PACHIKUTO | KODI MOYO UNAYAMBA BWANJI?
Baibulo Lili Ndi Mayankho Ogwira Mtima
ANTHU ambiri akaganizira umboni womwe ulipo amaona kuti payenera kukhala winawake wanzeru amene analenga zonse. Pulofesa wina dzina lake Antony Flew, poyamba ankalimbikitsa chikhulupiriro choti kulibe Mulungu. Kenako anaphunzira zinthu zochititsa chidwi zokhudza moyo komanso kuti zinthu zakuthambo zimayenda motsatira malamulo enaake. Zimenezi zinapangitsa kuti asinthe maganizo ake. Flew analemba mfundo yomwe akatswiri akale anzeru za anthu ankaikhulupirira. Iye anati: “Tiyenera kuvomereza zotsatira za kafukufuku ngakhale zitakhala kuti n’zosiyana ndi zomwe timayembekezera.” Pulofesayu anaona kuti kafukufuku amasonyeza kuti pali winawake wanzeru amene analenga zinthu zonse.
Gerard, yemwe tamutchula m’nkhani yoyamba ija, nayenso anayamba kukhulupirira zimenezi. Iye anati: “Ndimaona kuti palibe umboni wokhutiritsa wosonyeza kuti zamoyo zinachita kusintha kuchokera ku zinthu zina. Zamoyo zimachita zinthu mwadongosolo komanso mogometsa kwambiri. Payenera kuti pali winawake amene anazilenga chifukwa zimenezi sizingangochitika zokha.”
Munthu akhoza kudziwa zambiri za katswiri wojambula zithunzi poona zimene katswiriyo anajambula. Nayenso Gerard anayamba kudziwa makhalidwe amene Mulungu ali nawo poona zimene Mulunguyo analenga. Anaphunziranso zambiri za Mulungu kudzera m’Mawu ake, Baibulo. (2 Timoteyo 3:16) Zinthu zina zimene anaphunzira m’Baibulo ndi mfundo zomveka bwino zonena za anthu oyambirira komanso zimene munthu angachite ngati akukumana ndi mavuto. Zimenezi zinamupangitsa kutsimikizira kuti Baibulo ndi Mawudi a Mulungu.
M’Baibulo muli mayankho ogwira mtima a mafunso osiyanasiyana. Tikukulimbikitsani kuti inunso muliphunzire ndipo mudzapeza mayankho a mafunso osiyanasiyana omwe muli nawo.