Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

KODI ZINANGOCHITIKA ZOKHA?

Tizilombo Tomwe Timachotsa Mafuta

Tizilombo Tomwe Timachotsa Mafuta

M’CHAKA cha 2010, choboolera chitsime cha mafuta chinaphulika n’kumira m’nyanja ya Gulf of Mexico, moti mafuta oposa migolo 4 miliyoni anatayikira m’nyanjayi. Koma patangotha miyezi yochepa, ambiri mwa mafutawa anali atatha. Kodi chinachitika n’chiyani kuti mafutawo athe?

Taganizirani izi: Akatswiri asayansi anapeza kuti pali tizilombo tina tam’madzi, kapena kuti timabakiteriya, tomwe timachotsa mafuta. Pulofesa wina, dzina lake Terry Hazen, ananena kuti timabakiteriyati tili ngati “asilikali oyamwa mafuta.” Choncho, timabakiteriyati ndi timene tinayamwa mafuta amene anatayikira m’nyanja ya Gulf of Mexico.

Lipoti lina la BBC linati: “N’zosadabwitsa kuti m’madzi mumapezeka tizilombo totereti.” Chifukwatu “kuyambira kalekale tizilomboti takhala tikuchotsa mafuta omwe amatuluka pansi pa nyanja.”

N’zoona kuti njira zimene anthu amagwiritsa ntchito pochotsa mafuta m’nyanja zimathandiza. Koma vuto ndi loti njira zimenezi zimabweretsanso mavuto ambiri. Mankhwala amene amagwiritsa ntchito pochotsa mafutawa amakhala oopsa. Mankhwalawa amapangitsa kuti zinthu zachilengedwe zizilephera kuthandiza kuchotsa mafuta m’nyanja. Komanso amakhala ndi poizoni yemwe amawononga chilengedwe kwa nthawi yaitali. Koma timabakiteriyati timathandiza kuyeretsa nyanja popanda mavuto alionse. *

Kodi inuyo mukuganiza bwanji? Kodi zinangochitika zokha kuti tizilomboti tizitha kuchotsa mafuta m’nyanja, kapena pali winawake amene anatilenga m’njira yoti tizitha kuchita zimenezi?

^ ndime 6 Panopa asayansi sakudziwa mmene ngozi ya mafuta yomwe inachitika m’nyanja ya Gulf of Mexico idzakhudzire zinthu za m’madzi m’zaka zikubwerazi.