Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Zoti Banja Likambirane

Zoti Banja Likambirane

KODI TIKUPHUNZIRA CHIYANI KWA . . . Abulahamu?

KODI MUMAONA KUTI NDIBWINO KUCHITIRA ENA CHIFUNDO?

• Kongoletsani zithunzizi ndi chekeni. • Werengani mavesiwa ndipo muwafotokoze pomalizitsa mawu amene akusoweka. • Pezani zinthu zimene zikusoweka: (1) buluzi ndi (2) mpeni.

Kodi Abulahamu atalandira alendo anawachitira zinthu zachifundo ziti?

ZOKUTHANDIZANI: Genesis 18:2, 4, 5.

Kodi mungatani kuti muzisonyeza ena chifundo?

ZOKUTHANDIZANI: Aroma 12:13.

Kodi mwaphunzirapo chiyani pa nkhani imeneyi?

Kodi inuyo mukuganiza bwanji?

Kodi tiyenera kuchitira chifundo makamaka ndani?

ZOKUTHANDIZANI: Agalatiya 6:10.

 Sungani Kuti Muzikumbukira

KHADI LA BAIBULO 24 SAMISONI

MAFUNSO

  1. A. Dzina la bambo ake linali․․․․․.

  2. B. Kodi Samisoni anachita zotani ku Gaza?

  3. C. Ndani anamupereka Samisoni kwa Afilisiti?

ANALI NDANI

Woweruza amene anatsogolera Isiraeli kwa zaka 20. (Oweruza 15:20) Yehova anagwiritsa ntchito Samisoni “populumutsa Isiraeli m’manja mwa Afilisiti.” (Oweruza 13:5) Mzimu wa Mulungu unamupatsa mphamvu ndiponso ankakhulupirira kwambiri Yehova.​—Aheberi 11:32-34.

MAYANKHO

  1. A. Manowa.​—Oweruza 13:8, 24.

  2. B. Anagwira zitseko za chipata cha mzinda pamodzi ndi nsanamira zake ziwiri, n’kuzizula pamodzi ndi mpiringidzo wake. Kenako anapita nazo pamwamba pa phiri limene linali moyang’anizana ndi Heburoni.—Oweruza 16:2, 3.

  3. C. Delila.—Oweruza 16:4, 5.

Anthu ndi Mayiko

Mayina athu ndi Lesly, Cathleen ndi Alondra ndipo tili ndi zaka 10, 8 ndi 7. Timakhala ku Mexico. Kodi mukudziwa kuti ku Mexico kuli Mboni za Yehova zingati? Kodi ziliko 295,400, 455,000, kapena 724,700?

Kodi ndi kadontho kati kamene kakusonyeza dziko limene ifeyo timakhala? Lembani mzere wozungulira kadonthoko. Kenako jambulani kadontho kosonyeza kumene inuyo mumakhala, kuti muone kuyandikana kwa dziko lanu ndi la Mexico.

Zithunzi Zoti Ana Apeze

Pezani zithunzi izi m’magazini ino. Fotokozani zimene zikuchitika pa chithunzi chilichonse.

 MAYANKHO A MAFUNSO

  1. Buluzi ali pachithunzi chachisanu.

  2. Mpeni uli pachithunzi chachiwiri.

  3. 724,700.

  4. A.