Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

KODI ZINANGOCHITIKA ZOKHA?

Kanyama Kam’madzi Komwe Kamasinthasintha Mtundu

Kanyama Kam’madzi Komwe Kamasinthasintha Mtundu

KANYAMAKA kamatha kusintha mtundu moti nthawi zina kakasintha, munthu sangakaone. Lipoti lina linanena kuti “thupi la kanyamaka limatha kusinthasintha kaonekedwe kake mofulumira kwambiri.” Kodi kamachita bwanji zimenezi?

Taganizirani izi: Kanyamaka kamasintha mtundu pogwiritsa ntchito maselo omwe amapezeka mkati mwa khungu lake. Maselowa amakhala ndi tinthu ting’onoting’ono tokhala ngati timatumba ndipo timakhala ndi mitundu yosiyanasiyana. Komanso kunja kwa tinthu tokhala ngati timatumbati kuli timinofu. Ndiyeno kanyamaka kakafuna kusintha mtundu, ubongo wake umatumiza uthenga kutiminofu tija, kuti tikokeke. Zikatere timatumbato timafutukuka ndipo nthawi yomweyo kamasintha mtundu. Kanyamaka kamasintha mtundu pofuna kudziteteza komanso kukopa kakakazi.

Akatswiri a payunivesite ya Bristol ku England anapanga kanthu kokhala ngati khungu la kanyamaka. Pofuna kuti kanthu komwe anapangako kazichita zinthu ngati khungu la kanyamaka, akatswiriwo anapanga tinthu tomwe timagwira ntchito ngati timinofu tamuselo la kanyama kaja ndipo anatilumikiza kutimalabala tinatake tozungulira, takuda. Akatswiriwa atalumimikiza kanthuka kumagetsi, timalabala tija tinakokeka ndipo kanthuko kanasintha mtundu.

Katswiri wina yemwe anachita nawo kafukufukuyu dzina lake Jonathan Rossiter ananena kuti zimene anapezazi zikhoza kuthandiza kuti akatswiri apange zovala zotha kusintha mtundu mofulumira kwambiri potengera “zimene zimachitika kuti kanyamaka kasinthe mtundu.” A Rossiter ananenanso kuti anthu angamavale zovalazi pofuna kuti anthu asawazindikire komanso kuti azioneka bwino.

Kodi inuyo mukuganiza bwanji? Kodi zinangochitika zokha kuti kanyamaka kazisintha mtundu chonchi, kapena pali winawake amene anakalenga kuti kazichita zimenezi?