Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mungatani Kuti Mukhale Kholo Labwino?

Kodi Mungatani Kuti Mukhale Kholo Labwino?

Kodi mungakumbukire nthawi imene munanyamula mwana wanu wakhanda kwa nthawi yoyamba?

Mwina pasanapite nthawi munayamba kuganizira za udindo waukulu umene munali nawo wolera mwanayo kwa zaka zambiri.

KUYAMBIRA kale, makolo amadziwa kuti kulera ana ndi udindo waukulu ndipo zimenezo ndi zoona makamaka masiku ano. N’chifukwa chiyani zili choncho? N’chifukwa chakuti masiku ano zinthu zinasintha kwambiri kuposa mmene zinalili pa nthawi yomwe munali mwana. Pa nthawi imeneyo kunalibe zinthu monga Intaneti yomwe ingachititse kuti ana akhale ndi makhalidwe oipa.

Ndiye kodi mungathandize bwanji mwana wanu kuti athane ndi mavuto amene angakumane nawo masiku ano? Taonani mfundo zitatu zimene mungatsatire.

1 Muziwauza momveka bwino mfundo zomwe mumatsatira.

Ana akamakula amauzidwa zinthu zambiri zolakwika mwina ndi anzawo kapena amazimva m’nyimbo ndi mafilimu amene amaonera. Iwo amayamba kuonetsa makhalidwe oipa amenewa makamaka akafika zaka zapakati pa 13 mpaka 19. Komabe kafukufuku amasonyeza kuti ana ambiri achinyamata akafuna kusankha zochita, amayendera mfundo zimene makolo awo amayendera.

Zimene mungachite. Kale, makolo a ku Isiraeli analangizidwa kuti azicheza ndi ana awo kawirikawiri n’cholinga choti aziwaphunzitsa makhalidwe abwino. (Deuteronomo 6:6, 7) Muzichitanso zimenezi ndi ana anu. Mwachitsanzo ngati mumatsatira mfundo za m’Baibulo, auzeni ana anu chifukwa chimene mumaonera kuti kutsatira mfundo zimenezo n’kothandiza.

2 Athandizeni kudziwa zotsatirapo za zochita zawo.

Baibulo limanena kuti: “Chilichonse chimene munthu wafesa, adzakololanso chomwecho.” (Agalatiya 6:7) Mfundo yakuti munthu amakolola zimene wafesa timaiona pa zinthu zambiri pa moyo wathu. Mwachitsanzo taganizirani pa nthawi yomwe munali mwana. N’zosakayikitsa kuti zinthu zimene mumakumbukira kwambiri ndi zomwe munaphunzira mutalakwitsa zinazake.

Zimene mungachite. Pogwiritsa ntchito zitsanzo za zinthu zomwe zinachitikadi, afotokozereni ana anu za anthu amene anachita zoipa ndi mavuto amene anakumana nawo, kapena za anthu amene anachita zabwino ndi madalitso amene anapeza. (Luka 17:31, 32; Aheberi 13:7) Komanso mwana wanu akakumana ndi mavuto chifukwa cha zimene walakwitsa, muzimusiya kuti athane nawo yekha. Mwachitsanzo, ngati wawononga mwadala chidole cha mnzake, mungamuuze kuti atenge chidole chake n’kukapereka kwa mnzakeyo. Zimenezi zingamuthandize kuti azisamalira zinthu za ena.

3 Athandizeni kukhala ndi makhalidwe abwino.

Baibulo limati: “Mnyamata [kapena mtsikana] amadziwika ndi ntchito zake, ngati zochita zake zili zoyera ndiponso zowongoka.” (Miyambo 20:11) Ana akamakula amakhala ndi khalidwe linalake limene amadziwika nalo. Koma n’zomvetsa chisoni kuti ana ena amadziwika ndi makhalidwe oipa. (Salimo 58:3) Komabe ena amakula ndi makhalidwe abwino omwe anthu ena amayamikira. Mwachitsanzo, mtumwi Paulo analembera kalata mpingo wa ku Filipi, yonena za mnyamata wina dzina lake Timoteyo. Iye anati: “Ndilibe wina wamtima ngati iye, amene angasamaledi za inu moona mtima.”​—Afilipi 2:20.

Zimene mungachite. Kuwonjezera pa kumuuza za zotsatira za zimene angachite, muthandizeninso kuganizira za makhalidwe amene angafune kudziwika nawo. Achinyamata akakumana ndi mavuto angathe kusankha zinthu mwanzeru ngati atadzifunsa mafunso otsatirawa:

  • Kodi ndimafuna kudziwika kuti ndine munthu wotani?—Akolose 3:10.

  • Kodi munthu amene ali ndi makhalidwe amene ndimawafunawo angatani atakumana ndi mavuto amenewa?​—Miyambo 10:1.

M’Baibulo muli zitsanzo zambiri za anthu amene ankadziwika kuti ndi anthu abwino kapena oipa mogwirizana ndi zimene ankachita. (1 Akorinto 10:11; Yakobo 5:10, 11) Mukhoza kugwiritsa ntchito zitsanzo zimenezi kuthandiza mwana wanu kuti akhale ndi makhalidwe abwino.

Mabuku amene a Mboni za Yehova amafalitsa angakuthandizeni kudziwa mmene mungathandizire banja komanso ana anu kugwiritsa ntchito mfundo za m’Baibulo.