Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 KODI ZINANGOCHITIKA ZOKHA?

Gologolo wa Ubongo Wodabwitsa Kwambiri

Gologolo wa Ubongo Wodabwitsa Kwambiri

PALI mtundu wina wa agologolo amene amapezeka ku madera ozizira kwambiri. Gologoloyu amagona m’nyengo yonse yozizira usana ndi usiku. Pa nthawi imene akugona, thupi lake limazizira kwambiri mpaka kufika madigiri -2.9. Kuzizira kumeneku kukhoza kuchititsa kuti ubongo wake uume ndipo akhoza kufa. Koma kodi n’chiyani chimachititsa kuti gologoloyu asafe ndi kuzizira?

Taganizirani izi: Kwa milungu iwiri kapena itatu iliyonse yomwe wakhala akugona, gologoloyu amanjenjemera n’cholinga choti thupi lake litenthe kufika madigiri 36.4. Ndipo thupilo siliziziranso mpaka patadutsa maola pafupifupi 15. Akatswiri ofufuza amanena kuti zimenezi zimathandiza kuti ubongo wa gologolo usaume. Komanso chodabwitsa kwambiri n’chakuti pa nthawi imene akugona, mutu wake sumazizira kwambiri poyerekeza ndi thupi lonse. Ofufuza atatenga gologoloyu kuti amuyeze anapeza kuti khosi lake silimazizira kuposa madigiri 0.7.

Gologoloyu akadzuka ubongo wake umayambanso kugwira ntchito bwinobwino pakangotha maola awiri. Ndipo kafukufuku wina anasonyeza kuti ubongo wake umagwira ntchito bwino kwambiri akadzuka. Asayansi amachita chidwi kwambiri ndi mmene ubongo wa gologoloyu umagwirira ntchito.

Iwo akuona kuti akhoza kuphunzira zambiri pa mmene ubongo wa gologoloyu umagwirira ntchito, zomwe zingawathandize kudziwa zinthu zina zimene ubongo wa munthu ungachite. Kudziwa zambiri za ubongo wa gologoloyu kungawathandize kupewa vuto la kuwonongeka kwa maselo a muubongo kapena kukonza maselo amene awonongeka chifukwa cha matenda ngati Alzheimer.

Kodi inuyo mukuganiza bwanji? Kodi zinangochitika zokha kuti ubongo wa gologoloyu uzigwira ntchito chonchi, kapena pali winawake amene anaulenga?