Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

Kumwamba

Kumwamba

Anthu amakhala ndi maganizo osiyanasiyana pa nkhani ya kumwamba. Komabe, zimene Baibulo limanena pa nkhaniyi ndi zosiyana kwambiri ndi zimene anthu amanena.

Kodi mawu akuti kumwamba amatanthauza chiyani?

ZIMENE ANTHU ENA AMANENA

Anthu amakhala ndi maganizo osiyanasiyana okhudza kumwamba. Mwachitsanzo:

  • Akhristu ambiri angagwirizane ndi zimene buku lina limanena kuti kumwamba “n’kumene anthu odala amapita akamwalira.”—New Catholic Encyclopedia.

  • Rabi wina wachipembedzo cha Chiyuda, dzina lake Bentzion Kravitz, ananena kuti Chiyuda chimafotokoza kwambiri za moyo uno osati wa pambuyo pa imfa. Komabe Rabiyu ananena kuti “mzimu wa munthu womwalira ukapita kumwamba, umakasangalala kwambiri ndipo munthuyo amayandikana kwambiri ndi Mulungu kuposa pamene anali padziko lapansi.” Rabiyu ananenanso kuti “ngakhale kuti anthu a m’chipembedzo cha Chiyuda amakhulupirira za kumwamba, buku la Torah silinena zambiri pa nkhaniyi.”

  • Ahindu ndi Abuda amakhulupirira kuti kumwamba kuli ndi magawo ambiri. Amati kumwamba ndi malo amene munthu akamwalira amakakhalako nthawi yochepa. Kenako munthuyo amatha kubadwanso padziko lapansi kapena kukwera kumwamba kwina, komwe ndi kwabwino kwambiri ndipo amakakhala mwamtendere.

  • Anthu ena amatsutsiratu zomwe zipembedzo zimanena zokhudza kumwamba ndipo amaona kuti anthu amene amakhulupirira zimenezi ndi achibwana komanso opepera.

Anthu amakhala ndi maganizo osiyanasiyana pa nkhani ya kumwamba

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

M’Baibulo mawu akuti kumwamba amatanthauza zinthu zingapo. Mwachitsanzo:

  • Lemba la Genesis 1:20 limanena kuti Mulungu atalenga mbalame anati, “ziuluke m’mlengalenga mwa dziko lapansi.” Palembali mawu akuti “m’mlengalenga” akutanthauza kumwamba kumene timatha kuona ndi maso athu.

  • Lemba la Yesaya 13:10 limanena za “nyenyezi zakumwamba ndi magulu a nyenyezi” zomwe zimakhala kutali kwambiri. Choncho kumwamba kumeneku ndi kutali poyerekeza ndi malo amene mbalame zimauluka.

  • Baibulo limatchulanso za malo omwe Mulungu komanso angelo amakhala kuti kumwamba. (1 Mafumu 8:30; Mateyu 18:10) Mawu akuti “kumwamba” amene takambiranawa si okuluwika koma amatanthauzadi malo enieni. *

“Yang’anani muli kumwamba, ndipo muone kuchokera pamalo anu okhala apamwamba, oyera ndi okongola.”Yesaya 63:15.

Kodi anthu onse abwino amapita kumwamba akamwalira?

Baibulo silinena kuti padzikoli ndi pongoyembekezera kuti tikadzamwalira tidzapite kumwamba. Komanso silisonyeza kuti chinali cholinga cha Mulungu kuti anthufe tizifa. Mwachitsanzo:

  • Mulungu anauza Adamu ndi Hava kuti: “Muberekane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi.” (Genesis 1:28) Mulungu ankafuna kuti anthu azikhala padziko lapansili mpaka kalekale. Koma anawauza kuti akadzadya chipatso choletsedwa adzafa. N’zomvetsa chisoni kuti Adamu ndi Hava anasankha kusamvera Mulungu.—Genesis 2:17; 3:6.

  • Zimene Adamu ndi Hava anachitazi zinachititsa kuti afe ndipo ana awonso anayamba kufa. (Aroma 5:12) Koma kodi zikutanthauza kuti anthu sangakhalenso ndi moyo mpaka kalekale?

  • Baibulo limanena kuti “pali kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano zimene ife tikuyembekezera mogwirizana ndi lonjezo lake.” * (2 Petulo 3:13) Mulungu adzathetsa mavuto padzikoli pogwiritsa ntchito Ufumu wake ndipo adzalikonza kuti likhale mmene linalili poyamba. Baibulo limanena kuti pa nthawiyi “imfa sidzakhalaponso.” (Chivumbulutso 21:3, 4) Kodi lembali likunena za kumwamba kapena padziko lapansi? Tikanena kuti chinthu ‘sichidzakhalaponso’ ndiye kuti poyamba chinalipo. Ndiyetu imfa sinayambe yachitikapo kumwamba. Zimenezi zikusonyeza kuti vesili likunena za dziko lapansi. Ndipo monga taonera kale, Mulungu analenga dzikoli kuti anthu azikhalamo mpaka kalekale, zomwenso anthufe timalakalaka. N’chifukwa chake Baibulo limanena kuti Mulungu adzaukitsa anthu amene anamwalira kuti azidzakhalanso ndi achibale awo.—Yohane 5:28, 29.

Anthu ambiri amasangalala akadziwa zinthu zolondola zomwe Baibulo limaphunzitsa pa nkhani ya kumwamba. Mwachitsanzo, munthu wina yemwe anali wa Katolika, dzina lake George anati: “Ndimaona kuti zomwe Baibulo limanena zoti anthu adzakhala padzikoli mpaka kalekale n’zomveka kwambiri poyerekezera ndi zomwe ena amanena zoti tonse tidzapita kumwamba.” *

“Kunena za kumwamba, kumwamba ndi kwa Yehova, koma dziko lapansi analipereka kwa ana a anthu.”Salimo 115:16.

^ ndime 13 Mulungu ali ndi thupi ngati la angelo loti sitingalione ndi maso athu. (Yohane 4:24) Choncho, amakhala kumalo amene angelo amakhala, ndipo malo amenewo ndi osiyana kwambiri ndi dzikoli komanso kumwamba kumene timaonaku.

^ ndime 19 Mawu akuti “dziko lapansi latsopano” sakutanthauza kuti Mulungu adzalenganso dziko lina. Koma amatanthauza anthu omvera omwe azidzakhala padzikoli.—Salimo 66:4.

^ ndime 20 Baibulo limanena kuti Mulungu anasankha anthu ochepa okha kuti adzapite kumwamba. Anthuwa ndi okwana 144,000 ndipo azidzalamulira dzikoli limodzi ndi Yesu ali kumwamba.—1 Petulo 1:3, 4; Chivumbulutso 14:1.