Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Muzikhala ndi Cholinga

Muzikhala ndi Cholinga

Munthu amalimbikira komanso kusangalala ndi sukulu ngati akudziwa phindu lake.

MUNTHU amene akuphunzira popanda cholinga chilichonse amakhala ngati munthu amene akungothamanga osadziwa kumene akupita. N’chifukwa chake Baibulo limanena kuti: “Salaza njira ya phazi lako,” kutanthauza kuti tizidziwa kumene tikupita. (Miyambo 4:26) Kukhala ndi cholinga kungakuthandizeni kuti mukadzamaliza sukulu musadzavutike kuzolowera moyo wapantchito. Ndiyeno mungatani kuti mukhale ndi cholinga?

Dzifunseni kuti, ‘Kodi ndizidzagwira ntchito yanji?’ Simuyenera kuzengereza kupeza yankho la funso limeneli chifukwa zingakuthandizeni kuyamba kukonzekera panopa. Mwachitsanzo, ngati mukufuna kunyamuka ulendo winawake, choyamba mungafunike kudziwa kumene mukupita. Kenako mungafunike kuyang’ana pa mapu kuti mudziwe mmene mungakafikire kumaloko. Mungachitenso chimodzimodzi ndi sukulu. Choyamba, ganizirani ntchito imene mukufuna kuti mudzagwire kenako sankhani kosi yogwirizana ndi ntchito imene mukufunayo.

Chenjezo: Achinyamata ambiri amafuna kudzagwira ntchito yokhayo imene amailakalaka, monga kudzakhala woimba wotchuka, ndipo amaona kuti sangagwire ntchito zina. Koma kodi tiyenera kuiona bwanji nkhani imeneyi?

  1. Ganizirani zinthu zimene mumakwanitsa. Mwachitsanzo, kodi mumasangalala kugwira ntchito zothandiza anthu? Kapena muli ndi luso la zopangapanga, la masamu, la zachuma kapena kukonza zinthu zowonongeka?

  2. Ganizirani ntchito zimene mungagwire. Kodi ndi ntchito ziti zimene zikugwirizana ndi zimene inuyo mumakwanitsa? Ganizirani ntchito zambirimbiri m’malo momangoganizira imene mumailakalaka. Komanso ngati mutati mwasamukira kudera lina, kodi ntchito imeneyo mungakaipeze mosavuta? Kodi kosi imene mukufuna ingachititse kuti mukhale ndi ngongole zambiri?

  3. Ganizirani amene angakulembeni ntchito. Mukasankha ntchito imene mukufuna kudzagwira, ganiziraninso amene angakulembeni ntchito m’dera lanu. Kodi mukudziwapo aliyense amene angadzakulembeni? Ngati alipo, kodi angalole kuti muzikagwirako ntchito pa nthawi imene muli pa sukulu? Kodi pali makampani amene amaphunzitsa ntchito imene mukufunayo?

Mfundo yothandiza: Funsani makolo anu, aphunzitsi komanso anzanu achikulire. Mungakafufuzenso za ntchito imene mukufunayo ku laibulale kapena pa Intaneti.

Mfundo yofunika kuikumbukira: Kukhala ndi cholinga kungakuthandizeni kuti muzilimbikira komanso kuti muzisankha zinthu mwanzeru.

Yambani kutsatira malangizo amenewa. Pa nthawi imene mudakali pa sukulu, ganizirani mfundo zitatu zimene takambiranazi. Lembani zolinga zanuzo ndipo mukambirane ndi makolo anu.