Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Sanasiye Kutsatira Zimene Amakhulupirira

Sanasiye Kutsatira Zimene Amakhulupirira

Pamene mtsikana wina dzina lake Song Hee anali ndi zaka 11, mayi ake anaona kuti ali ndi vuto la msana. Atapita kuchipatala, dokotala anapeza kuti ali ndi matenda opindika msana. Matendawa anakula kwambiri moti anafunika kumupanga opaleshoni. Koma iye sankafuna kuikidwa magazi pomuchita opaleshoniyo. Olemba Galamukani! anacheza naye motere:

Kodi madokotala anakuthandiza bwanji matendawo atapezeka?

Panali madokotala awiri amene anandithandiza kwa zaka zitatu. Koma msana wanga unkangopindikabe. Zinafika poipa kwambiri chifukwa msanawo unapindikira kumene kuli mtima ndi mapapo moti ndinkapuma movutikira kwambiri. Apa chofunika chinali opaleshoni basi.

Kodi unavomera kuti akupange opaleshoni?

Ee, ndinavomera. Anandiuza kuti opaleshoni yake ndi yovuta chifukwa msana wanga unapindika kwambiri ndipo pangafunike kundiika magazi. Koma ndinakana kuikidwa magazi chifukwa cha mfundo za m’Baibulo zimene ndimakhulupirira. *

Kodi unapeza dokotala wopanga opaleshoni mmene unkafunira?

Ine ndi mayi anga tinapeza dokotala wa kwathu ku Florida m’dziko la United States. Koma nditamuuza kuti sindikufuna kuikidwa magazi, ananena kuti palibe dokotala amene angapange opaleshoni yovuta choncho popanda kundiika magazi. Pa nthawiyo ndinali ndi zaka 14 ndipo anandiuza kuti ngati sindipangidwa opaleshoni ndidzafa ndisanakwanitse zaka 20.

Kodi unafotokoza chifukwa chake sulola kuikidwa magazi?

Ee, ndinafotokoza. Ndinamuuza kuti ndimakhulupirira zimene Baibulo limanena zoti Mulungu amaona kuti magazi ndi opatulika, kaya akhale a nyama kapena a munthu. * Munthu aliyense mu Isiraeli akadya magazi ankaphedwa. * Ndinamusonyezanso lemba la Machitidwe 15:19, 20 limene limalamula Akhristu kuti “apewe . . . magazi.” Ndiye ndinanena kuti lembali likutanthauza kuti sitiyenera kudya kapena kuikidwa magazi.

Kodi dokotalayo anayankha bwanji?

Anachita makani n’kumanena kuti andiikabe magazi. Achipatala ananena kuti ndikalola kuikidwa magazi, adzandichita opaleshoniyo kwaulere.

Iwe ndi mayi ako munatani atakuuzani zimenezo?

Tinakanabe ngakhale kuti madokotala onse ankakana kuchita opaleshoni popanda kundiika  magazi. Zinthu zinafika povuta kwambiri chifukwa ndinali mwana ndipo matendawo ankaipiraipirabe. Choncho nkhaniyi inapita kukhoti. Chosangalatsa n’chakuti woweruza milandu ku Florida ananena kuti tipeze dokotala amene angakwanitse zimene ndikufunazo pasanathe masiku 30.

Kodi munapeza dokotala wina?

Ee, anapezeka. Komiti Yolankhulana ndi Achipatala ya Mboni za Yehova inapeza dokotala wina wodziwa bwino maopaleshoni oterewa. Ndipo anamupeza ku New York masiku 30 aja asanathe. *

Kodi opaleshoniyo inayenda bwanji?

Inayenda bwino kwabasi. Dr. Robert M. Bernstein ndi amene anapanga opaleshoniyi ndipo anandiika zitsulo zowongolera msana. Atapanga mbali yoyamba ya opaleshoniyi anasiya kaye kuti adzamalize pakatha milungu iwiri.

N’chifukwa chiyani anaganiza zopanga kawiri?

Ankaganiza kuti tsiku loyambalo ndidzataya magazi ambiri choncho padzafunika kudikira milungu iwiri kuti maselo ofiira ena apangidwenso m’thupi. Koma chosangalatsa n’chakuti maulendo awiri onsewo sindinataye magazi ambiri. Izi zinatheka chifukwa choti anthu opanga opaleshoniwo anagwira bwino ntchito yovutayi. Ndinachiranso mwamsanga ndipo ndinapewa mavuto amene amabwera munthu akaikidwa magazi. *

Kodi dokotalayo anamva bwanji opaleshoniyo itayenda bwino?

Madokotala ayenera kuganizira odwala

Anasangalala kwambiri. Ananena kuti madokotala ochita opaleshoni ayenera kuganizira odwala awo. Iye amaona kuti si bwino kuchita zinthu zosemphana ndi maganizo a odwala kapena zimene amakhulupirira. Anthu ambiri amene si Mboni za Yehova amavomerezanso mfundo imeneyi.

^ ndime 7 Song Hee komanso mayi ake ndi a Mboni za Yehova. Song Hee anabatizidwa mu 2012 ali ndi zaka 16.

^ ndime 17 Makomiti Olankhulana ndi Achipatala amathandiza a Mboni kupeza madokotala amene angawathandize bwinobwino popanda kuwaika magazi.

^ ndime 21 Bungwe lina loona za umoyo ku Australia linalemba mavuto amene amabwera ngati munthu waikidwa magazi. Linati: “Munthu akaikidwa magazi, ndiye kuti waikidwa chiwalo chinachake. Ndiyeno munthu akaikidwa chiwalo china, thupi limadabwa ndipo limafuna chitachoka. Choncho kuikidwa magazi kuli ndi mavuto ake.”