Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

KODI ZINANGOCHITIKA ZOKHA?

Zomera Nazonso Zimadziwa Masamu

Zomera Nazonso Zimadziwa Masamu

ZOMERA zimapanga zakudya zake masana pogwiritsa ntchito dzuwa. Popeza dzuwa limawala masana okha, zomerazi zimasunga chakudya china kuti zigwiritse ntchito kukada. Nazonso zimadziwa kuti usiku ndi wautali, moti zimachita masamu kuti zakudyazo zifike m’mawa.

Taganizirani izi: Akatswiri ena anafufuza mtundu winawake wa zomera ndipo anapeza kuti kukangocha, zomerazi zimayambapo ntchito yake yosintha mpweya woipa kuti ukhale chakudya. Zimachita zimenezi pogwiritsa ntchito mphamvu ya dzuwa. Ndiyeno kukada, zomerazi zimagwiritsa ntchito zakudya zomwe zinasunga zija kuti zisafe ndi njala komanso kuti zikule. Komatu sikuti zimangodya mowononga. Akatswiri aja anapeza kuti zomerazi zimagwiritsa ntchito zakudya mwanzeru kwambiri moti kukamacha, zina zimatsala.

Anapezanso kuti zomerazi zimachita masamu n’kugawa bwino chakudya kuti chisathe pakati pa usiku. Ndiye kaya usiku utalike kapena ufupike, zimapezekabe kuti kukamacha, chakudya china chimatsala. Kodi zimenezi zimatheka bwanji? Zomerazi zimagawa kuchuluka kwa chakudya chimene zasunga ndi kuchuluka kwa maola amene atsala kuti kuche. Zikaona kuti maola achuluka, zimachepetsa kadyedwe, koma maola akachepa, zimadya momasuka.

Ndiye kodi zomerazi zimadziwa bwanji kuchuluka kwa chakudya chimene zasunga? Nanga zimadziwa bwanji maola amene atsala kuti kunja kuche? Akatswiri akufufuzabe kuti apeze mayankho a mafunso amenewa.

Kodi inuyo mukuganiza bwanji? Kodi zinangochitika zokha kuti zomerazi zizidziwa masamu chonchi, kapena pali winawake amene anazilenga kuti zizichita zimenezi?