Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 KUCHEZA NDI | A GENE HWANG

Katswiri wa Masamu Akufotokoza za Chikhulupiriro Chake

Katswiri wa Masamu Akufotokoza za Chikhulupiriro Chake

A Gene Hwang anabadwa mu 1950 ku Tainan m’dziko la Taiwan, ndipo anali pulofesa wa masamu pa yunivesite ya National Chung Cheng. Anaphunzitsaponso pa yunivesite ya Cornell ku United States ndipo ali kumeneko anachita kafukufuku wosiyanasiyana. A Hwang ndi munthu wodziwika bwino pa nkhani zamasamu. Poyamba ankakhulupirira kuti zamoyo zinachita kusintha kuchokera ku zinthu zina koma kenako anasintha maganizo. Mtolankhani wa Galamukani! anacheza nawo kuti adziwe za ntchito yawo komanso zimene amakhulupirira.

Kodi n’chiyani chinakuchititsani kuti muzikhulupirira kuti zamoyo zinachita kusintha?

Ndili mwana, aphunzitsi athu ankatiphunzitsa kuti zamoyo zinachita kusintha kuchokera ku zinthu zina, komabe sikuti ndinkazimvetsa bwinobwino. Kenako makolo anga anayamba chipembedzo cha Chitao, ndipo nthawi zina ndinkapita nawo limodzi kukapemphera. Ndinkakonda kufunsa atsogoleri achipembedzo chathucho mafunso ambiri, koma sankandiyankha zogwira mtima.

N’chifukwa chiyani munasankha kuphunzira zamasamu?

Nditangoyamba kumene sukulu ndinkakonda kwambiri masamu. Ankandisangalatsa kwambiri moti nditapita ku yunivesite, ndinasankha kuti ndiphunzire masamu. Chimene amandisangalatsira kwambiri n’choti amakhala ndi njira yotsatirika yopezera yankho.

N’chiyani chinachititsa kuti muyambe kuchita chidwi ndi Baibulo?

Mu 1978, mkazi wanga Jinghuei, anayamba kuphunzira Baibulo ndi a Mboni za Yehova ndipo nthawi zina ndinkakhalapo akamaphunzira. Pa nthawiyi, tinkakhala ku United States ndipo n’kuti Jinghuei atangolandira kumene digirii yake ya zasayansi. Ineyo ndinkaphunzira zamasamu pa yunivesite ya Purdue m’chigawo cha Indiana ku United States.

Kodi pa nthawiyi munkaona kuti Baibulo ndi buku lapadera?

Ee. Ndinkachita chidwi ndi zimene limanena pa nkhani ya mmene Mulungu anakonzera dzikoli kuti pakhale anthu. Buku la Genesis limafotokoza mwachidule komanso momveka bwino za masiku 6 amene Mulungu analenga zinthu. * Zimenezi n’zomveka poyerekeza ndi  zimene nthano zina zakale zimanena pa nkhaniyi. Komabe, panatenga nthawi kuti ndiyambe kukhulupirira kuti palidi Mulungu amene analenga zonse.

N’chifukwa chiyani zinkakuvutani kukhulupirira kuti kuli Mulungu?

Zinali zovuta kwambiri kuti ndisiye zimene ndinkakhulupirira kuyambira ndili mwana

Monga ndanenera, ndinayamba kukhulupirira zoti kulibe Mulungu ndili wamng’ono kwambiri. Komanso chipembedzo chomwe ndinkapita sichinkaphunzitsa zoti pali Mulungu amene analenga zinthu zonsezi. Ndiye ndisaname, zinali zovuta kuti ndiyambe kukhulupirira zoti kuli Mulungu kamodzin’kamodzi.

Ndiye munandiuza kuti kenako munayamba kukhulupirira zoti kuli Mulungu. N’chifukwa chiyani munasintha maganizo?

Nditaganizira mozama mmene moyo unayambira, ndinaona kuti zamoyo sizinachokere ku zinthu zopanda moyo. Mwachitsanzo, kuti selo lipange linzake limayenera kukhala ndi malangizo olithandiza kupanga maselo ena ofanana nalo. Ngakhale selo wamba, limafunika kukhala ndi zonse zofunika kuti lipange selo lina. Ineyo ndimaona kuti n’zosamveka kunena kuti zimenezi zinangochitika zokha. Kuti munthu upeze yankho la samu, sumangolota yankho lake. Umafunika kutsatira njira yake yonse bwinobwino n’kupeza yankho. Ndiye kungakhale kulakwitsa kwambiri kungoganiza kuti selo linachita kusintha kuchokera ku zinthu zopanda moyo, popanda umboni womveka bwino.

Ndiye n’chiyani chinachititsa kuti muyambirenso kuphunzira Baibulo ndi a Mboni za Yehova?

Mu 1995, ndinapita ku Taiwan ndipo mwadzidzidzi ndinayamba kudwala kwambiri. Ndinamuimbira foni mkazi wanga n’kumuuza kuti sizili bwino ndipo mkazi wangayo anaimbira foni a Mboni za Yehova a ku Taiwan kuti andithandize. A Mboniwo anandisakasaka n’kundipeza panja pa chipatala china nditafookeratu. Popeza pachipatalapo panali patadzaza, wa Mboni mmodzi anandilipirira chipinda cha pahotelo ina kuti ndigone. Wa Mboniyo ankabwera kudzandiona ndipo kenako ananditengera kuchipatala china kuti ndikalandire thandizo.

Zimene anandichitirazi zinandikhudza kwambiri moti ndinaona kuti a Mboni za Yehova ndi anthu achifundo kwambiri ndipo aka sikanali koyamba kundithandiza ineyo ndi banja langa. Ndinaona kuti zimene amakhulupirira ndi zimene zimawapangitsa kukhala anthu abwino kwambiri. Choncho ndinayambiranso kuphunzira Baibulo moti chaka chotsatira ndinabatizidwa n’kukhala wa Mboni za Yehova.

Kodi zimene mumakhulupirira sizitsutsana ndi kafukufuku amene mumachita?

M’pang’ono pomwe. Moti posachedwapa ndinatulukira njira inayake ya masamu yomwe ingathandize asayansi omwe amafufuza za majini. Kuphunzira mmene majini amagwirira ntchito kumatithandiza kumvetsa mmene zinthu zamoyo zinapangidwira. Kumatithandizanso kumvetsa zimene zimachitika kuti moyo ukhalepo. Kudziwa mmene zimenezi zimachitikira kumandigometsa kwambiri komanso kumandipangitsa kuona kuti Mulungu ali ndi nzeru zakuya.

Mungapereke chitsanzo?

Ndimagoma kwambiri ndi zimene zimachitika kuti zamoyo zichulukane. Pali zamoyo zinazake zomwe sizikhala zazimuna kapena zazikazi. Mwina mungadabwe kuti zimachulukana bwanji. N’zochititsa chidwi kwambiri chifukwa zamoyozi zikakula, zimaduka pakati n’kukhala ziwiri. Koma pali zamoyo zina zomwe zimachulukana pakakhala kuti pali zazimuna ndi zazikazi.

Kusiyana kumenekutu n’kochititsa chidwi kwambiri. Asayansi ena amati zamoyo zomwe zimakhala zina zazikazi, zina zazimuna, zinasintha kuchokera ku zamoyo zomwe zimangoduka pakati zija. Ndiye zingatheke bwanji kuti m’kupita kwa nthawi zinthu zisinthe kuchokera pa chinthu chimodzi kuduka pakati, kufika pa zamoyo ziwiri kukumana n’kubereka chamoyo china? N’zosamveka kuganiza kuti zimenezi zinachitikadi. Kwa ineyo, ndimaona kuti pali Mulungu amene analenga zamoyo zimenezi.

^ ndime 11 Kuti mudziwe zambiri pa nkhaniyi, werengani kabuku kachingelezi kakuti, Was Life Created? Kabukuka ndi kofalitsidwa ndi a Mboni za Yehova ndipo kakupezeka pa webusaiti ya www.jw.org.