Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 NKHANI YA PACHIKUTO

Kodi Zionetsero Zimathetsadi Mavuto M’dziko?

Kodi Zionetsero Zimathetsadi Mavuto M’dziko?

A Mboni za Yehova, omwe amafalitsa magazini ino salowerera ndale. (Yohane 17:16; 18:36) Ngakhale kuti nkhaniyi ifotokoza mavuto azandale omwe achitika m’mayiko ena, siikusonyeza kuti a Mboni za Yehova amaikira kumbuyo dziko lililonse kapena kulowerera nawo m’nkhani iliyonse yokhudza ndale.

PA DECEMBER 17, 2010, munthu wina wa zaka 26, dzina lake Mohamed Bouazizi, anadziwotcha chifukwa chotopa ndi mavuto. Mohamed ankachita bizinezi yogulitsa mapeyala, nthochi ndi maapozi mumsewu ku Tunisia. Iye anayesetsa kufunafuna ntchito koma sankaipeza. Kuwonjezera pamenepo, Mohamed ankadziwanso kuti akuluakulu a boma ndi okonda ziphuphu. M’mawa wa tsiku limene anadziwotchalo, oyang’anira mzinda analanda katundu amene Mohamed ankagulitsa. Anthuwo ankafuna kumulandanso masikelo amene ankagwiritsa ntchito pogulitsa zinthuzo koma iye anakaniza. Ena amene anaona zimenezi zikuchitika ananenanso kuti anaona wapolisi wina wamkazi akum’menya Mohamed mbama.

Mohamed anachita manyazi ndi zimenezi ndipo anakwiya kwambiri moti anapita ku ofesi ina yaboma kukadandaula koma sanamuthandize. Ena amati anatuluka panja pa ofesiyo n’kukuwa kuti: “Ndiye mukuganiza kuti ineyo nditani? Ndisamalira bwanji banja langa?” Kenako anadzithira petulo n’kudziyatsa ndi machesi. Mohamed anapsa kwambiri ndipo anamwalira patatha milungu itatu.

Zimene Mohamed Bouazizi anachita zinakhudza kwambiri anthu a ku Tunisia komanso a m’mayiko ena. Ambiri amakhulupirira kuti zimene Mohamed anachita n’zimene zinapangitsa anthu kuyamba kuchita zionetsero zomwe zinachititsa kuti pulezidenti wadzikolo atule pansi udindo wake. Zinachititsanso kuti mayiko ena a ku Arabia ayambe kuchita zionetsero. Nyumba ya malamulo ya ku Ulaya inapatsa Bouazizi komanso anthu ena 4 omwe anafa podziotcha, mendulo ya ulemu yotchedwa 2011 Sakharov chifukwa chomenyera ufulu wonena maganizo awo. Komanso nyuzipepala ina ya ku London, yotchedwa The Times, inanena kuti Mohamed anachita zinthu zapadera kwambiri m’chaka cha 2011.

Zimene zinachitikazi zikusonyeza kuti nthawi zina zionetsero zingathe kusintha zinthu. Koma n’chifukwa chiyani masiku ano anthu akumakonda kuchita zionetsero? Kodi pali njira zina zothetsera mavuto kupatulapo kuchita zionetsero?

 N’chifukwa Chiyani Anthu Akukonda Kuchita Zionetsero?

Nthawi zambiri anthu amakonda kuchita zionetsero pa zifukwa zotsatirazi:

  • Kukwiya ndi mmene boma likuyendetsera zinthu. Anthu akaona kuti boma likuwachitira zimene amafuna samaganiza zochita zionetsero. Pakakhala mavuto anthu amangouza oimira boma kuti akanene mavuto awowo ku boma. Koma ngati akuona kuti anthu a m’boma akuchita zachinyengo, zopanda chilungamo komanso zokondera, amayamba kuchita zionetsero.

  • Pamakhala chinachake chimene chachititsa. Nthawi zambiri pakachitika chinachake, anthu amaona kuti akufunika achitepo kanthu. Mwachitsanzo, zimene Mohamed Bouazizi anachita zinachititsa kuti anthu ayambe kuchita zionetsero ku Tunisia. Ndipo ku India, bambo wina dzina lake Anna Hazare, anasala kudya pokwiya ndi zachinyengo zimene zinkachitika. Zimenezi zinapangitsa kuti anthu omutsatira ayambitse zionetsero m’matauni ndi m’mizinda yokwana 450.

Baibulo linaneneratu kalekale kuti tikukhala m’nthawi imene ‘anthu akupweteka anthu anzawo powalamulira.’ (Mlaliki 8:9) Zinthu zopanda chilungamo komanso zachinyengo n’zofala kwambiri masiku ano. Anthu akuchita kuoneratu kuti andale komanso mabungwe azachuma awagwiritsa mwala. Zimene anthu amaona m’mafoni, pa Intaneti, pa TV komanso kumvera pa wailesi, zimapangitsa kuti azitha kuona zinthu zimene zikuchitika kulikonse. Zimenezi zimachititsanso kuti zionetsero zizichitikachitika.

Kodi zionetsero zathandizadi kuthetsa mavuto?

Anthu amene amalimbikitsa zionetsero amanena kuti zionetsero:

  • Zathandiza kuthetsa umphawi. M’zaka za m’ma 1930, ku America, m’chigawo cha Illinois, mumzinda wa Chicago, anthu anachita zionetsero chifukwa chouzidwa kuti atuluke m’nyumba za lendi. Anthuwa sankalipira ndalama za lendi chifukwa sanali pa ntchito. Atapanga zionetsero, akuluakulu a mumzindawo anawauza kuti asatuluke m’nyumbazo komanso anapezera ntchito anthu ena omwe ankapanga zionetserozo. Zofanana ndi zimenezi zinachitikanso mumzinda wa New York City, ndipo mabanja okwana 77, 000 anabwerera m’nyumba zawo.

  • Zathandiza kusintha malamulo opondereza. M’chaka cha 1955 ndi 1956, anthu akuda a mu mzinda wa Montgomery ku Alabama, m’dziko la America, anayamba kunyanyala kukwera mabasi pokwiya chifukwa chakuti munthu wina wakuda anamangidwa atakana kupereka malo amene anakhala m’basi kwa mzungu. Zimenezi zinachititsa kuti boma lisinthe malamulo okhudza mmene anthu akuda ndi azungu azikhalira m’basi.

  • Zathandiza kusiyitsa boma ntchito zimene anthu sakugwirizana nazo. Mu December 2011, anthu masauzande ambiri anachita zionetsero pofuna kuletsa kumangidwa kwa kampani yopanga mphamvu za magetsi pogwiritsa ntchito malasha, yomwe ili pafupi ndi mzinda wa Hong Kong, m’dziko la Japan. Iwo ankaona kuti kampaniyi ingadzawonongetse zachilengedwe monga mpweya. Chifukwa cha zimenezi analamula kuti ntchito yomanga kampaniyi iime.

Ngakhale kuti kuchita zionetsero kumathetsa mavuto ena, Ufumu wa Mulungu ndi umene udzathetseretu mavuto onse

 Koma si nthawi zonse pamene zionetsero zimathandiza kuthetsa mavuto. Nthawi zina akuluakulu a boma amatha kukhaulitsa anthu m’malo mowachitira zimene akufuna. Chaposachedwapa, pulezidenti wina wa dziko la ku Middle East, kumene kunali zionetsero, ananena kuti: “Anthu amenewa ndi ofunika kuwakhaulitsa,” ndipo anthu masauzande ambiri anaphedwa chifukwa cha zimenezi.

Ngakhale kuti kuchita zionetsero kumathetsa mavuto ena, zoona zake n’zakuti kumabweretsanso mavuto. Munthu wina amene anachita nawo zionetsero zoti pulezidenti wina wa ku Africa atule pansi udindo wake, anauza mtolankhani wa magazini ya Time kuti: “Pulezidenti watsopano atangoyamba kulamulira, zinthu zinkaoneka ngati ziyamba kuyenda bwino. Koma mapeto ake zinkangoipiraipira.”

Kodi pali njira yabwino yothetsera mavuto?

Anthu ambiri odziwika amaona kuti ngati boma likuchita zinthu zopondereza, si kulakwa kuchita zionetsero. Mwachitsanzo, pulezidenti wakale wa ku Czech yemwe anamwalira, dzina lake Václav Havel, anatsekeredwa m’ndende chifukwa chochita zionetsero zomenyera ufulu wa anthu. M’chaka cha 1985, iye analemba kuti: “Munthu akamachita nawo zionetsero amakhala wokonzeka kufa pofuna kusonyeza boma kuti zimene bomalo likuchita n’zolakwika.”

Zimene ananena Havel zikusonyeza maganizo amene Mohamed Bouazizi komanso anthu ena anali nawo.  M’dziko lina la ku Asia, anthu ambiri anadziwotcha pochita zionetsero atakhumudwa ndi zimene atsogoleri a zipembedzo komanso andale ankachita. Munthu wina anauza mtolankhani wa magazini ya Newsweek chifukwa chake anthu amenewa anadziwotcha. Iye ananena kuti: “Tilibe mfuti komanso sitikufuna kuvulaza anthu ena. Njira yachidule n’kungodzipha basi.”

Baibulo limafotokoza amene adzathetse zinthu zopanda chilungamo, katangale komanso kuponderezana. Limanena za boma limene Mulungu analikhazikitsa kumwamba, lomwe lidzalowe m’malo mwa maboma onse alipowa. Ulosi umanena za Wolamulira wa boma limeneli kuti: “Adzalanditsa wosauka wofuulira thandizo, komanso wosautsika ndi aliyense wopanda womuthandiza. Adzawombola miyoyo yawo ku chipsinjo ndi chiwawa.”—Salimo 72:12, 14.

A Mboni za Yehova amakhulupirira kuti Ufumu wa Mulungu ndi umene udzabweretse mtendere padzikoli. (Mateyu 6:9, 10) N’chifukwa chake a Mboni za Yehova sachita nawo zionetsero. Koma kodi n’zomveka kukhulupirira kuti Ufumu wa Mulungu udzathetsa mavuto onse omwe amapangitsa anthu kuchita zionetsero? Mwina zingaonekedi ngati n’zosamveka. Komatu pali anthu ambiri amene amakhulupirira kuti Ufumu wa Mulungu udzathetsa mavuto amenewa. Inunso mungachite bwino mutafufuza za Ufumu umenewu.