Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

ANTHU NDI MAYIKO

Dziko la Liechtenstein

Dziko la Liechtenstein

DZIKOLI lili m’gulu la mayiko aang’ono kwambiri padziko lonse ndipo lili m’chigawo cha mapiri pakati pa dziko la Switzerland ndi Austria. Anthu a mitundu yosiyanasiyana monga Aselote, Alatiyani, Aroma komanso Alemani akhala m’dzikoli kwa zaka zambiri. Koma panopa Alemani ndi amene alipo ochuluka kwambiri, ndipo akhala m’dzikoli kwa zaka pafupifupi 1,500.

Chiyankhulo chachikulu cha m’dzikoli ndi Chijeremani koma anthu amayankhulanso mosiyanasiyana malinga ndi madera. M’dzikoli anthu amakonda kudya chakudya china chotchedwa Tüarka-Rebel. Chakudya chimenechi chimapangidwa kuchokera ku chimanga. Amakondanso chakudya china chotchedwa Käsknöpfle chomwe amachiphika posakaniza tchizi ndi zakudya zinazake zopangidwa ndi tirigu.

Käsknöpfle

Zovala zachikhalidwe

Anthu ochokera m’mayiko ena amakonda kupita kudzikoli kukaona malo chifukwa choti lokongola kwambiri. Alendowa amaona zigwa zokongola, minda ya mpesa, zomera za mitundu yosiyanasiyana komanso mapiri okongola omwe amaoneka oyera chifukwa kumagwa chisanu. Mwachitsanzo, ngakhale kuti dzikoli ndi laling’ono kwambiri, muli mitundu pafupifupi 50 ya maluwa am’tchire okongola kwambiri. M’dzikoli mulinso malo osungira zinthu zakale, malo ochitira masewero komanso malo ambiri opangira vinyo. Chifukwa cha zimenezi, alendo amabwera m’dzikoli m’nthawi yotentha ngakhalenso yozizira.

M’dzikoli mwakhala muli a Mboni za Yehova kuyambira m’ma 1920. Panopo m’dzikoli muli a Mboni za Yehova pafupifupi 90 ndipo amaphunzira Baibulo ndi anthu a m’dzikolo komanso alendo ochokera m’mayiko ena.