Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Timabuku tambirimbiri takuti Dziperekeni pa Kuwerenga ndi Kulemba tapangidwa m’zilankhulo zoposa 100

Amaphunzitsa Baibulo Komanso Kuwerenga ndi Kulemba

Amaphunzitsa Baibulo Komanso Kuwerenga ndi Kulemba

Bungwe lina * loona za maphunziro linanena kuti: “Munthu aliyense ali ndi ufulu wophunzira ndipo akaphunzira, zinthu zimamuyendera bwino pa moyo wake.”

MALIPOTI akusonyeza kuti padziko lonse, anthu oposa 700 miliyoni azaka zoposa 15, sadziwa kuwerenga ndi kulemba. Choncho sangaphunzire paokha zinthu zosiyanasiyana zomwe zimalembedwa. Sangawerengenso mfundo za m’Baibulo zimene “zinalembedwa kuti zitilangize.” (Aroma 15:4) A Mboni za Yehova m’mayiko ambiri amaphunzitsa Baibulo komanso kuwerenga ndi kulemba ndipo amachita zonsezi kwaulere. Kodi ntchito imeneyi ikuthandizadi anthu?

Kuti tiyankhe, tiyeni tikambirane za ku Mexico. M’dzikoli, anthu ambiri amalankhula Chisipanishi ndipo kuyambira mu 1946, a Mboni aphunzitsa anthu oposa 152,000 kuwerenga ndi kulemba. Ena mwa anthuwa anayambanso kuphunzitsa anzawo. Boma la Mexico lalemba  makalata ambiri othokoza Mboni za Yehova chifukwa cha ntchito imeneyi. M’kalata ina linalemba kuti: “Anthu inu mukuchita bwino kwambiri. Akuluakulu a zamaphunziro akudziwa ntchito yaikulu imene mukugwira pophunzitsa anthu kuwerenga ndi kulemba.”

Ana ndi achikulire omwe akuthandizidwa chifukwa cha sukulu imeneyi. Mwachitsanzo, mayi wina dzina lake Josefina analowa sukuluyi ali ndi zaka 101 ndipo anadziwa kuwerenga ndi kulemba pambuyo pa zaka ziwiri.

Ngakhale kuti m’dzikoli anthu ambiri amalankhula Chisipanishi, ntchito yophunzitsa kuwerenga ndi kulembayi imachitikanso m’zilankhulo zina. Mu 2013, sukuluyi inachitika m’zilankhulo zokwana 8 ndipo anthu anaphunzira kuwerenga ndi kulemba m’zilankhulo zawo.

Kunena zoona, kuwerenga ndi kulemba n’kothandiza m’njira zambiri.Koma chofunika kwambiri n’chakuti kumathandiza anthu kuphunzira Baibulo. Tikutero chifukwa chakuti munthu akaphunzira Baibulo amatha kusiya makhalidwe oipa ndiponso kukhulupirira zinthu za bodza.—Yohane 8:32.

^ ndime 2 United Nations Educational, Scientific, and Cultural Organization.