Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 KODI ZINANGOCHITIKA ZOKHA?

Miyendo ya Hatchi

Miyendo ya Hatchi

HATCHI imathamanga pa liwiro la mtunda wa makilomita 50 pa ola limodzi. Ngakhale kuti pamachitika zambiri kuti hatchi izitha kuthamanga mofulumira chonchi, n’zochititsa chidwi kuti sigwiritsa ntchito mphamvu zambiri. Kodi zimenezi zimatheka bwanji? Chinsinsi chake chagona pa miyendo yake.

Taganizirani zimene zimachitika hatchi ikamathamanga. M’mawondo mwake muli minofu ndi minyewa yangati sipuling’i. Ndipo izi zimachititsa kuti miyendoyi ikaponda pansi izifwamphuka mwamphamvu n’kupita m’tsogolo.

Komatu mmene hatchi imathamangiramu ikhoza kudzivulaza minyewa ya m’miyendo yake. Koma n’zochititsa chidwi kuti sivulala chifukwa minofu ya m’mawondo ake imateteza minyewayi. Akatswiri amati “mawondo a hatchi anapangidwa mogometsa kwambiri” ndipo amathandiza kuti miyendo ya hatchi ikhale yolimba komanso yamphamvu.

Akatswiri opanga zinthu akufuna kutengera miyendo ya hatchi kuti apange maloboti a miyendo 4. Komabe panopa akatswiri sangakwanitse kupanga loboti potengera miyendo ya hatchiyi. Izi zili choncho malinga ndi zimene bungwe lina loona za luso lopanga zinthu zamakono potengera zam’chilengedwe linanena. Bungweli linati panopa akatswiriwa alibe zipangizo zoti angathe kugwirira ntchito imeneyi. Vuto linanso ndi loti padakali pano akatswiriwa sakudziwa zambiri pa nkhaniyi.

Kodi inuyo mukuganiza bwanji? Kodi zinangochitika zokha kuti miyendo ya hatchi izitha kuchita zimenezi, kapena pali winawake amene anailenga?