Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 NKHANI YA PACHIKUTO

Umphawi Komanso Vuto Losowa Pokhala Zidzatha

Umphawi Komanso Vuto Losowa Pokhala Zidzatha

Bambo ena a ku United States, dzina lawo a Joe, anapuma pa ntchito yausilikali. Pa moyo wawo anakumana ndi mavuto ambiri, zomwe zinachititsa kuti kwa zaka 18, azisowa pokhala. Bambowa ankapita kulaibulale ina ya m’dera lakwawo. Nthawi zina ankacheza ndi mayi ena omwe ankagwira ntchito palaibulaleyi, dzina lawo a Cindi. Zimene ankakambirana zinasintha moyo wa bambowa.

Mnyamata wina wa ku Argentina, dzina lake Martín, ankaona kuti akusowekera kenakake pa moyo wake. Iye ankaona choncho, ngakhale kuti sanali wosauka. Zimenezi zinkachititsa kuti aziona kuti moyo wake ndi wopanda phindu. Pofuna kuthetsa vuto lakeli anachoka panyumba n’kumakakhala m’mbali mwa nyanja. Ankaganiza kuti zimenezi zipangitsa kuti azisangalala. Koma m’malo mosangalala, anayamba kuvutika maganizo. Kenako anapemphera kwa Mulungu akulira kuti: “Ngati mulipodi, ndithandizeni kuti ndikudziweni.” Ichi chinali chiyambi cha kusintha kwa moyo wake.

PALI zifukwa zosiyanasiyana zomwe zimapangitsa kuti anthu azisowa pokhala. Kwa ena, ngati a Joe, chimakhala chifukwa choti anakumana ndi mavuto enaake pa moyo wawo. Koma kwa ena monga Martín, chimakhala chifukwa choti angotopa ndi moyo wochita zomwezomwezo, ndipo akufuna kuchoka panyumba kuti mwina angakakhale ndi moyo wosangalala. Pali enanso amene amasowa pokhala chifukwa cha nkhanza za m’banja, umphawi, ulova, ngozi zadzidzidzi komanso chifukwa choti alibe nyumba. Ndiye pali enanso amene amangokhala m’misewu chifukwa cha kumwa mwauchidakwa, kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo komanso chifukwa cha matenda.

Poyamba, anthu a m’mayiko osauka kapena a m’mayiko omwe muli nkhondo komanso umphawi wadzaoneni ndi amene ankasowa pokhala. Koma pulofesa wina dzina lake Paul Toro ananena kuti, “masiku ano vutoli likupezekanso m’mayiko olemera.” * Zina zomwe zikuchititsa zimenezi, ndi chifukwa choti maboma ambiri sathandiza mokwanira mabanja osauka komanso chifukwa choti pali kusiyana kwakukulu pakati pa anthu olemera ndi osauka.

Anthu ambiri osowa pokhala amada nkhawa akamaganizira za tsogolo lawo. Koma ena amalimba mtima akadziwa zomwe  Baibulo limanena zokhudza zimene zidzachitike m’tsogolo. Komanso m’Baibulo muli mfundo zomwe zingatithandize pa nkhani zachuma ndiponso kuti tikhale ndi moyo wathanzi. Mfundo zimenezi ndi zimenenso zinathandiza a Joe komanso Martín.

ZIMENE ANAPHUNZIRA M’BAIBULO ZINASINTHA MOYO WAWO

Mayi Cindi, omwe tawatchula kale aja ananena kuti: “A Joe ankaoneka kuti ndi anzeru, akhalidwe labwino komanso odzichepetsa.” Popeza a Cindi ndi a Mboni za Yehova, ankawapatsa a Joe magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Kenako anawaitanira ku mwambo wokumbukira imfa ya Yesu womwe a Mboni za Yehova amachita. A Joe anapitadi ndipo anaona kuti anthu ake anali okoma mtima komanso aulemu. Choncho anayamba kusonkhana ndi a Mboni mlungu uliwonse. Anavomeranso kuti aziphunzira Baibulo ndi wa Mboni wina wa mumpingomo.

Zimene Bambo Joe anaphunzira m’Baibulo zinawathandiza kwambiri

A Joe anasangalala kwambiri ndi zimene ankaphunzira m’Baibulo ndipo anayamba kuzigwiritsa ntchito pa moyo wawo. Anazindikira kuti akufunika kusintha zina ndi zina pa moyo wawo. Mwachitsanzo, anaphunzira kuti moyo ndi mphatso yamtengo wapatali yochokera kwa Mulungu. (Salimo 36:9) Anaphunziranso kuti kusuta kumaipitsa thupi. Choncho anatsatira malangizo a palemba la 2 Akorinto 7:1 ndipo anasiya kusuta. Lembali limati: “Tiyeni tidziyeretse ndipo tichotse chinthu chilichonse choipitsa thupi.” Izi zinathandiza kuti a Joe akhale ndi thanzi labwino komanso kuti asamawononge ndalama pogula fodya.

A Joe anamvetsanso mfundo ya m’Baibulo yomwe imanena kuti tiyenera kugwira ntchito mwakhama kuti tizipeza zofunika pa moyo. Choncho anayamba kufufuza ntchito. * (1 Atesalonika 4:11, 12) Lemba la Mlaliki 2:24 limati: “Kwa munthu, palibe chabwino kuposa kuti adye, amwe, ndi kusangalatsa mtima wake chifukwa choti wagwira ntchito mwakhama.” Munthu akamagwira ntchito yachilungamo amakhala wosangalala ngakhale ntchitoyo itakhala yooneka ngati yonyozeka. Munthu wotereyu angathenso kuthandiza anthu ovutika.—Aefeso 4:28.

Mayi Cindi anati: “Anthu a mumpingo mwathu ataona kuti a Joe asintha, anawathandiza kuti apeze nyumba komanso zinthu zina.” A Joe anapitiriza kuphunzira Baibulo ndipo kenako anabatizidwa n’kukhala a Mboni za Yehova. Panopa amafotokozera anthu mmene Baibulo linawathandizira ndipo amawalimbikitsa kuti nawonso azitsatira malangizo a m’Baibulo.—Miyambo 3:13, 14.

ANAYAMBA KUONA KUTI MOYO NDI WAPHINDU

Martín ali ndi zaka 20, ankafunitsitsa kudziwa ngati pali zomwe angachite kuti moyo wake ukhale waphindu. Ankachita zimenezi chifukwa cha vuto lake lija, loona kuti akusoweka chinachake pa moyo wake. Iye anati: “Ndinapita m’zipembedzo zosiyanasiyana komanso ndinawerenga mabuku osiyanasiyana. Ndiponso ndinayamba kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo. Koma zonsezi sizinathetse vuto langa.” Kenako anapita ku California m’dziko la United States, komwe anakhalako nthawi pang’ono, n’kusamukiranso ku Hawaii. Martín anati: “Malo amene ndinkakhala ku Hawaii ankandisangalatsa kwambiri chifukwa anali okongola kwabasi. Ndinkaganiza kuti ndiyamba kusangalala.” Koma patapita nthawi, Martín anaona kuti vuto lake lija lilipobe. Martín anati: “Ndinayamba kuvutika maganizo kwambiri moti ndinaganiza zongodzipha.” Pa nthawiyo ndi pamene anapemphera kwa Mulungu, uku akulira. Anapempha Mulungu kuti ngati alipodi, amuthandize kuti amudziwe.

Panopa Martín amaona kuti moyo wake ndi waphindu

Martín anakumbukira kuti tsiku lina anaona chikwangwani chomwe panalembedwa kuti, “Nyumba ya Ufumu ya Mboni za Yehova.”  Choncho anaganiza zopita ku Nyumba ya Ufumuyo. Martín anati: “Ndinapitako ndili ndi tsitsi lalitali komanso lanyankhalala. Ndinalinso ndi ndevu zosameta ndipo zovala zimene ndinavala zinali zakuda chifukwa ndinali nditazivala kwa miyezi yambiri. Koma ngakhale kuti ndinkaoneka chonchi, a Mboni anandilandira bwino kwambiri.” Atamupempha kuti ayambe kuphunzira Baibulo, anavomera. Martín ankayenda ulendo wautali kuchokera komwe ankakhala kupita m’tauni inayake, kuti akachite phunzirolo.

Martín anayamba kupeza mayankho a mafunso ake. Zimenezi zinamuthandiza kuti asiye kuvutika maganizo ndipo anayamba kusangalala. Anaona kuti zimene Yesu ananena palemba la Mateyu 5:3 ndi zoona. Palembali Yesu anati: “Odala ndi anthu amene amazindikira zosowa zawo zauzimu.”

‘Anthu anadabwa kwambiri ndi mmene zinthu zinasinthira pa moyo wanga’

Mofanana ndi a Joe, Martín anayamba kugwiritsa ntchito zimene ankaphunzira m’Baibulo ndipo anasintha kwambiri. Anameta tsitsi ndi ndevu zake, anasamuka kumene ankakhala kuja ndipo a Mboni anamuthandiza kupeza ntchito. Martín anati: “Poyamba anthu ankangondidziwa monga munthu wosowa pokhala. Koma nditayamba kuphunzira Baibulo, anadabwa kwambiri ndi mmene zinthu zinasinthira pa moyo wanga.”

Kenako, Martín anabwereranso kwawo ku Argentina, ndipo anakabatizidwa n’kukhala wa Mboni za Yehova. Panopa amathandizanso ena kudziwa za Mulungu kuti nawonso apeze mayankho a m’Baibulo a mafunso awo.

TIDZASANGALALA KWAMBIRI UMPHAWI KOMANSO VUTO LOSOWA POKHALA ZIKADZATHA

Yeremiya, yemwe anali mneneri wa Mulungu, anakhalapo m’nthawi yomwe m’dziko lawo munali mavuto ambiri. Asilikali ankhanza analanda dziko limene ankakhala ndipo anatenga anthu kupita nawo ku ukapolo. (Maliro 1:3) Ngakhale  kuti Yeremiya sanatengedwe nawo, anatsala wopanda chilichonse. Chifukwa chothedwa nzeru, anapemphera kwa Yehova kuti: “Kumbukirani kuti ndine wosautsika ndi wosowa pokhala.”—Maliro 3:19.

Koma sikuti Yeremiya ankangoganizira za mavuto akewo. Ankadziwa kuti Yehova sangamutaye. (Yeremiya 1:8) Ankakondanso kuwerenga Mawu a Mulungu, omwe amanena kuti umphawi komanso mavuto zidzatha ndipo anthu adzakhala mwamtendere komanso adzakhala ndi malo abwino okhala.—Salimo 37:10, 11.

Anthu sangakwanitse kuthetsa vuto losowa pokhala komanso umphawi. Mulungu yekha ndi amene adzachite zimenezi ndipo adzagwiritsa ntchito Ufumu wake. (Danieli 7:13, 14) Mfumu ya Ufumu umenewu ndi Yesu Khristu, ndipo pamene anali padziko lapansi ankathandiza anthu osauka. (Luka 7:22; 14:13) Yesu akamadzalamulira dzikoli, “wolungama adzaphuka, ndipo padzakhala mtendere wochuluka . . . adzalanditsa wosauka amene akufuula popempha thandizo, komanso wosautsika ndi aliyense wopanda womuthandiza. Adzawombola miyoyo yawo ku chipsinjo ndi chiwawa.”—Salimo 72:7, 12, 14.

“Adzamanga nyumba n’kukhalamo.”—Yesaya 65:21

Yesu ali padziko lapansi, ankakonda kulalikira za Ufumu wa Mulungu. (Luka 4:43) Anaphunzitsanso anthu kuti azipemphera kuti: “Ufumu wanu ubwere. Chifuniro chanu chichitike, monga kumwamba, chimodzimodzinso pansi pano.” (Mateyu 6:9, 10) Kodi zinthu zidzakhala bwanji padzikoli Ufumu wa Mulungu ukadzayamba kulamulira? Baibulo lingatithandize kudziwa mmene zidzakhalire. Mwachitsanzo, ponena za anthu amene adzakhale nzika za Ufumu wa Mulungu, limati:

  • “Adzamanga nyumba n’kukhalamo. Adzabzala minda ya mpesa n’kudya zipatso zake. Sadzamanga wina n’kukhalamo. Sadzabzala wina n’kudya. . . . Ndipo anthu anga osankhidwa mwapadera adzapindula mokwanira ndi ntchito ya manja awo.”—Yesaya 65:21, 22.

  • “Aliyense adzakhala pansi pa mtengo wake wa mpesa ndi mtengo wake wa mkuyu ndipo sipadzakhala wowaopsa, pakuti pakamwa pa Yehova wa makamu panena zimenezi.”—Mika 4:4.

Kuganizira zimenezi kungatithandize tikakumana ndi mavuto. Komanso Baibulo lingatithandize kukhala ndi moyo waphindu ngakhale panopa, ngati mmene linathandizira a Joe, Martín komanso anthu ena. Ndipotu Yehova, yemwe ndi Mlengi wathu, amatiuza kuti: “Munthu wondimvera adzakhala mwabata ndipo sadzasokonezeka chifukwa choopa tsoka.” (Miyambo 1:33) Inunso mukhoza kukhala m’gulu la anthu amenewa.

^ ndime 6 Zinthu monga mikangano, ziwawa kapena kuzunzidwa, zimachititsa anthu ena kuchoka panyumba pawo. Anthu oterewa amasowa pokhala m’dziko lawo lomwelo kapena m’dziko limene asamukira. Vuto limeneli lafotokozedwa mu Galamukani! ya February 8, 2002.

^ ndime 11 Anthu ena amafuna kugwira ntchito, koma amalephera chifukwa cha kulumala, matenda kapena ukalamba. Mulungu sadana ndi anthu oterewa koma amadana ndi amene ‘safuna kugwira ntchito.’—2 Atesalonika 3:10.