkhani ino.