Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 NKHANI YA PACHIKUTO | KODI MUMAONERA CHIYANI KUTI MUNTHU ZIKUMUYENDERA?

Ndani Amene Mungati Zinthu Zikumuyenderadi?

Ndani Amene Mungati Zinthu Zikumuyenderadi?

Kuti muone ngati mumadziwadi munthu amene zikumuyendera bwino kapena ayi, taganizirani zitsanzo zotsatirazi.

Pa anthu otsatirawa ndi ndani amene mungati zinthu zikumuyenderadi?

 • ALEX

  Alex ali ndi bizinezi yaikulu, ndi wolimbikira ntchito, amachita zinthu moona mtima komanso ndi waulemu. Bizinezi yake ikuyenda bwino ndipo iye ndi banja lake amakhala mosangalala.

 • CAL

  Cal nayenso ali ndi bizinezi yaikulu ndipo amapeza ndalama zambiri kuposa Alex. Kuti azipeza phindu lochuluka amangokhalira kugwira ntchito ndipo zimenezi zimam’pangitsa kuti azidwala matenda osiyanasiyana.

 • JANET

  Janet amalimbikira kwambiri sukulu komanso amakonda kuphunzira zinthu. Chifukwa cha zimenezi iye amakhoza bwino m’kalasi.

 • ELLEN

  Ellen nayenso ali pa sukulu ndipo amakhoza bwino kuposa Janet moti amaonedwa kuti ali m’gulu la ana anzeru kwambiri ku sukulu yawo. Koma Ellen amaonera mayeso ndipo sakonda kwenikweni maphunziro.

Kodi mukuona kuti Cal ndi Ellen ndi omwe zikuwayendera? Kapena mukuona kuti anthu 4 onsewa zikuwayendera bwino? Ngati mukuona choncho, ndiye kuti mumaona kuti munthu zikumuyendera pongoona zimene akukwanitsa kuchita osaganizira zomwe akuchita kuti akwanitse zinthuzo.

Koma ngati mukuona kuti Alex ndi Janet ndi omwe zikuwayendera bwino, ndiye kuti mumaona kuti munthu zikumuyendera poona khalidwe lake, ngati amachita zinthu molimbikira komanso ngati amachita zinthu moyenera. Ndipotu zimenezi n’zomveka. Mwachitsanzo taganizirani izi:

 • Kodi n’chiyani chimene chingadzamuthandize Janet? Kodi ndi kukhoza kwambiri m’kalasi kapena mtima wokonda kuphunzira zinthu?

 • • Kodi n’chiyani chingathandize kuti ana a Alex azikhaladi osangalala? Zinthu zodula zimene bambo awo angawagulire kapena kukhala ndi bambo amene amapeza nthawi yocheza nawo komanso kuchita nawo zinthu zina?

Mfundo yofunika kwambiri ndi yoti: Si bwino kuganiza kuti munthu zikumuyendera pongoona zimene akukwanitsa kuchita. Tingadziwe kuti munthu zikumuyendera poona khalidwe lake, ngati amachita zinthu molimbikira komanso ngati amachita zinthu moyenera.