Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

KODI ZINANGOCHITIKA ZOKHA?

Magiya a Kachilombo Kofanana ndi Nyenje

Magiya a Kachilombo Kofanana ndi Nyenje

KWA nthawi yaitali, anthu ankaganiza kuti magiya amangopezeka m’makina basi. Koma zimenezi si zoona. Tikutero chifukwa chakuti tizilombo tinatake tomwe timapezekapezeka ku Europe timakhalanso ndi magiya. *

Kachilomboka kakakhala kakang’ono kakhoza kulumpha maulendo ambirimbiri n’kuyenda mtunda wa mamita pafupifupi 4 pa sekondi imodzi yokha. Choncho munthu akangophethira kamodzi, kachilomboka kakhoza kulumpha mtunda wautali n’kusowa. Koma kuti kachite zimenezi, miyendo yake iwiri yakumbuyo iyenera kulumpha ndi mphamvu zofanana pa nthawi yofanana. Kodi n’chiyani chimakathandiza kuchita zimenezi?

Taganizirani izi: Asayansi apeza kuti miyendo yakumbuyo ya kachilomboka ili ndi magiya amene amalowana. Ndiyeno kakalumpha, magiyawo amathandiza kuti miyendoyo iziyenda mofanana. Koma popanda magiyawo, ndiye kuti kachilomboka kakalumpha kakhoza kumangozungulirazungulira.

Kachilomboka kakakhala kakang’ono kamafunika magiyawo chifukwa chakuti minyewa yake imakhala isanayambe kugwira ntchito bwinobwino. Koma kakakula minyewa yake ndi imene imathandiza kuti miyendo izichita zinthu zofanana kakamalumpha. Wasayansi wina dzina lake Gregory Sutton ananena kuti: ‘Tinkaganiza kuti magiya amapezeka m’makina opangidwa ndi anthu basi. Koma vuto ndi lakuti tinali tisanafufuze bwinobwino m’chilengedwe.’

Kodi inuyo mukuganiza bwanji? Kodi zinangochitika zokha kuti tizilomboti tizikhala ndi magiya kapena pali winawake amene anatilenga?

^ ndime 3 Tizilomboti tikakula magiyawo amathothoka.