Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 ANTHU NDI MAYIKO

Dziko la Honduras

Dziko la Honduras

DZINA lakuti “Honduras” ndi lachisipanishi ndipo limatanthauza “kuya.” Dziko la Honduras lili m’mphepete mwa nyanja ya Atlantic. Zikuoneka kuti Christopher Columbus ankagwiritsa ntchito mawu akuti “Hondurus” ponena za kuya kwa madzi a m’nyanjayi. Anthu ena amanena kuti apa m’pamene dzina la dzikoli linachokera.

Anthu a ku Honduras amakhala okhulupirika m’banja komanso ogwirizana. Mwamuna ndi mkazi wake asanasankhe zochita, amakambirana kaye n’kugwirizana. Mwachitsanzo amakambirana pa nkhani zokhudza mmene azigwiritsira ntchito ndalama pakhomo pawo komanso sukulu zomwe angatumizeko ana awo.

Anthu ambiri a ku Honduras ndi Amesitizo. Makolo a Amesitizo ndi ochokera ku Europe ndi ku Honduras komweko. M’dzikoli mumapezekanso anthu otchedwa a Chortí ndipo iwowa ndi amene anali oyamba kukhala m’dzikoli. Kulinso anthu ena otchedwa Agarifuna amene makolo awo anali akuda komanso amwenye.

Munthu wachigarifuna akuimba ng’oma

 Poyamba makolo a Agarifuna ankakhala pachilumba chotchedwa St. Vincent. Mu 1797, Agarifuna anafika pazilumba za Bay. Kenako anakhazikika m’mbali mwa nyanja kudera lotchedwa Caribbean. Patapita nthawi, Agarifuna anafalikira m’chigawo chapakati ndi kumpoto kwa America.

Agarifuna amavina magule osiyanasiyana ndipo povina magulewa amaimba ng’oma. Amakondanso zovala zowala komanso kufotokozerana nkhani. Amakonda chakudya chotchedwa ereba, chomwe ndi keke yopyapyala yopangidwa ndi ufa wa chinangwa.

Ku Honduras kuli mipingo 400 ya Mboni za Yehova. Misonkhano yawo imachitika m’Chigarifuna, m’Chimandarini cha ku China, m’Chimisikito, m’chinenero chamanja cha ku Honduras, m’Chingelezi ndi m’Chisipanishi.

Chakudya chotchedwa ereba chopangidwa ndi ufa wa chinangwa