Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mavuto Amene Amabwera Chifukwa Chosaleza Mtima

Mavuto Amene Amabwera Chifukwa Chosaleza Mtima

PALI maumboni ambiri osonyeza kuti anthu sakumaleza mtima. Mwachitsanzo tayerekezerani kuti mukuona anthu awiri akuyendetsa galimoto mondondozana kwambiri. Wapatsogoloyo akuyendetsa paliwiro lovomerezeka koma amene ali pambuyoyo akuona kuti wapatsogoloyo akuchedwa kwambiri. Chifukwa chosaleza mtima, wapambuyo uja akupitirira mwaliwiro wapatsogoloyo ngakhale kuti pamalopo salola kupitirira galimoto ina. Zimenezi zikhoza kuchititsa ngozi.

Mwina mumadziwanso munthu winawake amene sakonda kugwira ntchito ndi anthu omwe amawaona kuti saganiza mofulumira. Kapena munaonapo munthu akugogoda kwambiri pachitseko poona kuti anthu odzamutsegulira akuchedwa. Palinso anthu ena omwe amafuna kuti makolo awo achikulire kapena ana awo aang’ono azichita zinthu mofulumira. Komanso anthu ena sachedwa kukhumudwa anzawo akawalakwira.

N’zoona kuti nthawi zina aliyense amachita zinthu mosaleza mtima. Koma munthu amene nthawi zonse amangofuna kuti zinthu  zizichitika mofulumira komanso mmene akufunira amakumana ndi mavuto aakulu.

Kuwonongeka kwa thanzi

Munthu amene saleza mtima sachedwa kukhumudwa, amachita zinthu monyinyirika ndipo nthawi zambiri sachedwa kupsa mtima. Zimenezi zingachititse kuti adwale. Kafukufuku waposachedwapa amene bungwe lina linachita anasonyeza kuti anthu ambiri omwe amachita zinthu mosaleza mtima amadwala matenda othamanga magazi ndipo zimenezi zimachitika ngakhale kwa achinyamata.—American Medical Association.

Komanso nyuzipepala ina inanena kuti: “Anthu amene saleza mtima akhoza kunenepa kwambiri poyerekezera ndi amene amachita zinthu moleza mtima.” (The Washington Post) M’mayiko ena, anthu amene safuna kudikira amakonda kudya zakudya za m’malesitanti zonenepetsa kwambiri chifukwa n’zimene zimapezeka nthawi zonse komanso sizichedwa kubwera akaitanitsa.

Kuzengereza kuchita zinthu

Kafukufuku amene bungwe lina linachita anasonyeza kuti anthu osaleza mtima amakonda kuzengereza pochita zinthu. N’kutheka kuti amachita zimenezi akaona kuti ntchito ina imene akufunika kugwira iwatengera nthawi yaitali kuti aimalize. Komabe kuzengereza pochita zinthu kumabweretsa mavuto aakulu kwa munthuyo komanso kungawonongetse ndalama. Nyuzipepala ina ya ku Britain, inanena mawu amene katswiri wina wofufuza zinthu, dzina lake Ernesto Reuben, ananena. Iye anati: “Kuzengereza pogwira ntchito kumachititsa kuti kampani isamapindule ndipo kungawonongetse ndalama zambiri chifukwa [anthu osaleza mtima] amazemba ntchito zimene zimatenga nthawi yaitali.”—The Telegraph.

Kumwa mowa mwauchidakwa komanso kuchita zachiwawa

Nyuzipepala inanso ya ku Britain inalemba za kafukufuku amene akatswiri anachita pa yunivesite ya Cardiff m’dziko lomwelo. Kafukufukuyu anasonyeza kuti: “Kawirikawiri anthu osaleza mtima amakonda kumwa mwauchidakwa ndiponso kuyambitsa ndewu akaledzera.”—South Wales Echo.

Kuchita zinthu mosaganiza

Akatswiri a bungwe lina ku Washington, D.C m’dziko la United States, anapeza kuti anthu omwe saleza mtima “amakonda kuchita zinthu mopupuluma.” (Pew Research Center) Dr.  Ilango Ponnuswami, yemwe ndi mkulu wa dipatimenti ina pa yunivesite ya Bharathidasan ku India, ananena kuti: “Kusaleza mtima kungachititse kuti muwononge ndalama zambiri, muzisowa wocheza naye komanso kuti mukumane ndi mavuto osiyanasiyana. Zili choncho chifukwa munthu wosaleza mtima sasankha zinthu mwanzeru.”

Mavuto azachuma

Chikalata chimene banki ina yaikulu mu mzinda wa Boston, ku United States inatulutsa, chinasonyeza kuti nthawi zambiri anthu osaleza mtima amakhala ndi ngongole zambiri. Mwachitsanzo, anthu ambiri amene angokwatirana kumene amafuna kuti m’nyumba mwawo mukhale chilichonse ngakhale kuti amakhala alibe ndalama zokwanira. Choncho iwo amagula nyumba, katundu wam’nyumba, magalimoto ndi zinthu zina zambiri pa ngongole. Zimenezi zimabweretsa mavuto aakulu m’banja. Akatswiri ofufuza a pa yunivesite ya Arkansas m’dziko la United States, ananena kuti: “Anthu amene amalowa m’banja ndi ngongole amakhala osasangalala poyerekeza ndi amene amalowa alibe ngongole kapena ali ndi ngongole zochepa.”

Ena amanena kuti mavuto azachuma omwe anachitika ku United States anayamba chifukwa choti anthu ankachita zinthu mosaleza mtima. Magazini ya Forbes inanena kuti: “Mavuto azachuma anachitika chifukwa chakuti anthu anachita zinthu mosaleza mtima komanso mwadyera. Mwachitsanzo, chifukwa cha kusaleza mtima, anthu ambiri anagula nyumba zodula pa ngongole. Kuti alipire nyumbazo anabwereka ndalama zambiri ku mabanki ndipo ndalamazo zinali zoti zingawatengere zaka zambiri kuti azibweze kapenanso sangazibweze n’komwe.”

Anzako amasiya kucheza nawe

Kusaleza mtima kungachititse kuti munthu asamalankhule bwino. Mwachitsanzo munthu wosaleza mtima amangolankhula mosaganizira. Komanso sachedwa kukhumudwa akamalankhula ndi ena. Munthu wotereyu safuna kudikira kuti anzake afotokoze bwinobwino zimene akufuna kunena. Choncho amafuna kuti anzakewo amalize msanga kulankhula. Iye angachite zimenezi pomalizitsa zimene munthu wina akufuna kunena kapena kupeza njira iliyonse yoti munthuyo amalize kulankhula mwamsanga.

Zimenezi zingachititse kuti anthu asamakonde kucheza naye. Dr. Jennifer Hartstein, yemwe ndi dokotala wamatenda amaganizo, ndipo tamutchula mu nkhani yapita ija ananenanso kuti: “Palibe amene angakonde kucheza ndi munthu yemwe nthawi zonse amafuna kuti anzake azichita zinthu mofulumira.” Zimenezi zikusonyeza kuti kusaleza mtima ndi khalidwe lachabe chifukwa lingachititse kuti anthu asamakonde kucheza nanu.

Amenewa ndi ena mwa mavuto amene amabwera chifukwa chochita zinthu mosaleza mtima. Nkhani yotsatira ifotokoza zimene mungachite kuti muzichita zinthu moleza mtima.